< Revelation 11 >

1 A reed like a rod was given to me. Someone said, “Rise and measure God’s temple, and the altar, and those who worship in it.
Ndinapatsidwa bango longa ndodo yoyezera ndipo ndinawuzidwa kuti, “Pita, kayeze Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukawerenge anthu opembedza mʼNyumbamo.
2 Leave out the court which is outside of the temple, and don’t measure it, for it has been given to the nations. They will tread the holy city under foot for forty-two months.
Koma bwalo lakunja ulisiye, usaliyeze chifukwa linaperekedwa kwa a mitundu ina. Iwo adzawupondereza mzinda woyerawo kwa miyezi 42.
3 I will give power to my two witnesses, and they will prophesy one thousand two hundred sixty days, clothed in sackcloth.”
Ndipo ndidzapereka mphamvu kwa mboni zanga ziwiri, zitavala ziguduli, ndipo kwa masiku 1,260 zidzakhala zikulalikira.”
4 These are the two olive trees and the two lamp stands, standing before the Lord of the earth.
Mboni ziwirizo ndi mitengo iwiri ya olivi ndi zoyikapo nyale ziwiri zija zimene zili pamaso pa Ambuye wa dziko lapansi.
5 If anyone desires to harm them, fire proceeds out of their mouth and devours their enemies. If anyone desires to harm them, he must be killed in this way.
Ngati wina atafuna kuzipweteka mbonizo, moto umatuluka mʼkamwa mwawo ndikuwononga adani awo.
6 These have the power to shut up the sky, that it may not rain during the days of their prophecy. They have power over the waters, to turn them into blood, and to strike the earth with every plague, as often as they desire.
Mbonizo zili ndi mphamvu yomanga mvula kuti isagwe pa nthawi imene akulalikirayo; ndipo zili ndi mphamvu yosanduliza madzi kukhala magazi ndi yokantha dziko lapansi ndi miliri ya mitundumitundu nthawi iliyonse imene zingafune.
7 When they have finished their testimony, the beast that comes up out of the abyss will make war with them, and overcome them, and kill them. (Abyssos g12)
Tsono zikadzatsiriza umboni wawowo, chirombo chotuluka mʼChidzenje chakuya chija chidzachita nawo nkhondo nʼkuzigonjetsa mpaka kuzipha. (Abyssos g12)
8 Their dead bodies will be in the street of the great city, which spiritually is called Sodom and Egypt, where also their Lord was crucified.
Mitembo yawo idzakhala ili gone pabwalo la mu mzinda waukulu umene mozimbayitsa umatchedwa Sodomu ndi Igupto, kumenenso Ambuye wawo anapachikidwako.
9 From among the peoples, tribes, languages, and nations, people will look at their dead bodies for three and a half days, and will not allow their dead bodies to be laid in a tomb.
Kwa masiku atatu ndi theka, anthu ochokera ku mtundu uliwonse, fuko lililonse, chiyankhulo chilichonse ndi dziko lililonse, azidzayangʼanitsitsa mitembo yawoyo koma adzakana kuyikwirira.
10 Those who dwell on the earth will rejoice over them, and they will be glad. They will give gifts to one another, because these two prophets tormented those who dwell on the earth.
Anthu okhala pa dziko lapansi adzasangalala nazo zimenezi. Adzachita chikondwerero ndi kutumizirana mphatso, chifukwa aneneri awiri amenewa ankasautsa anthu okhala pa dziko lapansi.
11 After the three and a half days, the breath of life from God entered into them, and they stood on their feet. Great fear fell on those who saw them.
Koma patapita masiku atatu ndi theka aja, mpweya wopatsa moyo wochoka kwa Mulungu unalowa mwa aneneriwo, ndipo anayimirira, ndipo amene anawaona anachita mantha aakulu.
12 I heard a loud voice from heaven saying to them, “Come up here!” They went up into heaven in a cloud, and their enemies saw them.
Kenaka aneneri aja anamva mawu ofuwula ochokera kumwamba owawuza kuti, “Bwerani kuno.” Ndipo anapitadi kumwamba mu mtambo adani awo aja akuwaona.
13 In that day there was a great earthquake, and a tenth of the city fell. Seven thousand people were killed in the earthquake, and the rest were terrified and gave glory to the God of heaven.
Nthawi yomweyo panachitika chivomerezi choopsa mwakuti chigawo chimodzi cha magawo khumi a mzinda chinagwa. Anthu 7,000 anaphedwa ndi chivomerezicho, ndipo opulumukawo anachita mantha kwambiri nayamba kutamanda Mulungu wakumwamba.
14 The second woe is past. Behold, the third woe comes quickly.
Tsoka lachiwiri lapita; koma tsoka lachitatu likubwera posachedwapa.
15 The seventh angel sounded, and great voices in heaven followed, saying, “The kingdom of the world has become the Kingdom of our Lord and of his Christ. He will reign forever and ever!” (aiōn g165)
Mngelo wachisanu ndi chiwiri anawomba lipenga lake, ndipo kumwamba kunamveka mawu ofuwula amene anati, “Ufumu wa dziko lapansi uli mʼmanja mwa Ambuye athu ndi Khristu wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.” (aiōn g165)
16 The twenty-four elders, who sit on their thrones before God’s throne, fell on their faces and worshiped God,
Ndipo akuluakulu 24 aja okhala pa mipando yawo yaufumu pamaso pa Mulungu, anadzigwetsa chafufumimba napembedza Mulungu
17 saying: “We give you thanks, Lord God, the Almighty, the one who is and who was, because you have taken your great power and reigned.
Iwo anati, “Ife tikuyamika Inu Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, amene mulipo ndipo munalipo, chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yayikulu, ndipo mwayamba kulamulira.
18 The nations were angry, and your wrath came, as did the time for the dead to be judged, and to give your bondservants the prophets, their reward, as well as to the saints and those who fear your name, to the small and the great, and to destroy those who destroy the earth.”
A mitundu ina anapsa mtima; koma yafika nthawi yoonetsa mkwiyo. Nthawi yakwana yoweruza anthu akufa, yopereka mphotho kwa atumiki anu, aneneri, anthu oyera mtima anu ndi amene amaopa dzina lanu, wamngʼono pamodzi ndi wamkulu yemwe. Yafika nthawi yowononga amene awononga dziko lapansi.”
19 God’s temple that is in heaven was opened, and the ark of the Lord’s covenant was seen in his temple. Lightnings, sounds, thunders, an earthquake, and great hail followed.
Pamenepo anatsekula Nyumba ya Mulungu kumwamba ndipo mʼkati mwake munaoneka Bokosi la Chipangano. Kenaka kunachita mphenzi, phokoso, mabingu, chivomerezi ndipo kunachita mkuntho wamatalala akuluakulu.

< Revelation 11 >