< Isaiah 62 >

1 For Zions sake I will not holde my tongue, and for Ierusalems sake I wil not rest, vntil the righteousnes thereof breake foorth as the light, and saluation thereof as a burning lampe.
Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete, chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete, mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala, ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
2 And the Gentiles shall see thy righteousnesse, and all Kings thy glory: and thou shalt be called by a new name, which the mouth of the Lord shall name.
Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako. Adzakuyitanira dzina latsopano limene adzakupatse ndi Yehova.
3 Thou shalt also be a crowne of glory in the hand of the Lord, and a royall diademe in the hand of thy God.
Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova, ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
4 It shall no more be sayd vnto thee, Forsaken, neither shall it be said any more to thy land, Desolate, but thou shalt be called Hephzi-bah, and thy land Beulah: for the Lord deliteth in thee, and thy land shall haue an husband.
Sadzakutchanso “Wosiyidwa,” ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.” Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.” Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.” Chifukwa Yehova akukondwera nawe, ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
5 For as a yong man marieth a virgine, so shall thy sonnes marry thee: and as a bridegrome is glad of the bride, so shall thy God reioyce ouer thee.
Monga mnyamata amakwatira namwali, momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira; monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi, chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.
6 I haue set watchmen vpon thy walles, O Ierusalem, which all the day and all the night continually shall not cease: ye that are mindfull of the Lord, keepe not silence,
Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda; sadzakhala chete usana kapena usiku. Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake musapumule.
7 And giue him no rest, till hee repaire and vntill hee set vp Ierusalem the prayse of the worlde.
Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemu kukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.
8 The Lord hath sworne by his right hand and by his strong arme, Surely I wil no more giue thy corne to be meate for thine enemies, and surely the sonnes of the strangers shall not drinke thy wine, for the which thou hast laboured.
Yehova analumbira atakweza dzanja lake. Anati, “Sindidzaperekanso tirigu wako kuti akhale chakudya cha adani ako, ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano pakuti unamuvutikira.
9 But they that haue gathered it, shall eate it, and prayse the Lord, and the gatherers thereof shall drinke it in the courtes of my Sanctuarie.
Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi ndi kutamanda Yehova, ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo mʼmabwalo a Nyumba yanga.”
10 Go through, go through the gates: prepare you the way for the people: cast vp, cast vp the way, and gather out the stones and set vp a standart for the people.
Tulukani, dutsani pa zipata! Konzerani anthu njira. Lambulani, lambulani msewu waukulu! Chotsani miyala. Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.
11 Beholde, the Lord hath proclaimed vnto the endes of the world: tell the daughter Zion, Beholde, thy Sauiour commeth: beholde, his wages is with him, and his worke is before him.
Yehova walengeza ku dziko lonse lapansi kuti, Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti, “Taonani, chipulumutso chanu chikubwera; Yehova akubwera ndi mphotho yake akubwera nazo zokuyenerani.”
12 And they shall call them, The holy people, the redeemed of the Lord, and thou shalt be named, A citie sought out and not forsaken.
Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika, owomboledwa a Yehova; ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova” “Mzinda umene Yehova sanawusiye.”

< Isaiah 62 >