< 5 Mose 9 >

1 Höre, Israel! Du ziehst jetzt über den Jordan, um Herr zu werden über Völker, die größer und mächtiger sind, als du, über Städte, die groß und himmelhoch befestigt sind,
Mvera Israeli. Watsala pangʼono kuwoloka Yorodani ndi kukathamangitsa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iweyo, imene mizinda yake ndi ikuluikulu yokhala ndi makoma ofika mpaka kumwamba.
2 über ein großes und hochgewachsenes Volk, die Enakiter, die du ja selber kennst und von denen du selbst hast sagen hören: Wer vermag den Enakitern standzuhalten?
Anthuwo ndi ataliatali, Aanaki! Ukudziwa za iwo ndipo unamvapo zikunenedwa kuti, “Ndani amene angalimbane ndi Aanaki?”
3 So wisse denn jetzt, daß es Jahwe, dein Gott, ist, der als verzehrendes Feuer dir voranzieht; er wird sie vertilgen und er wird sie vor dir niederwerfen, so daß du sie rasch aus ihrem Besitze vertreiben und vernichten kannst, wie dir Jahwe verheißen hat.
Koma khulupirira lero kuti Yehova Mulungu wako amene ali patsogolo pako ali ngati moto wonyeketsa. Adzawononga iwowo ndipo adzawagonjetsa iweyo ukuona. Pamenepo udzawathamangitsa ndi kuwakantha mwamsanga, monga momwe Yehova wakulonjezera.
4 Denke nicht etwa, wenn Jahwe, dein Gott, sie vor dir herjagt: Um meiner Rechtbeschaffenheit willen hat mich Jahwe in den Besitz dieses Landes gelangen lassen! - während Jahwe diese Völker vielmehr um ihrer Frevel willen vor dir vertreibt.
Yehova Mulungu wako akadzawapirikitsa pamaso pako, usadzanene mu mtima mwako kuti, “Yehova wandibweretsa kuno kudzalanda dziko lino chifukwa cha kulungama kwanga.” Ayi, koma ndi chifukwa cha kuyipa kwa anthu amene Yehova ati awapirikitse pamaso pako.
5 Nicht um deiner Rechtbeschaffenheit und um deines lauteren Herzens willen gelangst du in den Besitz ihres Landes, sondern Jahwe, dein Gott, vertreibt diese Völker vor dir um ihrer Frevel willen und um die eidliche Zusage zu erfüllen, die Jahwe deinen Vätern Abraham, Isaak und Jakob gegeben hat.
Sukalowa ndi kutenga dziko lawolo chifukwa cha kulungama kwako kapena kukhulupirika kwako koma chifukwa cha kuyipa kwa anthuwo. Yehova Mulungu wako awapirikitsa pamaso pako kuti akwaniritse zimene analumbira kwa makolo ako Abrahamu, Isake ndi Yakobo.
6 So erkenne nun, daß dir Jahwe, dein Gott, dieses schöne Land nicht um deiner Rechtbeschaffenheit willen zum Besitze verleiht, denn du bist ein halsstarriges Volk.
Tsono zindikira kuti si chifukwa cha kulungama kwako kuti Yehova Mulungu wako akukupatsa dziko labwinoli kuti ulitenge popeza ndiwe wokanika.
7 Denke daran und vergiß es nicht, wie du Jahwe, deinen Gott, in der Steppe erzürntest! Von dem Tage an, wo du aus Ägypten wegzogst, bis zu eurer Ankunft an diesem Orte zeigtet ihr euch widerspenstig gegen Jahwe.
Kumbukirani izi ndipo musayiwale mmene munaputira mkwiyo wa Yehova Mulungu mʼchipululu muja. Kuyambira tsiku limene munatuluka mu Igupto mpaka pamene munafika kuno, mwakhala owukira Yehova.
8 Am Horeb erzürntet ihr Jahwe, und Jahwe wurde über euch so aufgebracht, daß er euch vertilgen wollte.
Ku Horebu munaputa mkwiyo wa Yehova, kotero kuti anakwiya kwambiri nafuna kukuwonongani.
