< Προς Κορινθιους Β΄ 5 >

1 οιδαμεν γαρ οτι εαν η επιγειος ημων οικια του σκηνους καταλυθη οικοδομην εκ θεου εχομεν οικιαν αχειροποιητον αιωνιον εν τοις ουρανοις (aiōnios g166)
Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. (aiōnios g166)
2 και γαρ εν τουτω στεναζομεν το οικητηριον ημων το εξ ουρανου επενδυσασθαι επιποθουντες
Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo,
3 ειγε και ενδυσαμενοι ου γυμνοι ευρεθησομεθα
chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche.
4 και γαρ οι οντες εν τω σκηνει στεναζομεν βαρουμενοι εφ ω ου θελομεν εκδυσασθαι αλλ επενδυσασθαι ινα καταποθη το θνητον υπο της ζωης
Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo.
5 ο δε κατεργασαμενος ημας εις αυτο τουτο θεος ο και δους ημιν τον αρραβωνα του πνευματος
Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.
6 θαρρουντες ουν παντοτε και ειδοτες οτι ενδημουντες εν τω σωματι εκδημουμεν απο του κυριου
Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye.
7 δια πιστεως γαρ περιπατουμεν ου δια ειδους
Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso.
8 θαρρουμεν δε και ευδοκουμεν μαλλον εκδημησαι εκ του σωματος και ενδημησαι προς τον κυριον
Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye.
9 διο και φιλοτιμουμεθα ειτε ενδημουντες ειτε εκδημουντες ευαρεστοι αυτω ειναι
Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo.
10 τους γαρ παντας ημας φανερωθηναι δει εμπροσθεν του βηματος του χριστου ινα κομισηται εκαστος τα δια του σωματος προς α επραξεν ειτε αγαθον ειτε κακον
Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.
11 ειδοτες ουν τον φοβον του κυριου ανθρωπους πειθομεν θεω δε πεφανερωμεθα ελπιζω δε και εν ταις συνειδησεσιν υμων πεφανερωσθαι
Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu.
12 ου γαρ παλιν εαυτους συνιστανομεν υμιν αλλα αφορμην διδοντες υμιν καυχηματος υπερ ημων ινα εχητε προς τους εν προσωπω καυχωμενους και ου καρδια
Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima.
13 ειτε γαρ εξεστημεν θεω ειτε σωφρονουμεν υμιν
Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike.
14 η γαρ αγαπη του χριστου συνεχει ημας κριναντας τουτο οτι [ει] εις υπερ παντων απεθανεν αρα οι παντες απεθανον
Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso.
15 και υπερ παντων απεθανεν ινα οι ζωντες μηκετι εαυτοις ζωσιν αλλα τω υπερ αυτων αποθανοντι και εγερθεντι
Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.
16 ωστε ημεις απο του νυν ουδενα οιδαμεν κατα σαρκα ει δε και εγνωκαμεν κατα σαρκα χριστον αλλα νυν ουκετι γινωσκομεν
Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso.
17 ωστε ει τις εν χριστω καινη κτισις τα αρχαια παρηλθεν ιδου γεγονεν καινα τα παντα
Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano.
18 τα δε παντα εκ του θεου του καταλλαξαντος ημας εαυτω δια ιησου χριστου και δοντος ημιν την διακονιαν της καταλλαγης
Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso.
19 ως οτι θεος ην εν χριστω κοσμον καταλλασσων εαυτω μη λογιζομενος αυτοις τα παραπτωματα αυτων και θεμενος εν ημιν τον λογον της καταλλαγης
Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso.
20 υπερ χριστου ουν πρεσβευομεν ως του θεου παρακαλουντος δι ημων δεομεθα υπερ χριστου καταλλαγητε τω θεω
Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu.
21 τον γαρ μη γνοντα αμαρτιαν υπερ ημων αμαρτιαν εποιησεν ινα ημεις γενωμεθα δικαιοσυνη θεου εν αυτω
Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

< Προς Κορινθιους Β΄ 5 >