< 2 Corinthians 10 >

1 Now I Paul myself beseech you by the meekness and gentleness of Christ, who in presence am base among you, but being absent am bold toward you:
Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu!
2 But I beseech you, that I may not be bold when I am present with that confidence, with which I think to be bold against some, who think of us as if we walked according to the flesh.
Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kumeneko ndisadzachite kuyankhula mwamphamvu monga mmene ndimayembekezera kudzachita kwa anthu ena amene amaganiza kuti machitidwe athu ndi ofanana ndi anthu a dziko lapansi.
3 For though we walk in the flesh, we do not war according to the flesh:
Ngakhale ife timakhala mʼdziko lapansi, sitimenya nkhondo monga mmene dziko lapansi limachitira.
4 ( For the weapons of our warfare are not carnal, but mighty through God to the pulling down of strong holds; )
Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga.
5 Casting down imaginations, and every high thing that exalteth itself against the knowledge of God, and bringing into captivity every thought to the obedience of Christ;
Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
6 And having in a readiness to punish all disobedience, when your obedience is fulfilled.
Ndipo ife tidzakhala okonzeka kulanga aliyense wosamvera ngati inuyo mutakhala omvera kwenikweni.
7 Do ye look on things after the outward appearance? If any man trusteth to himself that he is Christ’s, let him of himself think this again, that, as he is Christ’s, even so are we Christ’s.
Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye.
8 For though I should boast somewhat more of our authority, which the Lord hath given us for edification, and not for your destruction, I should not be ashamed:
Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi.
9 That I may not seem as if I would terrify you by letters.
Ine sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga.
10 For his letters, say they, are weighty and powerful; but his bodily presence is weak, and his speech contemptible.
Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.”
11 Let such a person think this, that, such as we are in word by letters when we are absent, such will we be also in deed when we are present.
Anthu oterewa ayenera kuzindikira kuti zomwe timalemba mʼmakalata tili kutali ndi zomwe tidzakhale tili komweko.
12 For we dare not make ourselves of the number, or compare ourselves with some that commend themselves: but they measuring themselves by themselves, and comparing themselves among themselves, are not wise.
Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru.
13 But we will not boast of things without our measure, but according to the measure of the rule which God hath distributed to us, a measure to reach even to you.
Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu.
14 For we stretch not ourselves beyond our measure, as though we reached not to you: for we are come as far as to you also in preaching the gospel of Christ:
Pakuti sitikudzitama modutsa malire ngati kuti sitinafike kwa inu, popeza tinali oyamba kufika kwa inu ndi Uthenga Wabwino wa Khristu.
15 Not boasting of things without our measure, that is, of other men’s labours; but having hope, when your faith is increased, that we shall be enlarged by you according to our rule abundantly,
Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri,
16 To preach the gospel in the regions beyond you, and not to boast in another man’s line of things made ready to our hand.
kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina.
17 But he that glorieth, let him glory in the Lord.
Koma, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
18 For not he that commendeth himself is approved, but whom the Lord commendeth.
Pakuti munthu amene amavomerezedwa, si amene amadziyenereza yekha, koma munthu amene Ambuye amuyenereza.

< 2 Corinthians 10 >