< Luke 8 >

1 And it was don aftirward, and Jhesus made iourney bi citees and castels, prechynge and euangelisynge the rewme of God, and twelue with hym;
Zitatha izi, Yesu anayendayenda kuchoka mzinda wina kupita wina ndiponso mudzi wina kupita wina, akulalikira Uthenga Wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ophunzira ake khumi ndi awiri aja anali naye,
2 and sum wymmen that weren heelid of wickid spiritis and sijknessis, Marie, that is clepid Maudeleyn, of whom seuene deuelis wenten out,
komanso akazi ena amene anachiritsidwa ku mizimu yoyipa ndi matenda: Mariya, wotchedwa Magadalena, amene mwa iye munatuluka ziwanda zisanu ndi ziwiri;
3 and Joone, the wijf of Chuse, the procuratoure of Eroude, and Susanne, and many othir, that mynystriden to hym of her ritchesse.
Yohana mkazi wa Kuza, woyangʼanira mʼnyumba ya Herode; Suzana; ndi ena ambiri analinso. Akazi awa ankawathandiza ndi chuma chawo.
4 And whanne myche puple was come togidir, and men hiyeden to hym fro the citees, he seide bi a symylitude,
Anthu ambiri ankasonkhana, ndipo pamene anthu ankabwera kwa Yesu kuchokera ku midzi, Iye anawawuza fanizo ili,
5 He that sowith, yede out to sowe his seed. And while he sowith, sum fel bisidis the weie, and was defoulid, and briddis of the eir eten it.
“Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa mbewuzo, zina zinagwa mʼmbali mwa njira; zinapondedwa, ndipo mbalame zamlengalenga zinadya.
6 And othir fel on a stoon, and it sprunge vp, and driede, for it hadde not moysture.
Zina zinagwa pa thanthwe, ndipo pamene zinamera, zinafota chifukwa panalibe chinyezi.
7 And othir fel among thornes, and the thornes sprongen vp togider, and strangliden it.
Mbewu zina zinagwera pakati pa minga, zinakulira pamodzi ndi mingazo ndipo zinalepheretsa mmerawo kukula.
8 And othir fel in to good erthe, and it sprungun made an hundrid foold fruyt. He seide these thingis, and criede, He that hath eeris of heryng, here he.
Mbewu zina zinagwera pa nthaka yabwino. Zinamera ndipo zinabala mowirikiza 100 kuposa zimene zinafesedwa zija.” Atanena izi, anafuwula kuti, “Amene ali ndi makutu, amve.”
9 But hise disciplis axiden him, what this parable was.
Ophunzira ake anamufunsa tanthauzo lake la fanizolo.
10 And he seide to hem, To you it is grauntid to knowe the pryuete of the kyngdom of God; but to othir men in parablis, that thei seynge se not, and thei herynge vndurstonde not.
Iye anati, “Kudziwa zinsinsi za ufumu wa Mulungu kwapatsidwa kwa inu, koma kwa ena ndimawayankhula mʼmafanizo kuti, “ngakhale akuona, asapenye; ngakhale akumva, asazindikire.”
11 And this is the parable.
“Tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu.
12 The seed is Goddis word; and thei that ben bisidis the weie, ben these that heren; and aftirward the feend cometh, and takith awei the word fro her herte, lest thei bileuynge be maad saaf.
Mbewu za mʼmbali mwa njira ndi anthu amene amamva mawu, ndipo kenaka mdierekezi amabwera ndi kuchotsa mawuwo mʼmitima mwawo kuti asakhulupirire ndi kupulumutsidwa.
13 But thei that fel on a stoon, ben these that whanne thei han herd, resseyuen the word with ioye. And these han not rootis; for at a tyme thei bileuen, and in tyme of temptacioun thei goen awei.
Mbewu za pa thanthwe ndi anthu amene amalandira mawu mwachimwemwe pamene akumva, koma mawuwo sazika mizu. Iwo amakhulupirira kwa kanthawi, koma pa nthawi ya mayesero, amagwa.
14 But that that fel among thornes, ben these that herden, and of bisynessis, and ritchessis, and lustis of lijf thei gon forth, and ben stranglid, and bryngen forth no fruyt.
Mbewu zimene zinagwa pakati pa minga zikuyimira anthu amene amamva mawu, koma akamayenda mʼnjira zawo amatsamwitsidwa ndi zodandaulitsa za moyo uno, chuma ndi zosangalatsa, ndipo iwo samakhwima.
