< Zechariah 6 >

1 Then I turned and lifted my eyes and I saw four chariots coming out from between two mountains; and the two mountains were made of bronze.
Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona magaleta anayi akutuluka pakati pa mapiri awiri, mapiri amkuwa.
2 The first chariot had red horses, the second chariot had black horses,
Galeta loyamba limakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiwiri ndi akavalo akuda,
3 the third chariot had white horses, and the fourth chariot had spotted gray horses.
lachitatu ndi akavalo oyera, ndipo lachinayi ndi akavalo otuwa a mawanga ofiirira, onsewa anali akavalo amphamvu kwambiri.
4 So I answered and said to the angel who talked with me, “What are these, my master?”
Ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane uja kuti, “Kodi mbuye wanga chimenechi nʼchiyani?”
5 The angel answered and said to me, “These are the four winds of heaven that go out from the place where they were standing before the Lord of all the earth.
Mngeloyo anandiyankha kuti, “Imeneyi ndi mizimu inayi yakumwamba, imene ikuchokera pamaso pa Ambuye wa dziko lonse.
6 The one with the black horses is going out to the north country; the white horses are going out to the west country; and the spotted gray horses are going out to the south country.”
Galeta la akavalo akuda likupita ku dziko la kumpoto, galeta la akavalo oyera likutsatira, ndipo galeta la akavalo amawanga ofiirira likupita ku dziko la kummwera.”
7 These strong horses went out and sought to go and roam over the earth, so the angel said, “Go and roam over the earth!” and they left for all the earth.
Pamene akavalo amphamvuwa ankapita, anali ndi changu chofuna kuyendera dziko lapansi. Ndipo iye anati, “Pitani, kayendereni dziko lapansi!”
8 Then he called out to me and spoke to me and said, “Look at the ones that are going out to the north country; they will appease my spirit concerning the north country.”
Pamenepo anandiyitana, “Taona, akavalo amene apita ku dziko la kumpoto apumulitsa Mzimu wanga kumeneko.”
9 So the word of Yahweh came to me, saying,
Yehova anayankhula nane kuti,
10 “Take an offering from the exiles—from Heldai, Tobijah, and Jedaiah—and go this same day and take it into the house of Josiah son of Zephaniah, who has come from Babylon.
“Landira mphatso kuchokera kwa anthu amene abwera ku ukapolo, Helidai, Tobiya ndi Yedaya, amene achokera ku Babuloni. Tsiku lomwelo pita ku nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya.
11 Then take the silver and gold, make a crown and set it upon the head of Joshua son of Jehozadak, the high priest.
Tenga siliva ndi golide upange chipewa chaufumu, ndipo uchiyike pamutu pa mkulu wa ansembe, Yoswa mwana wa Yehozadaki.
12 Speak to him and say, 'Yahweh of hosts says this: This man, his name is Branch! He will grow up where he is and will then build the temple of Yahweh!
Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova.
13 It is he who builds the temple of Yahweh, and he will be clothed with royal splendor, and will sit and rule on his throne. He will be a priest on his throne, and he will bear a counsel of peace between the two.
Ndiye amene adzamange Nyumba ya Yehova, adzalandira ulemerero waufumu ndipo adzalamulira pa mpando wake waufumu. Adzakhalanso wansembe pa mpando wake waufumu. Ndipo padzakhala mtendere.’
14 The crown will given to Heldai, Tobijah, Jedaiah, and for Hen son of Zephaniah as a memorial in the temple of Yahweh.
Chipewa cha ufumucho adzachipereka kwa Helemu, Tobiya, Yedaya, ndi kwa Heni mwana wa Zefaniya, kuti chikhale chikumbutso mʼNyumba ya Yehova.
15 Then those who are far off will come and build the temple of Yahweh, so you will know that Yahweh of hosts has sent me to you; for this will happen if you truly listen to the voice of Yahweh your God!'”
Anthu okhala kutali adzabwera kudzathandiza kumanga Nyumba ya Yehova, ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. Zimenezi zidzachitika ngati mudzamvera mwachangu Yehova Mulungu wanu.”

< Zechariah 6 >