< 1 Samuel 13 >

1 Saul was — years old when he began to reign; and two years he reigned over Israel.
Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42.
2 And Saul chose him three thousand men of Israel; whereof two thousand were with Saul in Michmas and in the mount of Beth-el, and a thousand were with Jonathan in Gibeath-benjamin; and the rest of the people he sent every man to his tent.
Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo.
3 And Jonathan smote the garrison of the Philistines that was in Geba, and the Philistines heard of it. And Saul blew the horn throughout all the land, saying: 'Let the Hebrews hear.'
Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli.
4 And all Israel heard say that Saul had smitten the garrison of the Philistines, and that Israel also had made himself odious with the Philistines. And the people were gathered together after Saul to Gilgal.
Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala.
5 And the Philistines assembled themselves together to fight with Israel, thirty thousand chariots, and six thousand horsemen, and people as the sand which is on the sea-shore in multitude; and they came up, and pitched in Michmas, eastward of Beth-aven.
Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni.
6 When the men of Israel saw that they were in a strait — for the people were distressed — then the people did hide themselves in caves, and in thickets, and in rocks, and in holds, and in pits.
Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime.
7 Now some of the Hebrews had gone over the Jordan to the land of Gad and Gilead; but as for Saul, he was yet in Gilgal, and all the people followed him trembling.
Ahebri ena anawoloka Yorodani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Koma Sauli anakhalabe ku Giligala ndipo ankhondo onse amene anali naye anali njenjenje ndi mantha.
8 And he tarried seven days, according to the set time that Samuel had appointed; but Samuel came not to Gilgal; and the people were scattered from him.
Saulo anadikirira masiku asanu ndi awiri, monga mwa nthawi imene ananena Samueli. Koma Samueli sanabwere ku Giligala, ndipo anthu anayamba kumuthawa Sauli uja.
9 And Saul said: 'Bring hither to me the burnt-offering and the peace-offerings.' And he offered the burnt-offering.
Kotero iye anati, “Bwera nayoni nsembe yopsereza ndi nsembe ya chiyanjano.” Ndipo Sauli anapereka nsembe yopsereza.
10 And it came to pass that, as soon as he had made an end of offering the burnt-offering, behold, Samuel came; and Saul went out to meet him, that he might salute him.
Atangomaliza kupereka nsembe, anangoona Samueli watulukira ndipo Sauli anapita kukamulonjera.
11 And Samuel said: 'What hast thou done?' And Saul said: 'Because I saw that the people were scattered from me, and that thou camest not within the days appointed, and that the Philistines assembled themselves together against Michmas;
Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?” Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi,
12 therefore said I: Now will the Philistines come down upon me to Gilgal, and I have not entreated the favour of the LORD; I forced myself therefore, and offered the burnt-offering.'
ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza.”
13 And Samuel said to Saul: 'Thou hast done foolishly; thou hast not kept the commandment of the LORD thy God, which He commanded thee; for now would the LORD have established thy kingdom upon Israel for ever.
Samueli anati, “Mwachita zopusa. Simunatsate zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muchite. Mukanazitsata, Yehova akanawukhazikitsa ufumu wanu mu Israeli mpaka kalekale.
14 But now thy kingdom shall not continue; the LORD hath sought him a man after His own heart, and the LORD hath appointed him to be prince over His people, because thou hast not kept that which the LORD commanded thee.'
Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Yehova wapeza munthu wapamtima pake ndipo wamusankha kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa inu simunasunge malamulo a Yehova.”
15 And Samuel arose, and got him up from Gilgal unto Gibeath-benjamin. And Saul numbered the people that were present with him, about six hundred men.
Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600.
16 And Saul, and Jonathan his son, and the people that were present with them, abode in Gibeath-benjamin; but the Philistines encamped in Michmas.
Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi.
17 And the spoilers came out of the camp of the Philistines in three companies: one company turned unto the way that leadeth to Ophrah, unto the land of Shual;
Ankhondo a Afilisti anatuluka mʼmisasa yawo mʼmagulu atatu. Gulu lina linapita ku Ofiri ku dziko la Suwala.
18 and another company turned the way to Beth-horon; and another company turned the way of the border that looketh down upon the valley of Zeboim toward the wilderness.
Gulu lina linalunjika ku Beti-Horoni, ndipo gulu lachitatu linalunjika ku malire oyangʼanana ndi chigwa cha Zeboimu cha ku chipululu.
19 Now there was no smith found throughout all the land of Israel; for the Philistines said: 'Lest the Hebrews make them swords or spears';
Nthawi imeneyo nʼkuti mulibe osula zitsulo mʼdziko lonse la Israeli, pakuti Afilisti anati, “Tisawalole Aheberi kudzipangira okha malupanga kapena mikondo!”
20 but all the Israelites went down to the Philistines, to sharpen every man his plowshare, and his coulter, and his axe, and his mattock.
Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo.
21 And the price of the filing was a pim for the mattocks, and for the coulters, and for the forks with three teeth, and for the axes; and to set the goads.
Mtengo wonolera mapulawo ndi makasu unali zigawo ziwiri za sekeli, mtengo wonolera zisonga ndi nkhwangwa unali gawo limodzi la Sekeli.
22 So it came to pass in the day of battle, that there was neither sword nor spear found in the hand of any of the people that were with Saul and Jonathan; but with Saul and with Jonathan his son was there found.
Motero tsiku la nkhondolo panalibe lupanga kapena mkondo mʼdzanja la aliyense amene anatsatira Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi Yonatani, iwo okha ndiwo anali ndi zida.
23 And the garrison of the Philistines went out unto the pass of Michmas.
Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi.

< 1 Samuel 13 >