15 But that that fel in to good erthe, ben these that, in a good herte, and best heren the word, and holdun, and brengen forth fruyt in pacience.
Koma mbewu za pa nthaka yabwino zikuyimira anthu amene ali ndi mtima woona ndi wabwino, amene amamva mawu nawasunga, ndipo amalimbikira mpaka amabala zipatso.
16 No man lityneth a lanterne, and hilith it with a vessel, or puttith it vndur a bed, but on a candilstike, that men that entren seen liyt.
“Palibe amayatsa nyale ndi kuyibisa mu mtsuko kapena kuyika pansi pa bedi. Koma mʼmalo mwake, amayika pa choyikapo chake, kuti anthu olowamo aone kuwala.
17 For ther is no priuei thing, which schal not be openyd, nether hid thing, which schal not be knowun, and come in to open.
Pakuti palibe kanthu kobisika kamene sikadzawululika, ndipo palibe kanthu kophimbika kamene sikadzadziwika kapena kuonetsedwa poyera.
18 Therfor se ye, hou ye heren; for it schal be youun to hym that hath, and who euer hath not, also that that he weneth that he haue, schal be takun awei fro hym.
Choncho ganizirani mozama. Iye amene ali nazo adzapatsidwa zambiri, iye amene alibe, ngakhale chimene akuganiza kuti ali nacho adzalandidwa.”
19 And his modir and britheren camen to hym; and thei myyten not come to hym for the puple.
Tsopano amayi ndi abale a Yesu anabwera kudzamuona Iye, koma analephera kuti afike pafupi ndi Iye chifukwa cha gulu la anthu.
20 And it was teeld to hym, Thi modir and thi britheren stonden with outforth, willynge to se thee.
Wina anamuwuza Iye kuti, “Amayi ndi abale anu ayima kunja, akufuna kukuonani.”
21 And he answeride, and seide to hem, My modir and my britheren ben these, that heren the word of God, and doon it.
Yesu anayankha kuti, “Amayi ndi abale anga ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kumachita zimene mawuwo akunena.”
22 And it was don in oon of daies, he wente vp in to a boot, and hise disciplis. And he seide to hem, Passe we ouer the see. And thei wenten vp.
Tsiku lina Yesu anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina la nyanja.” Ndipo analowa mʼbwato nanyamuka.
23 And while thei rowiden, he slepte. And a tempest of wynde cam doun in to the watir, and thei weren dryuun hidur and thidur with wawis, and weren in perel.
Akuwoloka, Iye anagona tulo. Namondwe wamkulu anayamba pa nyanja, ndipo bwatolo linayamba kudzaza ndi madzi ndipo anali pa chiopsezo chachikulu.
24 And thei camen nyy, and reisiden hym, and seiden, Comaundoure, we perischen. And he roos, and blamyde the wynde, and the tempest of the watir; and it ceesside, and pesibilte was maad.
Ophunzira anapita ndi kukamudzutsa Iye, nati, “Ambuye, Ambuye, ife tikumira!” Anadzuka ndipo anadzudzula mphepo ndi madzi owindukawo. Namondwe anasiya, ndipo panali bata.
25 And he seide to hem, Where is youre feith? Which dredynge wondriden, and seiden togidir, Who, gessist thou, is this? for he comaundith to wyndis and to the see, and thei obeien to hym.
Iye anafunsa ophunzira ake kuti, “Chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma pogwidwa ndi mantha ndi kudabwa anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndi ndani? Iye alamulira ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zimumvera Iye.”
26 And thei rowiden to the cuntree of Gerasenus, that is ayens Galilee.
Iwo anawolokera ku chigawo cha Gerasa chimene chili tsidya lina la nyanja kuchokera ku Galileya.
27 And whanne he wente out to the loond, a man ran to hym, that hadde a deuel long tyme, and he was not clothid with cloth, nether dwellide in hous, but in sepulcris.
Yesu ataponda pa mtunda, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi ziwanda wochokera mu mzindawo. Kwa nthawi yayitali munthuyu sanavale zovala kapena kukhala mʼnyumba, koma amakhala ku manda.
28 This, whanne he saiy Jhesu, fel doun bifor hym, and he criynge with a greet vois seide, What to me and to thee, Jhesu, the sone of the hiyest God? Y biseche thee, that thou turmente `not me.
