< Psalms 41 >

1 To the Overseer. — A Psalm of David. O the happiness of him Who is acting wisely unto the poor, In a day of evil doth Jehovah deliver him.
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka; Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.
2 Jehovah doth preserve him and revive him, He is happy in the land, And Thou givest him not into the will of his enemies.
Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake; Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.
3 Jehovah supporteth on a couch of sickness, All his bed Thou hast turned in his weakness.
Yehova adzamuthandiza pamene akudwala ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.
4 I — I said, 'O Jehovah, favour me, Heal my soul, for I did sin against Thee,'
Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo; chiritseni pakuti ndakuchimwirani.”
5 Mine enemies say evil of me: When he dieth — his name hath perished!
Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti, “Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?”
6 And if he came to see — vanity he speaketh, His heart gathereth iniquity to itself, He goeth out — at the street he speaketh.
Pamene wina abwera kudzandiona, amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe; kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja.
7 All hating me whisper together against me, Against me they devise evil to me:
Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane, iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti,
8 A thing of Belial is poured out on him, And because he lay down he riseth not again.
“Matenda owopsa amugwira; sadzaukapo pamalo pamene wagona.”
9 Even mine ally, in whom I trusted, One eating my bread, made great the heel against me,
Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira, iye amene amadya pamodzi ndi ine watukula chidendene chake kulimbana nane.
10 And Thou, Jehovah, favour me, And cause me to rise, And I give recompence to them.
Koma Yehova mundichititre chifundo, dzutseni kuti ndiwabwezere.
11 By this I have known, That Thou hast delighted in me, Because my enemy shouteth not over me.
Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane, pakuti mdani wanga sandigonjetsa.
12 As to me, in mine integrity, Thou hast taken hold upon me, And causest me to stand before Thee to the age.
Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.
13 Blessed [is] Jehovah, God of Israel, From the age — and unto the age. Amen and Amen.
Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. Ameni ndi Ameni.

< Psalms 41 >