< דברי הימים ב 13 >

בשנת שמונה עשרה למלך ירבעם וימלך אביה על יהודה 1
Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda,
שלוש שנים מלך בירושלם ושם אמו מיכיהו בת אוריאל מן גבעה ומלחמה היתה בין אביה ובין ירבעם 2
ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka zitatu. Dzina la amayi ake linali Maaka mwana wa Urieli wa ku Gibeya. Koma panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu.
ויאסר אביה את המלחמה בחיל גבורי מלחמה ארבע מאות אלף איש בחור וירבעם ערך עמו מלחמה בשמונה מאות אלף איש בחור גבור חיל 3
Abiya anapita ku nkhondo ndi asilikali odziwa bwino nkhondo 400,000, ndipo Yeroboamu anandandalitsa ankhondo, asilikali 800,000 odziwa bwino nkhondo, osankhidwa ndi amphamvu, woti amenyane naye.
ויקם אביה מעל להר צמרים אשר בהר אפרים ויאמר שמעוני ירבעם וכל ישראל 4
Abiya anayima pa phiri la Zemaraimu, mʼdziko lamapiri la Efereimu, ndipo anati, “Yeroboamu ndi Aisraeli onse, tandimverani!
הלא לכם לדעת כי יהוה אלהי ישראל נתן ממלכה לדויד על ישראל לעולם לו ולבניו ברית מלח 5
Kodi inu simukudziwa kuti Yehova, Mulungu wa Israeli, wapereka ufumu wa Israeli kwa Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya ndiponso pangano la mchere?
ויקם ירבעם בן נבט עבד שלמה בן דויד וימרד על אדניו 6
Komabe Yeroboamu mwana wa Nebati, mtumiki wa Solomoni mwana wa Davide, anawukira mbuye wake.
ויקבצו עליו אנשים רקים בני בליעל ויתאמצו על רחבעם בן שלמה ורחבעם היה נער ורך לבב ולא התחזק לפניהם 7
Ndipo anthu ena achabechabe anasonkhana kwa iye ndipo anatsutsana ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni pamene anali wamngʼono ndi wosalimba mtima ndi wopanda mphamvu kuti athe kulimbana nawo.
ועתה אתם אמרים להתחזק לפני ממלכת יהוה ביד בני דויד ואתם המון רב ועמכם עגלי זהב אשר עשה לכם ירבעם לאלהים 8
“Ndipo tsopano inu mwakonzekera kutsutsana ndi ufumu wa Yehova, umene uli mʼmanja mwa zidzukulu za Davide. Inu ndithu mulipo ankhondo ambirimbiri ndipo muli ndi ana angʼombe agolide amene Yeroboamu anapanga kuti akhale milungu yanu.
הלא הדחתם את כהני יהוה את בני אהרן והלוים ותעשו לכם כהנים כעמי הארצות--כל הבא למלא ידו בפר בן בקר ואילם שבעה והיה כהן ללא אלהים 9
Koma kodi inu simunathamangitse ansembe a Yehova, ana a Aaroni ndiponso Alevi ndi kudzisankhira ansembe anuanu monga anthu ena amachitira? Aliyense amene amabwera kuti adzipatule atatenga mwana wangʼombe wamwamuna ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri amakhala wansembe wa zinthu zimene sizili milungu.
ואנחנו יהוה אלהינו ולא עזבנהו וכהנים משרתים ליהוה בני אהרן והלוים במלאכת 10
“Koma kunena za ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, ndipo sitinamusiye. Ansembe amene amatumikira Yehova ndi ana a Aaroni ndipo amathandizidwa ndi Alevi.