Iye ataona Yesu, anakuwa nagwa pa mapazi ake akufuwula kwambiri kuti, “Mukufuna chiyani ndi ine, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Ndikupemphani Inu, musandizunze ine!”
29 For he comaundide the vncleene spirit, that he schulde go out fro the man. For he took hym ofte tymes, and he was boundun with cheynes, and kept in stockis, and, whanne the boondis weren brokun, he was lad of deuelis in to desert.
Pakuti Yesu analamula mzimu woyipawo kuti utuluke mwa munthuyo. Kawirikawiri umamugwira iye, ndipo ngakhale anali womangidwa ndi unyolo dzanja ndi mwendo ndi kuti ankamuyangʼanira, koma amadula maunyolo akewo ndipo ziwanda zimamutengera kumalo a yekha.
30 And Jhesus axide hym, and seide, What name is to thee? And he seide, A legioun; for many deuelis weren entrid in to hym.
Yesu anamufunsa kuti, “Dzina lako ndani?” Iye anayankha kuti, “Legiyo,” chifukwa ziwanda zambiri zinalowa mwa iye.
31 And thei preyden hym, that he schulde not comaunde hem, that thei schulden go in to helle. (Abyssos g12)
Ndipo ziwandazo zimamupempha mobwerezabwereza kuti asazitumize ku dzenje la mdima. (Abyssos g12)
32 And there was a flok of many swyne lesewynge in an hil, and thei preieden hym, that he schulde suffre hem to entre in to hem. And he suffride hem.
Gulu lalikulu la nkhumba limadya pamenepo mʼmbali mwa phiri. Ziwandazo zinamupempha Yesu kuti azilole kuti zikalowe mu nkhumbazo ndipo Iye anazilola.
33 And so the deuelis wenten out fro the man, and entriden in to the swyne; and with a birre the flok wente heedlyng in to the pool, and was drenchid.
Ziwanda zija zitatuluka mwa munthuyo, zinakalowa mwa nkhumbazo, ndipo gulu lonselo linathamangira ku mtsetse ndi kukalowa mʼnyanja ndi kumira.
34 And whanne the hirdis sayn this thing don, thei flowen, and tolden in to the cite, and in to the townes.
Oweta nkhumbazo ataona zimene zinachitikazo, anathamanga ndi kukanena izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi.
35 And thei yeden out to se that thing that was don. And thei camen to Jhesu, and thei founden the man sittynge clothid, fro whom the deuelis wenten out, and in hool mynde at hise feet; and thei dredden.
Ndipo anthu anapita kukaona zimene zinachitika. Atafika kwa Yesu, anapeza munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja atakhala pa mapazi a Yesu, atavala ndipo ali ndi nzeru zake; ndipo iwo anachita mantha.
36 And thei that sayn tolden to hem, hou he was maad hool of the legioun.
Amene anaona izi anawuza anthu mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anachiritsidwira.
37 And al the multitude of the cuntre of Gerasenus preiede hym, that he schulde go fro hem, for thei werun holdun with greet drede. He wente vp in to a boot, and turnede ayen.
Kenaka anthu onse a ku chigawo cha Gerasa anamupempha Yesu kuti achoke kwa iwo, chifukwa anadzazidwa ndi mantha. Choncho Iye analowa mʼbwato nachoka.
38 And the man of whom the deuelis weren gon out, preide hym, that he schulde be with hym. Jhesus lefte hym,
Munthu amene anatulutsidwa ziwanda uja, anapempha Yesu kuti apite nawo, koma Yesu anamubweza nati,
39 and seide, Go ayen in to thin hous, and telle hou grete thingis God hath don to thee. And he wente thorow al the cite, and prechide, hou grete thingis Jhesus hadde don to hym.
“Bwerera kwanu kafotokoze zimene Mulungu wakuchitira.” Ndipo munthuyo anachoka ndi kukanena ku mzinda wonsewo zimene Yesu anamuchitira iye.
40 And it was don, whanne Jhesus was gon ayen, the puple resseyuede hym; for alle weren abidynge hym.
Yesu atabwerera, gulu lalikulu la anthu linamulandira, chifukwa onse ankamuyembekezera.
