< Revelation 12 >

1 Then a great portent was seen in the heavens – a woman whose robe was the sun, and who had the moon under her feet, and on her head a crown of twelve stars.
Chizindikiro chachikulu chinaoneka kuthambo; mayi atavala dzuwa, mapazi ake ataponda mwezi, pamutu pake pali chipewa chaufumu chokhala ndi nyenyezi khumi ndi ziwiri.
2 She was pregnant; and she is crying out in the pain and agony of childbirth.
Mayiyo anali woyembekezera ndipo pa nthawi yake yochira analira mokuwa chifukwa cha ululu wakubala.
3 Another portent also was seen in the heavens There was a great red Dragon, with seven heads and ten horns, and on his heads were seven diadems.
Kenaka ku thambo kunaonekanso chizindikiro china; chinjoka chachikulu kwambiri, chofiira chomwe chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi; pamutu uliwonse chitavala chipewa chaufumu.
4 His tail draws after it a third of the stars in the heavens, and it hurled them down on the earth. The Dragon is standing in front of the woman who is about to give birth to the child, so that he may devour it as soon as it is born.
Mchira wake unakokolola gawo limodzi la magawo atatu a nyenyezi kuzichotsa ku thambo ndi kuziponya pa dziko lapansi. Chinjoka chija chinadzayima patsogolo pa mayi uja amene anali pafupi kuberekayu kuti mwanayo akangobadwa chimudye.
5 The woman gave birth to a son, a male child, who is destined to rule all the nations with an iron rod; and her child was at once caught up to God on his throne.
Mayiyo anabereka mwana wamwamuna amene adzalamulira anthu a mitundu ina yonse ndi ndodo yachitsulo. Ndipo mwanayo analandidwa ku dzanja la mayiyo ndi kupita naye kwa Mulungu ku mpando wake waufumu.
6 But the woman fled into the wilderness, where there is a place prepared for her by God, to be tended there for twelve hundred and sixty days.
Mayiyo anathawira ku chipululu ku malo kumene Mulungu anamukonzera, kumene akasamalidweko masiku 1,260.
7 Then a battle took place in the heavens. Michael and his angels fought with the Dragon. But though the Dragon, with his angels, fought,
Zitatero, kumwamba kunayambika nkhondo. Mikayeli ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho ndi angelo ake anabwezeranso.
8 he did not prevail; and there was no place left for them any longer in the heavens.
Koma analibe mphamvu ndipo anagonjetsedwa nathamangitsidwa kumwambako.
9 Then the great Dragon, the primeval snake, known as the “devil” and “Satan,” who deceives all the world, was hurled down to the earth, and his angels were hurled down with him.
Chinjoka chachikulu chija chinagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakalekale ija yotchedwa Mdierekezi kapena Satana, amene amasocheretsa anthu a pa dziko lonse lapansi. Chinaponyedwa pa dziko la pansi pamodzi ndi angelo ake.
10 And I heard a loud voice in heaven which said – “Now has begun the day of the salvation, and Power, and Dominion of our God, and the Rule of his Christ; for the Accuser of our people has been hurled down, he who has been accusing them before our God day and night.
Kenaka ndinamva mawu ofuwula kumwamba akunena kuti, “Tsopano chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wake zabwera. Pakuti woneneza abale athu uja, amene amangokhalira kuwaneneza pamaso pa Mulungu usana ndi usiku, wagwetsedwa pansi.
11 Their victory was due to the blood of the Lamb, and to the message to which they bore their testimony. In their love of life they shrank not from death.
Abale athuwo anamugonjetsa ndi magazi a Mwana Wankhosa ndiponso mawu a umboni wawo. Iwo anadzipereka kwathunthu, moti sanakonde miyoyo yawo.
12 Therefore, be glad, heaven, and all who live in heaven! Alas for the earth and for the sea, for the devil has gone down to you in great fury, knowing that he has but little time.”
Choncho, kondwerani, inu dziko lakumwamba ndi onse okhala kumeneko! Koma tsoka dziko lapansi ndi nyanja chifukwa Mdierekezi wagwetsedwa kwa inu! Iye wadzazidwa ndi ukali chifukwa akudziwa kuti nthawi yake ndi yochepa.”
13 When the Dragon saw that he was hurled down to the earth, he pursued the woman who had given birth to the male child.
Pamene chinjokacho chinaona kuti chagwetsedwa pa dziko lapansi, chinayamba kuthamangitsa mayi uja amene anali atabala mwana wamwamunayu.
14 But to the woman were given the two wings of the great eagle, so that she might fly to her place in the wilderness, where she is being tended for one year, and for two years, and for half a year in safety from the snake.
Mayiyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu kuti athawire ku malo ake aja a ku chipululu. Kumeneko adzasamalidwako zaka zitatu ndi theka kuti chinjoka chija chisamupeze.
15 Then the snake poured water from its mouth after the woman, like a river, so that it might sweep her away.
Kenaka chinjoka chija chinalavulira mayiyo madzi ambiri ngati mtsinje, kuti madziwo amukokolole.
16 But Earth came to her help, and opened her mouth and drank up the river which the Dragon had poured out of its mouth.
Koma dziko lapansi linamuthandiza mayiyo. Nthaka inatsekuka ndi kumeza mtsinje uja unachokera mʼkamwa mwa chinjokacho.
17 The Dragon was enraged at the woman, and went to fight with the rest of her offspring – those who lay to heart the commands of God and bear their testimony to Jesus;
Pamenepo chinjokacho chinamupsera mtima mayiyo ndipo chinachoka kupita kukachita nkhondo ndi ana ena onse a mayiyo, ndiye kuti anthu amene anasunga malamulo a Mulungu ndi kuchitira umboni za Yesu.

< Revelation 12 >