< 1 John 2 >

1 My little children, these things write I to you, that you sin not. And if any man sin, we have an advocate with the Father, Jesus Christ the righteous:
Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, Yesu Khristu, Wolungamayo.
2 And he is the propitiation for our sins: and not for ours only, but also for the sins of the whole world.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso machimo onse a dziko lapansi.
3 And hereby we do know that we know him, if we keep his commandments.
Ife timatsimikiza kuti tikumudziwa ngati tikusunga malamulo ake.
4 He that says, I know him, and keeps not his commandments, is a liar, and the truth is not in him.
Munthu akamanena kuti, “Ine ndimadziwa Mulungu,” koma samvera malamulo a Mulunguyo, ndi wabodza ameneyo ndipo mwa iye mulibe choonadi.
5 But whoever keeps his word, in him truly is the love of God perfected: hereby know we that we are in him.
Koma munthu aliyense akamvera mawu ake, ndiye kuti chikondi cha Mulungu chafikadi penipeni mwa iyeyo. Pamenepo timatsimikizadi kuti tili mwa Iye.
6 He that says he stays in him ought himself also so to walk, even as he walked.
Aliyense amene amati amakhala mwa Mulungu, ayenera kukhala moyo umene Yesu ankakhala.
7 Brothers, I write no new commandment to you, but an old commandment which you had from the beginning. The old commandment is the word which you have heard from the beginning.
Okondedwa, sindikukulemberani lamulo latsopano koma lakale lomwe lija, limene munali nalo kuyambira pachiyambi. Lamulo la kalelo ndi mawu amene munawamva kale.
8 Again, a new commandment I write to you, which thing is true in him and in you: because the darkness is past, and the true light now shines.
Komabe ndi lamulo latsopano limene ndikukulemberani. Choonadi chake chikuoneka mwa Yesu ndiponso mwa inu, chifukwa mdima ukutha ndipo kuwunika kwenikweni kwayamba kale kuwala.
9 He that says he is in the light, and hates his brother, is in darkness even until now.
Aliyense amene amati ali mʼkuwunika, koma nʼkumadana ndi mʼbale wake ali mu mdima.
10 He that loves his brother stays in the light, and there is none occasion of stumbling in him.
Aliyense amene amakonda mʼbale wake amakhalanso mʼkuwunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.
11 But he that hates his brother is in darkness, and walks in darkness, and knows not where he goes, because that darkness has blinded his eyes.
Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.
12 I write to you, little children, because your sins are forgiven you for his name’s sake.
Inu ana okondedwa, ndikukulemberani popeza kuti machimo anu akhululukidwa chifukwa cha dzina la Yesu.
13 I write to you, fathers, because you have known him that is from the beginning. I write to you, young men, because you have overcome the wicked one. I write to you, little children, because you have known the Father.
Inu abambo, ndikukulemberani popeza kuti munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani popeza kuti munagonjetsa woyipayo.
14 I have written to you, fathers, because you have known him that is from the beginning. I have written to you, young men, because you are strong, and the word of God stays in you, and you have overcome the wicked one.
Ana okondedwa, ndikukulemberani chifukwa mumawadziwa Atate. Abambo, ndikukulemberani chifukwa munamudziwa Iye amene analipo kuyambira pachiyambi. Inu anyamata, ndikukulemberani chifukwa ndinu amphamvu. Mawu a Mulungu amakhala mwa inu ndipo mumamugonjetsa woyipayo.
15 Love not the world, neither the things that are in the world. If any man love the world, the love of the Father is not in him.
Musamakonde dziko lapansi kapena chilichonse cha dziko lapansi. Ngati munthu wina aliyense akonda dziko lapansi, mwa iyeyo mulibe chikondi chokonda Atate.
16 For all that is in the world, the lust of the flesh, and the lust of the eyes, and the pride of life, is not of the Father, but is of the world.
Pakuti zonse za mʼdziko lapansi, zilakolako za thupi, zinthu zimene maso amakhumbira ndiponso kuyandikira zinthu za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.
17 And the world passes away, and the lust thereof: but he that does the will of God stays for ever. (aiōn g165)
Dziko lapansi likupita pamodzi ndi zilakolako zake, koma amene amachita chifuniro cha Mulungu amakhalapo mpaka muyaya. (aiōn g165)
18 Little children, it is the last time: and as you have heard that antichrist shall come, even now are there many antichrists; whereby we know that it is the last time.
Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza.
19 They went out from us, but they were not of us; for if they had been of us, they would no doubt have continued with us: but they went out, that they might be made manifest that they were not all of us.
Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu.
20 But you have an unction from the Holy One, and you know all things.
Koma inu muli ndi kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo nonsenu mukudziwa choonadi.
21 I have not written to you because you know not the truth, but because you know it, and that no lie is of the truth.
Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi.
22 Who is a liar but he that denies that Jesus is the Christ? He is antichrist, that denies the Father and the Son.
Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana.
23 Whoever denies the Son, the same has not the Father: he that acknowledges the Son has the Father also.
Aliyense wokana Mwana alibenso Atate. Wovomereza Mwana alinso ndi Atate.
24 Let that therefore abide in you, which you have heard from the beginning. If that which you have heard from the beginning shall remain in you, you also shall continue in the Son, and in the Father.
Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate.
25 And this is the promise that he has promised us, even eternal life. (aiōnios g166)
Ndipo chimene anatilonjeza nʼchimenechi: moyo wosatha. (aiōnios g166)
26 These things have I written to you concerning them that seduce you.
Ine ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuwuzeni za amene akufuna kukusocheretsani.
27 But the anointing which you have received of him stays in you, and you need not that any man teach you: but as the same anointing teaches you of all things, and is truth, and is no lie, and even as it has taught you, you shall abide in him.
Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.
28 And now, little children, abide in him; that, when he shall appear, we may have confidence, and not be ashamed before him at his coming.
Tsopano ana okondedwa, khalani mwa Yesu, kuti pamene adzaonekera, ife tidzakhale otsimikizika mu mtima ndi wopanda manyazi pamaso pake akamadzabwera.
29 If you know that he is righteous, you know that every one that does righteousness is born of him.
Popeza mukudziwa kuti Khristu ndi wolungama, choncho mukudziwanso kuti aliyense amene amachita chilungamo ndi mwana wa Mulungu.

< 1 John 2 >