< 2 Corinthians 3 >

1 Are we beginning again to commend ourselves? Or do we need, as do some, letters of commendation to you or from you?
Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena?
2 You are our letter, written in our hearts, known and read by all men,
Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense.
3 being revealed that you are a letter of Christ, served by us, written not with ink, but with the Spirit of the living God; not in tablets of stone, but in tablets that are hearts of flesh.
Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.
4 Such confidence we have through Christ toward God,
Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu.
5 not that we are sufficient of ourselves to account anything as from ourselves; but our sufficiency is from God,
Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu.
6 who also made us sufficient as servants of a new covenant, not of the letter but of the Spirit. For the letter kills, but the Spirit gives life.
Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.
7 But if the service of death, written engraved on stones, came with glory, so that the children of Israel could not look steadfastly on the face of Moses for the glory of his face, which was passing away,
Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala,
8 won’t service of the Spirit be with much more glory?
kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa?
9 For if the service of condemnation has glory, the service of righteousness exceeds much more in glory.
Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo!
10 For most certainly that which has been made glorious has not been made glorious in this respect, by reason of the glory that surpasses.
Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo.
11 For if that which passes away was with glory, much more that which remains is in glory.
Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!
12 Having therefore such a hope, we use great boldness of speech,
Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri.
13 and not as Moses, who put a veil on his face so that the children of Israel wouldn’t look steadfastly on the end of that which was passing away.
Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala.
14 But their minds were hardened, for until this very day at the reading of the old covenant the same veil remains, because in Christ it passes away.
Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha.
15 But to this day, when Moses is read, a veil lies on their heart.
Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo.
16 But whenever someone turns to the Lord, the veil is taken away.
Koma pamene aliyense atembenukira kwa Ambuye, “chophimbacho chimachotsedwa.”
17 Now the Lord is the Spirit; and where the Spirit of the Lord is, there is liberty.
Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu.
18 But we all, with unveiled face seeing the glory of the Lord as in a mirror, are transformed into the same image from glory to glory, even as from the Lord, the Spirit.
Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.

< 2 Corinthians 3 >