< Psalms 72 >

1 A psalm of Solomon. God, please give the king fairness, and give the king's son the ability to do what's right.
Salimo la Solomoni. Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo, Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.
2 May he rightly judge your people, and may he be fair to the poor.
Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo, anthu anu ozunzika mosakondera.
3 May the mountains bring peace to the people, and the hills bring goodness.
Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu, timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.
4 May he defend the poor and save their children, may he crush those who oppress them.
Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo.
5 May they respect him as long as the sun and the moon shine above, for all generations.
Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse, nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.
6 May his reign be like rain falling on new grass, like showers that water the earth.
Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.
7 May those who live right prosper under his rule; may there be great prosperity until the moon is no more.
Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika; chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.
8 May he rule from sea to sea, from the river to the ends of the earth.
Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
9 Desert tribes will kneel before him; and his enemies will bite the dust.
Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake ndipo adani ake adzanyambita fumbi.
10 The kings of Tarshish and the islands will bring him tribute; the kings of Sheba and Seba will present him with gifts.
Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali adzabweretsa mitulo kwa iye, mafumu a ku Seba ndi Seba adzapereka mphatso kwa iyeyo.
11 Every king will bow down to him; every nation will serve him.
Mafumu onse adzamuweramira ndipo mitundu yonse idzamutumikira.
12 He will help the poor when they cry out to him, and help those who are suffering that have no one to support them.
Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza.
13 He has pity on the poor and needy—he saves their lives!
Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa.
14 He rescues them from violence and oppression, for their lives mean so much to him.
Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.
15 May he live long! May the gold from Sheba be given to him. May people always pray for him and bless him all day long.
Iye akhale ndi moyo wautali; golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye. Anthu amupempherere nthawi zonse ndi kumudalitsa tsiku lonse.
16 May there be plenty of grain in the land, even growing on mountain-tops. May the fruit on the trees sway like the trees of Lebanon. May the people in the city flourish like grass in a field.
Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse; pamwamba pa mapiri pakhale tirigu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni; zichuluke ngati udzu wakuthengo
17 May his fame live forever, may it last as long as the sun. May all nations be blessed through him, and may they praise him.
Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala.
18 Praise the Lord God, the God of Israel, who is the only one who can do such fantastic things!
Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.
19 Praise his wonderful nature forever! May the whole world be full of his glory! Amen and amen!
Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni.
20 (This is the end of the psalms of David, son of Jesse.)
Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.

< Psalms 72 >