9 Ich war auf den Berg gestiegen, um die steinernen Tafeln, die Tafeln des Bundes, den Jahwe mit euch geschlossen hatte, in Empfang zu nehmen, und verweilte vierzig Tage und vierzig Nächte auf dem Berg, ohne Brot zu essen und Wasser zu trinken.
Nditakwera ku phiri kuti ndikalandire miyala iwiri ya malamulo, ya pangano limene Yehova anachita ndi inu, ndinakhala ku phiriko kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana, sindinadye buledi kapena kumwa madzi.
10 Jahwe übergab mir die beiden steinernen Tafeln, die vom Finger Gottes beschrieben waren und alle die Worte enthielten, die Jahwe am Versammlungstag auf dem Berg aus dem Feuer mit euch geredet hatte.
Yehova anandipatsa miyala iwiri yolembedwa ndi chala chake. Pa miyalapo panali malamulo onse amene Yehova analengeza kwa inu pa phiri kuchokera mʼmoto pa tsiku la msonkhano.
11 Nach Verlauf von vierzig Tagen und vierzig Nächten übergab mir Jahwe die beiden steinernen Tafeln, die Tafeln mit dem Gesetz.
Pakutha pa masiku makumi anayi usiku ndi usana, Yehova anandipatsa miyala iwiri, miyala ya pangano.
12 Dann aber sprach Jahwe zu mir: Auf! steige eilends von hier hinab; denn dein Volk, das du aus Ägypten weggeführt hast, handelt verderbt. Gar schnell sind sie von dem Weg abgewichen, den ich ihnen vorgeschrieben habe; sie haben sich ein Gußbild verfertigt.
Tsono Yehova anandiwuza, “Tsikako kuno msanga, chifukwa anthu ako aja unawatulutsa ku Iguptowa adziyipitsa. Iwo apatukapo mofulumira pa zimene ndinawalamulira ndipo adzipangira fano lachitsulo.”
13 Und Jahwe sprach zu mir: Ich sehe nun wohl, daß dieses Volk ein halsstarriges Volk ist.
Ndipo Yehova anati kwa ine, “Anthu awa ndawaona ndipo ndi anthu okanikadi!
14 So laß mich nun, daß ich sie vertilge und ihren Namen unter dem Himmel auslösche und dich zum Stammvater eines Volkes mache, das stärker und größer ist, als dieses.
Ndilekeni ndiwawononge ndi kufafaniza mayina awo pa dziko lapansi. Ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu wa anthu wamphamvu ndi wochuluka kuposa iwo.”
15 Da machte ich mich auf den Rückweg und stieg vom Berge, der in hellem Feuer stand, hinab, mit den beiden Gesetztafeln in meinen beiden Händen.
Choncho ndinatembenuka ndi kutsika phiri moto ukanayakabe. Ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga.
16 Da sah ich denn wahrhaftig: Ihr hattet euch gegen Jahwe, euren Gott, versündigt, hattet euch ein gegossenes Kalb verfertigt und wart so gar schnell von dem Weg abgewichen, den Jahwe euch vorgeschrieben hatte.
Ine poyangʼana ndinaona kuti inu munachimwira Yehova Mulungu wanu. Munadzipangira fano lowumbidwa ngati mwana wangʼombe. Inuyo munapatuka msanga kuchoka pa njira imene Yehova anakulamulirani.
17 Da faßte ich die beiden Tafeln, schleuderte sie weg aus meinen beiden Händen und zerschmetterte sie vor euren Augen.
Motero ine ndinaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwanga, ndi kuyiphwanya inu mukuona.
18 Dann aber warf ich mich, wie das erste Mal, vierzig Tage und vierzig Nächte, ohne Brot zu essen und Wasser zu trinken, vor Jahwe nieder um aller eurer Sünde willen, die ihr begangen hattet, indem ihr thatet, was Jahwe mißfiel, so daß es ihn erzürnen mußte.
Tsono nthawi yomweyo ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usiku ndi usana. Sindinadye buledi kapena kumwa madzi chifukwa cha machimo onse amene munawachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kumukwiyitsa kwambiri.
