< 2 Chroniques 10 >

1 Et Roboam se rendit à Sichem, parce que tout Israël y était venu pour le proclamer roi.
Rehobowamu anapita ku Sekemu, pakuti Aisraeli onse anapita kumeneko kuti akamulonge ufumu.
2 Or, dès que Jéroboam, fils de Nabat, apprit ces nouvelles en Égypte, où il avait fui loin de Salomon, il en revint.
Yeroboamu mwana wa Nebati atamva zimenezi (Iye anali ku Igupto, kumene anapita pothawa mfumu Solomoni) anabwerako kuchokera ku Igupto.
3 Et le peuple l'envoya chercher, et il alla devant Roboam avec toute la synagogue, disant:
Kotero anthu anakayitana Yeroboamu ndipo iye ndi Aisraeli onse anapita kwa Rehobowamu ndi kumuwuza kuti,
4 Ton père a rendu notre joug bien dur; allège donc maintenant la servitude trop dure de ton père, que notre joug soit moins lourd, et nous te servirons.
“Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma tsopano mutipeputsire ntchito yolemetsayi ndi goli lolemerali limene analiyika pa ife ndipo ifeyo tidzakutumikirani.”
5 Et il leur dit: Allez-vous-en pendant trois jours; puis, revenez auprès de moi; et le peuple s'en alla.
Rehobowamu anayankha kuti, “Mukabwerenso pakapita masiku atatu.” Choncho anthuwo anachoka.
6 Le roi Roboam réunit les anciens qui, du vivant de Salomon, son père, se tenaient auprès de lui, disant: Que me conseillez-vous de répondre à ce peuple?
Kenaka mfumu Rehobowamu anafunsira nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira abambo ake, Solomoni, pamene anali moyo. Iye anafunsa kuti, “Kodi inu mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu awa?”
7 Il lui dirent: Si aujourd'hui tu es bienveillant pour ce peuple, si tu veux bien lui dire de bonnes paroles, ils seront tes serviteurs tous les jours.
Iwo anayankha kuti, “Ngati inu muwakomera mtima anthu awa ndi kuwasangalatsa ndiponso kuwayankha mawu abwino, iwo adzakutumikirani nthawi zonse.”
8 Mais, il dédaigna le conseil des anciens qu'il avait consultés, et il consulta les jeunes gens élevés avec lui, qui se tenaient devant lui.
Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakulu anamupatsa ndipo anakafunsira nzeru kwa anyamata amene anakula naye pamodzi komanso amamutumikira.
9 Et il leur dit: Comment me conseillez-vous de répondre à ce peuple qui me dit: Allège le joug que nous a mis ton père?
Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ndi otani? Kodi tiwayankhe chiyani anthu amene akunena kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anayika pa ife?’”
10 Or, les jeunes gens, élevés avec lui, dirent: Voici comment tu parleras à ce peuple qui t'a dit: Ton père a rendu pesant notre joug, allège-le pour nous, réponds-leur: Mon petit doigt est plus gros que le corps de mon père.
Anyamata amene anakula pamodzi naye anamuyankha kuti, “Anthu amene anena kwa inu kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa koma inu mupeputse goli lathu,’ muwawuze kuti, ‘Chala changa chachingʼono ndi chachikulu kuposa chiwuno cha abambo anga.
11 Mon père vous a châtiés avec un joug pesant, je le rendrai pour vous plus pesant encore; il vous a châtiés à coups de fouet, mais je vous châtierai avec des scorpions.
Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’”
12 Et Jéroboam revint le troisième jour, avec tout le peuple, auprès de Roboam comme il le leur avait prescrit, disant: Revenez dans trois jours.
Tsiku lachitatu Yeroboamu ndi anthu onse anabwerera kwa Rehobowamu monga ananenera mfumu kuti, “Mukabwerenso kwa ine pakapita masiku atatu.”
13 Et le roi leur répondit durement, car il avait dédaigné le conseil des anciens.
Mfumu inawayankha mwankhanza, pokana malangizo a akuluakulu aja.
14 Et il leur parla selon le conseil des jeunes gens, et il leur dit: Mon père vous a chargés d'un joug pesant, je le rendrai pour vous plus pesant encore; il vous a châtiés à coups de fouet, moi je vous châtierai avec des scorpions.
Iye anatsatira malangizo a anyamata ndipo anati, “Abambo anga anakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzalichititsa kukhala lolemetsa kwambiri. Abambo anga anakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.”
15 Et le roi n'avait point écouté les fils d'Israël, parce que Dieu s'était tourné contre lui, disant: «Le Seigneur a relevé la parole qu'il a dite, par Achias le Sélonite, concernant Jéroboam, fils de Nabat,
Kotero mfumu sinamvere anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Mulungu, kukwaniritsa mawu amene Yehova ananena kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
16 Et tout Israël.» C'est pourquoi le roi ne l'avait pas écouté, et le peuple s'écria: Qu'y a-t-il entre nous et David? Notre héritage dépend-il du fils de Jessé? A tes tentes, ô Israël, et toi, David, veille sur ta maison. Et Israël s'en alla chacun en sa demeure.
Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kuwamvera, iwo anayankha mfumu kuti, “Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide, gawo lanji mwa mwana wa Yese? Inu Aisraeli! Pitani kwanu. Iwe Davide! Yangʼana banja lako.” Kotero Aisraeli onse anapita kwawo.
17 Et les hommes d'Israël qui habitaient Juda rentrèrent en leurs villes, et Jéroboam régna sur eux.
Koma Rehobowamu anakhala akulamulirabe Aisraeli amene amakhala mʼmizinda ya Yuda.
18 Et le roi envoya aux autres fils d'Israël, Adoniram, intendant des impôts; ils le lapidèrent, il mourut; et le roi Roboam s'empressa de monter sur son char pour fuir, et se renfermer dans Jérusalem.
Mfumu Rehobowamu inatuma Hadoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli anamugenda miyala ndi kumupha. Koma mfumu Rehobowamu anakwera galeta lake ndi kuthawira ku Yerusalemu.
19 Et jusqu'à nos jours la maison de David a été rejetée par Israël.
Motero Israeli wakhala akuwukira banja la Davide mpaka lero lino.

< 2 Chroniques 10 >