< Exodus 36 >

1 Then wrought Bezaleel and Aholiab, and every wise hearted man, in whom the LORD put wisdom and understanding to know how to work all manner of work for the service of the sanctuary, according to all that the LORD had commanded.
Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.”
2 And Moses called Bezaleel and Aholiab, and every wise hearted man, in whose heart the LORD had put wisdom, even every one whose heart moved him to come to the work to do it:
Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito.
3 And they received from Moses all the offering, which the children of Israel had brought for the work of the service of the sanctuary, to make it with. And they brought yet to him free offerings every morning.
Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse.
4 And all the wise men, that wrought all the work of the sanctuary, came every man from his work which they made;
Kotero amisiri onse amene amagwira ntchito yonse ya malo wopatulika anasiya ntchitoyo
5 And they spoke to Moses, saying, The people bring much more than enough for the service of the work, which the LORD commanded to make.
ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.”
6 And Moses gave commandment, and they caused it to be proclaimed throughout the camp, saying, Let neither man nor woman make any more work for the offering of the sanctuary. So the people were restrained from bringing.
Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri,
7 For the things they had were sufficient for all the work to make it, and too much.
chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse.
8 And every wise hearted man among them that wrought the work of the tabernacle made ten curtains of fine twined linen, and blue, and purple, and scarlet: he made them with cherubim of skilful work.
Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi.
9 The length of one curtain was twenty and eight cubits, and the breadth of one curtain four cubits: the curtains were all of one size.
Nsalu zonse zinali zofanana. Mulitali mwake zinali mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri.
10 And he coupled the five curtains one to another: and the other five curtains he coupled one to another.
Iwo analumikiza nsalu zisanu, kuti ikhale nsalu imodzi ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo.
11 And he made loops of blue on the edge of one curtain from the selvedge in the coupling: likewise he made in the extremity of another curtain, in the coupling of the second.
Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo.
12 Fifty loops he made in one curtain, and fifty loops he made in the edge of the curtain which was in the coupling of the second: the loops held one curtain to another.
Iwo anasokerera zokolowekamo makumi asanu pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Anapanga kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana.
13 And he made fifty clasps of gold, and coupled the curtains one to another with the clasps: so it became one tabernacle.
Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi.
14 And he made curtains of goats’ hair for the tent over the tabernacle: eleven curtains he made them.
Iwo anapanga nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zinalipo khumi ndi imodzi.
15 The length of one curtain was thirty cubits, and four cubits was the breadth of one curtain: the eleven curtains were of one size.
Nsalu zonse khumi ndi imodzi zinali zofanana. Mulitali mwake munali mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake munali mamita awiri.
16 And he coupled five curtains by themselves, and six curtains by themselves.
Iwo analumikiza nsalu zisanu kukhala nsalu imodzi ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, analumikizanso kukhala nsalu imodzinso.
17 And he made fifty loops upon the outer edge of the curtain in the coupling, and fifty loops made he upon the edge of the curtain which coupleth the second.
Kenaka anasokerera zokolowekamo makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija ndiponso anapanga zokolowekamo zina makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija.
18 And he made fifty clasps of brass to couple the tent together, that it might be one.
Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi.
19 And he made a covering for the tent of rams’ skins dyed red, and a covering of badgers’ skins above that.
Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu.
20 And he made boards for the tabernacle of shittim wood, standing up.
Iwo anapanga maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho.
21 The length of a board was ten cubits, and the breadth of a board one cubit and a half.
Feremu iliyonse inali yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake munali masentimita 69.
22 One board had two tenons, equally distant one from another: thus did he make for all the boards of the tabernacle.
Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri. Iwo anapanga maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere.
23 And he made boards for the tabernacle; twenty boards for the south side southward:
Anapanga maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho,
24 And forty sockets of silver he made under the twenty boards; two sockets under one board for its two tenons, and two sockets under another board for its two tenons.
ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija.
25 And for the other side of the tabernacle, which is toward the north corner, he made twenty boards,
Iwo anapanganso maferemu makumi awiri a mbali yakumpoto ya chihemacho,
26 And their forty sockets of silver; two sockets under one board, and two sockets under another board.
ndiponso matsinde makumi anayi asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse.
27 And for the sides of the tabernacle westward he made six boards.
Anapanganso maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo,
28 And two boards he made for the corners of the tabernacle in the two sides.
ndiponso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti.
29 And they were coupled beneath, and coupled together at its head, to one ring: thus he did to both of them in both the corners.
Pa ngodya ziwirizi panali maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba atalumikizidwa pa ngowe imodzi. Maferemu onse anali ofanana.
30 And there were eight boards; and their sockets were sixteen sockets of silver, under every board two sockets.
Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse.
31 And he made bars of shittim wood; five for the boards of the one side of the tabernacle,
Iwo anapanganso mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha. Mitanda isanu inali ya maferemu a mbali imodzi ya chihema,
32 And five bars for the boards of the other side of the tabernacle, and five bars for the boards of the tabernacle for the sides westward.
mitanda isanu inanso inali ya maferemu a mbali inayo ndipo mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema.
33 And he made the middle bar to shoot through the boards from the one end to the other.
Anapanga mtanda wapakati omwe umachokera pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso.
34 And he overlaid the boards with gold, and made their rings of gold to be places for the bars, and overlaid the bars with gold.
Iwo anakuta maferemuwo ndi golide ndiponso anapanga mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso anayikuta ndi golide.
35 And he made a veil of blue, and purple, and scarlet, and fine twined linen: with cherubim he made it of skilful work.
Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi.
36 And he made for it four pillars of shittim wood, and overlaid them with gold: their hooks were of gold; and he cast for them four sockets of silver.
Iwo anapanga nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide. Anapanganso ngowe zagolide za nsanamirazo ndi matsinde asiliva anayi.
37 And he made an hanging for the tabernacle door of blue, and purple, and scarlet, and fine twined linen, of needlework;
Anapanga nsalu ya pa chipata cholowera mu chihema, yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira yomwe inali yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso.
38 And its five pillars with their hooks: and he overlaid their tops and their bands with gold: but their five sockets were of brass.
Anapanga nsanamira zisanu ndi ngowe zake. Anakuta pamwamba pa nsanamirazo ndi zomangira zake ndi golide, ndipo anapanganso matsinde asanu amkuwa.

< Exodus 36 >