19 Denn mir war bange vor dem Zorn und Grimm, den Jahwe gegen euch hegte, daß er euch vertilgen wollte. Und Jahwe erhörte mich auch diesmal.
Ine ndinachita mantha ndi mkwiyo ndi ukali wa Yehova chifukwa anakwiya nanu kokwanira kukuwonongani. Koma Yehova anandimveranso.
20 Auch über Aaron war Jahwe so sehr erzürnt, daß er ihn vertilgen wollte, und ich flehte damals auch für Aaron.
Ndipo Yehova anakwiya ndi Aaroni ndipo akanamuwononga, koma ine ndinamupemphereranso Aaroniyo.
21 Das Denkmal eurer Sünde aber, das ihr verfertigt hattet, das Kalb, nahm ich, verbrannte es und zerstieß und zermalmte es vollständig, bis es zu feinem Staube wurde; diesen Staub warf ich in den Bach, der vom Berge herabfließt.
Ndiponso ndinatenga chinthu chanu choyipacho, mwana wangʼombe amene munapangayo, ndi kumuwotcha pa moto. Kenaka ndinamuphwanya ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi ndipo ndinawaza fumbilo mu mtsinje umene unkayenda kuchokera mʼphiri.
22 Ferner erzürntet ihr Jahwe zu Tabera, zu Massa und bei den Lustgräbern.
Inu munamukwiyitsanso Yehova ku Tabera, ku Masa ndi ku Kibiroti Hatava.
23 Auch als euch Jahwe von Kades-Barnea entsandte, indem er gebot: Zieht hinauf und nehmt das Land ein, das ich euch verliehen habe, zeigtet ihr euch widerspenstig gegen den Befehl Jahwes, eures Gottes, und wolltet ihm nicht vertrauen, noch auf seine Stimme hören.
Ndipo Yehova atakutulutsani ku Kadesi Barinea anati, “Pitani mukatenge dziko limene ndakupatsani.” Koma munawukira ulamuliro wa Yehova Mulungu wanu. Inu simunamukhulupirire kapena kumumvera.
24 Widerspenstig habt ihr euch gegen Jahwe gezeigt, seitdem ich euch kenne.
Kuyambira pamene ndinakudziwani, mwakhala owukira Yehova.
25 Als ich nun die vierzig Tage und vierzig Nächte; die ich mich niederwarf, vor Jahwe lag, weil Jahwe gedroht hatte, euch vertilgen zu wollen,
Ine ndinagwa chafufumimba pamaso pa Yehova kwa masiku makumi anayi usana ndi usiku chifukwa Yehova ananena kuti akuwonongani.
26 da betete ich zu Jahwe und sprach: O Herr, Jahwe! Verdirb dein Volk und dein Eigentum nicht, das du durch deine große Macht erlöst, das du mit starker Hand auf Ägypten weggeführt hast!
Ndinapemphera kwa Ambuye ndi kuti, “Haa Yehova Wamkulukulu, musawawononge anthu anu, chuma chanuchanu chimene munachipulumutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ku Igupto ndi dzanja lanu la mphamvu.
27 Denke an deine Knechte, an Abraham, Isaak und Jakob! Kehre dich nicht an die Halsstarrigkeit deines Volks, an seine Bosheit und seine Sünde,
Kumbukirani atumiki anu Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Musatengere kupulupudza, kuyipa ndi kuchimwa kwawo anthuwa.
28 damit man in dem Land, aus dem du uns weggeführt hast, nicht sagen könne: Weil Jahwe nicht imstande war, sie in das Land zu bringen, das er ihnen verheißen hatte, und weil er sie haßte, hat er sie weggeführt, um sie in der Steppe umkommen zu lassen!
Kupanda kutero, ndiye kuti anthu a ku dziko lija munatitulutsaku adzati, ‘Yehova anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu popeza sanathe kukawalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza ndipo anadana nawo.’
29 Sie sind ja dein Volk und dein Eigentum, das du mit deiner großen Kraft und deinem ausgereckten Arm hinweggeführt hast.
Koma iwowa ndi anthu anu, chuma chanu chimene munachitulutsa ndi mphamvu yanu yayikulu ndi mkono wanu wotambasuka.”

< 5 Mose 9 >