< 1 Chronicles 17 >

1 Nowe afterward when Dauid dwelt in his house, he saide to Nathan the Prophet, Beholde, I dwell in an house of cedar trees, but the Arke of the Lordes couenant remaineth vnder curtaines.
Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”
2 Then Nathan said to Dauid, Do all that is in thine heart: for God is with thee.
Natani anayankha Davide kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu, chifukwa Mulungu ali nanu.”
3 And the same night euen the word of God came to Nathan, saying,
Usiku umenewo mawu a Mulungu anafika kwa Natani, ndipo anati,
4 Goe, and tell Dauid my seruant, Thus saith the Lord, Thou shalt not buylde me an house to dwell in:
“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’
5 For I haue dwelt in no house, since the day that I brought out the childre of Israel vnto this daye, but I haue bene from tent to tent, and from habitation to habitation.
Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Israeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda kuchoka mʼtenti ina kupita mʼtenti ina, kuchoka malo ena kupita malo ena.
6 Wheresoeuer I haue walked with all Israel spake I one word to any of the iudges of Israel (whome I commanded to feede my people) saying, Why haue ye not built mee an house of cedar trees?
Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’”
7 Nowe therefore thus shalt thou say vnto my seruant Dauid, Thus saith the Lord of hostes, I tooke thee from the sheepecoat and from following the sheepe, that thou shouldest bee a prince ouer my people Israel.
Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli.
8 And I haue bene with thee whithersoeuer thou hast walked, and haue destroyed all thine enemies out of thy sight, and haue made thee a name, like the name of the great men that are in the earth.
Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.
9 (Also I will appoynt a place for my people Israel, and will plant it, that they may dwell in their place, and moue no more: neither shall the wicked people vexe them any more, as at the beginning,
Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja;
10 And since the time that I commanded iudges ouer my people Israel) And I wil subdue all thine enemies: therefore I say vnto thee, that the Lord wil buylde thee an house.
monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzagonjetsanso adani anu onse. “‘Ine ndikulengeza kwa iwe kuti Yehova adzakhazikitsa banja lako.
11 And when thy dayes shalbe fulfilled to go with thy fathers, then will I rayse vp thy seede after thee, which shalbe of thy sonnes, and will stablish his kingdome.
Masiku ako akadzatha ndipo ukadzatsatira makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, mmodzi mwa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.
12 He shall builde me an house, and I will stablish his throne for euer.
Iye ndiye amene adzandimangira nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya.
13 I wil be his father, and he shalbe my sonne, aud I will not take my mercie away from him, as I tooke it from him that was before thee.
Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo.
14 But I wil establish him in mine house, and in my kingdome for euer, and his throne shalbe stablished for euer,
Ndidzamuyika kukhala wolamulira nyumba yanga ndi ufumu wanga kwamuyaya. Mpando wake waufumu udzakhazikika kwamuyaya.’”
15 According to all these wordes, and according to al this vision. So Nathan spake to Dauid.
Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.
16 And Dauid the King went in and sate before the Lord and said, Who am I, O Lord God, and what is mine house, that thou hast brought me hitherto?
Choncho Mfumu Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati, “Ine ndine yani, Inu Yehova Mulungu, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?
17 Yet thou esteeming this a small thing, O God, hast also spoken concerning the house of thy seruaut for a great while, and hast regarded me according to the estate of a man of hie degree, O Lord God.
Inu Mulungu, kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inuyo mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Mwandiyangʼana ndipo mwandiyesa ngati munthu wolemekezeka kwambiri pakati pa anthu, Inu Yehova Mulungu.”
18 What can Dauid desire more of thee for the honour of thy seruant? for thou knowest thy seruant.
“Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu, pakuti mwachitira ulemu wotere mtumiki wanu? Pakuti Inu mukumudziwa mtumiki wanu.
19 O Lord, for thy seruantes sake, euen according to thine heart hast thou done all this great thing to declare all magnificence.
Inu Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwawulula malonjezo anu aakulu onse.
20 Lord, there is none like thee, neither is there any God besides thee, according to all that we haue heard with our eares.
“Palibe wina wofanana nanu, Inu Yehova, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha monga tamvera ndi makutu athu.
21 Moreouer what one nation in the earth is like thy people Israel, whose God went to redeeme them to be his people, and to make thy selfe a Name, and to doe great and terrible things by casting out nations from before thy people, whom thou hast deliuered out of Egypt?
Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto?
22 For thou hast ordeined thy people Israel to be thine owne people for euer, and thou Lord art become their God.
Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.
23 Therefore nowe Lord, let the thing that thou hast spoken concerning thy seruant and concerning his house, be confirmed for euer, and doe as thou hast sayd,
“Ndipo tsopano Yehova, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake, likhazikitseni kwamuyaya. Chitani monga mwalonjezera,
24 And let thy name be stable and magnified for euer, that it may be sayd, The Lord of hostes, God of Israel, is the God of Israel, and let the house of Dauid thy seruant bee stablished before thee.
kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
25 For thou, O my God, hast reueiled vnto the eare of thy seruant, that thou wilt builde him an house: therefore thy seruant hath bene bolde to pray before thee.
“Inu Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzamumangira nyumba. Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere.
26 Therefore nowe Lord (for thou art God, and hast spoken this goodnesse vnto thy seruant)
Inu Yehova, ndinu Mulungu! Mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu.
27 Now therfore, it hath pleased thee to blesse the house of thy seruant, that it may bee before thee for euer: for thou, O Lord, hast blessed it, and it shalbe blessed for euer.
Ndipo chakukomerani kudalitsa banja la mtumiki wanu kuti likhale pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti Inu Yehova mwalidalitsa, lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”

< 1 Chronicles 17 >