ומקטרים ליהוה עלות בבקר בבקר ובערב בערב וקטרת סמים ומערכת לחם על השלחן הטהור ומנורת הזהב ונרתיה לבער בערב בערב--כי שמרים אנחנו את משמרת יהוה אלהינו ואתם עזבתם אתו 11
Mmawa uliwonse ndi madzulo aliwonse amapereka nsembe zopsereza ndi kufukiza lubani kwa Yehova. Iwo amayika buledi pa tebulo loyeretsedwa monga mwa mwambo ndipo amayatsa nyale pa zoyikapo nyale zagolide madzulo aliwonse. Ife timachita zofuna za Yehova Mulungu wathu. Koma inu mwamusiya.
והנה עמנו בראש האלהים וכהניו וחצצרות התרועה--להריע עליכם בני ישראל אל תלחמו עם יהוה אלהי אבתיכם--כי לא תצליחו 12
Mulungu ali nafe pakuti ndiye mtsogoleri wathu. Ansembe ake atanyamula malipenga, adzayimba mfuwu wankhondo kulimbana nanu. Inu Aisraeli musalimbane ndi Yehova, Mulungu wa makolo anu, pakuti simungathe kupambana.”
וירבעם הסב את המארב לבוא מאחריהם ויהיו לפני יהודה והמארב מאחריהם 13
Tsono Yeroboamu anali atatumiza asilikali kumbuyo mowazungulira, kotero kuti iye ali kutsogolo kwa anthu a ku Yuda, anthu owabisalira anali kumbuyo kwawo.
ויפנו יהודה והנה להם המלחמה פנים ואחור ויצעקו ליהוה והכהנים מחצצרים (מחצרים) בחצצרות 14
Asilikali a Yuda anatembenuka ndipo anaona kuti nkhondo imachitikira kutsogolo ndi kumbuyo. Ndipo iwo anafuwulira Yehova. Ansembe anayimba malipenga awo
ויריעו איש יהודה ויהי בהריע איש יהודה והאלהים נגף את ירבעם וכל ישראל לפני אביה ויהודה 15
ndipo asilikali a Yuda anafuwula mawu ankhondo. Atafuwula mawu ankhondowo, Mulungu anagonjetsa Yeroboamu pamodzi ndi Aisraeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.
וינוסו בני ישראל מפני יהודה ויתנם אלהים בידם 16
Aisraeli anathawa Ayuda. Ndipo Mulungu anawapereka mʼmanja mwawo.
ויכו בהם אביה ועמו מכה רבה ויפלו חללים מישראל חמש מאות אלף איש בחור 17
Abiya pamodzi ndi anthu ake anapha anthu ambiri, kotero kuti Aisraeli 500,000 odziwa bwino nkhondo anaphedwa.
ויכנעו בני ישראל בעת ההיא ויאמצו בני יהודה כי נשענו על יהוה אלהי אבותיהם 18
Ankhondo a Israeli anagonjetsedwa pa nthawi imeneyi, ndipo ankhondo a Yuda anapambana chifukwa anadalira Yehova, Mulungu wa makolo awo.
וירדף אביה אחרי ירבעם וילכד ממנו ערים את בית אל ואת בנותיה ואת ישנה ואת בנותיה ואת עפרון (עפרין) ובנתיה 19
Abiya anathamangitsa Yeroboamu ndipo anamulanda mizinda ya Beteli, Yesana, ndi Efroni pamodzi ndi midzi yawo yozungulira.
ולא עצר כח ירבעם עוד בימי אביהו ויגפהו יהוה וימת 20
Yeroboamu sanapezenso mphamvu nthawi ya Abiya. Ndipo Yehova anamukantha nafa.
ויתחזק אביהו--וישא לו נשים ארבע עשרה ויולד עשרים ושנים בנים ושש עשרה בנות 21
Koma Abiya mphamvu zake zinakula. Iye anakwatira akazi 14 ndipo anali ndi ana aamuna 22 ndi ana aakazi 16.
ויתר דברי אביה ודרכיו ודבריו--כתובים במדרש הנביא עדו 22
Zina ndi zina zokhudza Abiya, zimene anachita ndi zimene anayankhula, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mneneri Ido.

< דברי הימים ב 13 >