< אסתר 4 >

ומרדכי ידע את כל אשר נעשה ויקרע מרדכי את בגדיו וילבש שק ואפר ויצא בתוך העיר ויזעק זעקה גדולה ומרה 1
Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima.
ויבוא עד לפני שער המלך כי אין לבוא אל שער המלך בלבוש שק 2
Ndipo anapita ndi kuyima pa chipata cha mfumu, chifukwa panalibe wina aliyense amaloledwa kulowa pa chipata cha mfumu atavala chiguduli.
ובכל מדינה ומדינה מקום אשר דבר המלך ודתו מגיע--אבל גדול ליהודים וצום ובכי ומספד שק ואפר יצע לרבים 3
Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa.
ותבואינה (ותבואנה) נערות אסתר וסריסיה ויגידו לה ותתחלחל המלכה מאד ותשלח בגדים להלביש את מרדכי ולהסיר שקו מעליו--ולא קבל 4
Anamwali otumikira mfumukazi Estere ndi adindo ake ofulidwa atabwera ndi kumuwuza za Mordekai, anavutika kwambiri. Estere anamutumizira zovala kuti avale ndi kuti avule chiguduli chake koma Mordekai sanalole zimenezo.
ותקרא אסתר להתך מסריסי המלך אשר העמיד לפניה ותצוהו על מרדכי--לדעת מה זה ועל מה זה 5
Kenaka Estere anayitana Hataki, mmodzi wa adindo a mfumu ofulidwa amene anayikidwa kuti azimutumikira kuti apite kwa Mordekai kuti akamve chimene chimamuvuta komanso chifukwa chochitira zimenezi.
ויצא התך אל מרדכי--אל רחוב העיר אשר לפני שער המלך 6
Choncho Hataki anapita kwa Mordekai ku bwalo la mzinda patsogolo pa chipata cha mfumu.
ויגד לו מרדכי את כל אשר קרהו ואת פרשת הכסף אשר אמר המן לשקול על גנזי המלך ביהודיים (ביהודים)--לאבדם 7
Mordekai anamuwuza zonse zimene zinamuchitikira kuphatikizapo mtengo weniweni wa ndalama zimene Hamani analonjeza kupereka mosungira chuma cha mfumu za anthu amene adzawononge a Yuda.
ואת פתשגן כתב הדת אשר נתן בשושן להשמידם נתן לו--להראות את אסתר ולהגיד לה ולצוות עליה לבוא אל המלך להתחנן לו ולבקש מלפניו--על עמה 8
Mordekai anamupatsanso imodzi mwa makalata a ulamuliro wonena za chiwembuchi amene anawasindikiza ku Susa kukamuonetsa ndi kumufotokozera zonse Estere. Anamuwuzanso kuti akamudandaulire kuti akapite kwa mfumu kukapempha chifundo ndi kuyidandaulira chifukwa cha anthu a mtundu wake.
ויבוא התך ויגד לאסתר את דברי מרדכי 9
Hataki anabwerera ndi kumufotokozera Estere zimene Mordekai ananena.
ותאמר אסתר להתך ותצוהו אל מרדכי 10
Ndipo Estere anamutuma Hataki kuti akanene kwa Mordekai kuti,
כל עבדי המלך ועם מדינות המלך ידעים אשר כל איש ואשה אשר יבוא אל המלך אל החצר הפנימית אשר לא יקרא אחת דתו להמית לבד מאשר יושיט לו המלך את שרביט הזהב וחיה ואני לא נקראתי לבוא אל המלך--זה שלושים יום 11
“Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.”
ויגידו למרדכי את דברי אסתר 12
Tsono Mordekai anawuzidwa mawu a Estere.
ויאמר מרדכי להשיב אל אסתר אל תדמי בנפשך להמלט בית המלך מכל היהודים 13
Kenaka Mordekai anawawuza kuti akamuyankhe Estere motere: “Usaganize kuti iwe wekha mwa Ayuda onse udzapulumuka chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu.
כי אם החרש תחרישי בעת הזאת--רוח והצלה יעמוד ליהודים ממקום אחר ואת ובית אביך תאבדו ומי יודע--אם לעת כזאת הגעת למלכות 14
Pakuti ngati ukhalatu chete nthawi ino, chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina nʼkutheka kuti iwe ndi a pa banja la makolo ako mudzafa. Ndipo adziwa ndani mwina unalowa ufumu chifukwa cha nthawi ngati imeneyi?”
ותאמר אסתר להשיב אל מרדכי 15
Pamenepo Estere anatumiza yankho ili kwa Mordekai:
לך כנוס את כל היהודים הנמצאים בשושן וצומו עלי ואל תאכלו ואל תשתו שלשת ימים לילה ויום--גם אני ונערתי אצום כן ובכן אבוא אל המלך אשר לא כדת וכאשר אבדתי אבדתי 16
“Pitani, mukasonkhanitse pamodzi Ayuda onse amene ali mu Susa ndipo mundisalire chakudya. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu, usiku ndi usana. Ine ndi anamwali anga onditumikira tidzasala chakudya monga inu. Izi zikachitika, ine ndidzapita kwa mfumu, ngakhale kutero ndikutsutsana ndi lamulo. Ndipo ngati nʼkufa ndife ndithu.”
ויעבר מרדכי ויעש ככל אשר צותה עליו אסתר 17
Choncho Mordekai anapita ndi kuchita monga Estere anamupemphera.

< אסתר 4 >