< Hebrews 3 >

1 Therefore, holy brethren, partakers of the heauenly vocation, consider the Apostle and high Priest of our profession Christ Iesus:
Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.
2 Who was faithfull to him that hath appointed him, euen as Moses was in al his house.
Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.
3 For this man is counted worthy of more glory then Moses, inasmuch as he which hath builded the house, hath more honour then the house.
Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo.
4 For euery house is builded of some man, and he that hath built all things, is God.
Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.
5 Now Moses verely was faithfull in all his house, as a seruant, for a witnesse of the thinges which should be spoken after.
Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo.
6 But Christ is as the Sonne, ouer his owne house, whose house we are, if we holde fast that confidence and that reioycing of that hope vnto the ende.
Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.
7 Wherefore, as the holy Ghost sayth, To day if ye shall heare his voyce,
Tsono monga Mzimu Woyera akuti, “Lero mukamva mawu ake,
8 Harden not your hearts, as in the prouocation, according to the day of the tentation in the wildernes,
musawumitse mitima yanu ngati munachitira pamene munawukira, pa nthawi yoyesedwa mʼchipululu.
9 Where your fathers tempted me, prooued me, and sawe my workes fourtie yeeres long.
Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa, ndipo kwa zaka makumi anayi anaona zimene Ine ndinachita.
10 Wherefore I was grieued with that generation, and sayde, They erre euer in their heart, neither haue they knowen my wayes.
Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo, ndipo Ine ndinati, ‘Nthawi zonse mitima yawo imasochera, ndipo iwo sadziwa njira zanga.’
11 Therefore I sware in my wrath, If they shall enter into my rest.
Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Iwo sadzalowa mu mpumulo wanga.’”
12 Take heede, brethren, least at any time there be in any of you an euill heart, and vnfaithfull, to depart away from the liuing God.
Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
13 But exhort one another dayly, while it is called to day, lest any of you be hardened through the deceitfulnes of sinne.
Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.
14 For we are made partakers of Christ, if we keepe sure vnto the ende that beginning, wherewith we are vpholden,
Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi.
15 So long as it is sayd, To day if ye heare his voyce, harden not your hearts, as in the prouocation.
Monga kunanenedwa kuti, “Lero ngati mumva mawu ake, musawumitse mitima yanu ngati momwe munachitira pamene munawukira.”
16 For some when they heard, prouoked him to anger: howbeit, not all that came out of Egypt by Moses.
Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto?
17 But with whome was he displeased fourtie yeeres? Was hee not displeased with them that sinned, whose carkeises fell in the wildernes?
Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja?
18 And to whom sware he that they should not enter into his rest, but vnto them that obeyed not?
Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja.
19 So we see that they could not enter in, because of vnbeliefe.
Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.

< Hebrews 3 >