41 And lo! a man, to whom the name was Jayrus, and he was prynce of a synagoge; and he fel doun at the feet of Jhesu, and preiede hym, that he schulde entre in to his hous,
Nthawi yomweyo munthu wotchedwa Yairo, woweruza wa mu sunagoge, anabwera ndi kugwa pa mapazi a Yesu, namupempha Iye kuti apite ku nyumba kwake,
42 for he hadde but o douyter `almost of twelue yeer eelde, and sche was deed. And it bifel, the while he wente, he was thrungun of the puple.
chifukwa mwana wake yekhayo wamkazi, kamtsikana ka zaka khumi ndi ziwiri, kanali pafupi kufa. Pamene Yesu ankapita gulu la anthu linkamupanikiza.
43 And a womman that hadde a flux of blood twelue yeer, and hadde spendid al hir catel in leechis, and sche miyte not be curid of ony,
Ndipo pomwepo panali mayi wina amene ankataya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri, koma panalibe wina akanamuchiritsa.
44 and sche cam nyy bihynde, and touchide the hem of his cloth, and anoon the fluxe of hir blood ceesside.
Iye anafika kumbuyo kwake ndi kukhudza mothera mwa chovala chake, ndipo nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka.
45 And Jhesus seide, Who is that touchide me? And whanne alle men denyeden, Petre seide, and thei that weren with hym, Comaundour, the puple thristen, and disesen thee, and thou seist, Who touchide me?
Yesu anafunsa kuti, “Wandikhudza ndani?” Onse atakana, Petro anati, “Anthu akukupanikizani ndi kukukankhani.”
46 And Jhesus seide, Summan hath touchid me, for that vertu yede out of me.
Koma Yesu anati, “Wina wandikhudza; ndikudziwa chifukwa mphamvu yachoka mwa Ine.”
47 And the womman seynge, that it was not hid fro hym, cam tremblynge, and fel doun at hise feet, and for what cause sche hadde touchid hym sche schewide bifor al the puple, and hou anoon sche was helid.
Ndipo mayiyo podziwa kuti sanathe kuchoka wosadziwika, anabwera akunjenjemera ndipo anagwa pa mapazi a Yesu. Pamaso pa anthu onse, anafotokoza chifukwa chimene anamukhudzira Iye ndi mmene iye anachiritsidwira nthawi yomweyo.
48 And he seide to hir, Douytir, thi feith hath maad thee saaf; go thou in pees.
Kenaka anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere.”
49 And yit while he spak, a man cam fro the prince of the synagoge, and seide to hym, Thi douytir is deed, nyle thou trauel the maister.
Pamene Yesu ankayankhulabe, munthu wina anabwera kuchokera ku nyumba ya Yairo, woweruza wa ku sunagoge uja. Iye anati, “Mwana wanu wa mkazi wamwalira, musawavutitsenso Aphunzitsiwa.”
50 And whanne this word was herd, Jhesus answeride to the fadir of the damysel, Nyle thou drede, but bileue thou oonli, and sche schal be saaf.
Atamva zimenezi, Yesu anati kwa Yairo, “Usachite mantha, ingokhulupirira basi ndipo adzachiritsidwa.”
51 And whanne he cam to the hous, he suffride no man to entre with hym, but Petir and Joon and James, and the fadir and the modir of the damysel.
Iye atafika ku nyumba ya Yairo, sanalole wina aliyense kulowa kupatula Petro, Yohane, ndi Yakobo ndi abambo ndi amayi a mwanayo.
52 And alle wepten, and biweileden hir. And he seide, Nyle ye wepe, for the damysel is not deed, but slepith.
Pa nthawiyi nʼkuti anthu onse akubuma ndi kumulirira iye. Yesu anati, “Lekani kulira, sanafe koma wagona tulo.”
53 And thei scorneden hym, and wisten that sche was deed.
Iwo anamuseka podziwa kuti anali atamwalira.
54 But he helde hir hoond, and criede, and seide, Damysel, rise vp.
Koma Iye anamugwira dzanja lake ndipo anati, “Mwana wanga, dzuka!”
55 And hir spirit turnede ayen, and sche roos anoon. And he comaundide to yyue to hir to ete.
Mzimu wake unabwerera, ndipo nthawi yomweyo anayimirira. Kenaka Yesu anawawuza kuti amupatse chakudya.
56 And hir fadir and modir wondriden greetli; and he comaundide hem, that thei schulden not seie to ony that thing that was don.
Makolo ake anadabwa, koma Iye anawalamulira kuti asawuze wina aliyense zimene zinachitikazo.

< Luke 8 >