< Ezra 5 >

1 The prophets Haggai and Zechariah, son of Iddo, gave messages to the Jews in Judah and Jerusalem from the God of Israel, their ruler.
Nthawi imeneyo aneneri Hagai ndi Zekariya, mwana wa Ido, ankayankhula kwa Ayuda okhala mʼdziko la Yuda ndi mu Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Israeli, amene anali nawo.
2 Then Zerubbabel, son of Shealtiel, and Jeshua, son of Jozadak, decided to start work on rebuilding God's Temple in Jerusalem. The prophets of God encouraged them and helped them.
Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza.
3 Almost immediately Tattenai, the governor of the province west of the Euphrates, Shethar-bozenai, and their fellow officials arrived and asked, “Who gave you permission to rebuild this Temple and finish it?”
Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?”
4 Then they asked, “What are the names of the men who are working on this building?”
Anawafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga nyumbayi mayina awo ndani?”
5 But their God was watching over the Jewish leaders, so that they were not prevented from working until a report could be sent to Darius and a written reply with instructions was received.
Koma Mulungu wawo amayangʼanira atsogoleri Ayuda, motero kuti anthu aja anaganiza kuti asawaletse kumanga Nyumbayo mpaka atalembera mfumu Dariyo kalata ndi kulandira yankho lake.
6 The following is a copy of the letter that Tattenai, the governor of the province west of the Euphrates, Shethar-bozenai, and their fellow officials, officials of the province, sent to King Darius.
Iyi ndi kalata imene Tatenai bwanamkubwa wa dera la patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe amene anali mʼchigawo cha patsidya pa Yufurate, anatumiza kwa mfumu Dariyo
7 The report they sent him read went like this: “To King Darius: Greetings.
Analemba kalatayo motere: Kwa mfumu Dariyo: Mukhale ndi mtendere wonse.
8 We wish to inform Your Majesty that we went to the province of Judah, to the Temple of the great God. It is being built with large stones, with timber beams being placed on the walls. This work is being done properly and is progressing well.
Amfumu mudziwe kuti ife tinapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu ndipo akuyala matabwa pa makoma. Ntchitoyi ikugwiridwa mwachangu ndipo ikuyenda bwino kwambiri mwautsogoleri wawo.
9 We questioned the leaders, asking them, ‘Who gave you permission to rebuild this Temple and finish it?’
Ndipo tinawafunsa atsogoleriwo kuti, “Anakulolezani kuti mumangenso Nyumbayi ndi kutsiriza makoma ake ndani?”
10 We also asked for their names, so that we could write them down and let you know the names of their leaders.
Tinawafunsanso mayina a atsogoleri awo, kuti tikalemba mayina atsogoleriwo tidzakudziwitseni kuti muwadziwe.
11 This is the answer they gave us. ‘We are servants of the God of heaven and earth. We are rebuilding the Temple built and completed many years ago by a great king of Israel.
Yankho limene anatipatsa ndi ili: “Ife ndife atumiki a Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israeli inamanga ndi kuyitsiriza zaka zambiri zapitazo.
12 But our forefathers made the God of heaven angry, so he handed them over to Nebuchadnezzar, king of Babylon, the Chaldean, who destroyed this Temple and deported the people to Babylon.
Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba, Iye anawapereka kwa Nebukadinezara Mkalideya, mfumu ya Babuloni, amene anawononga Nyumbayi ndi kutenga anthu onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
13 However, Cyrus, king of Babylon, in the first year of his reign, issued a decree to rebuild this Temple of God.
“Komabe chaka choyamba cha Koresi, mfumu ya ku Babuloni, mfumu Koresiyo anapereka lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso.
14 He even gave back the gold and silver items belonging to God's Temple, which Nebuchadnezzar had taken from the Temple in Jerusalem and placed in his temple in Babylon. King Cyrus gave them to a man named Sheshbazzar, whom he had appointed governor,
Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa.
15 telling him, Take these items and place them in the Temple in Jerusalem. Rebuild God's Temple on its original site.
Tsono mfumuyo inamuwuza kuti, ‘Tenga ziwiyazi ukaziyike mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo Nyumba ya Mulunguyo ikamangidwenso pa maziko ake akale.’
16 So Sheshbazzar came and laid the foundation of God's Temple in Jerusalem. It has been under construction since then, but hasn't yet been completed.’
“Choncho Sesibazarayo anabwera ndi kumanga maziko a Nyumba ya Mulunguyo mu Yerusalemu. Kuyambira tsiku limenelo mpaka lero yakhala ikumangidwa ndipo sinathebe.”
17 So, if Your Majesty wishes, authorize a search to be made of the royal archives in Babylon to discover if there is a record that King Cyrus issued a decree to rebuild God's Temple in Jerusalem. Then please let us know Your Majesty's decision in this matter.”
Nʼchifukwa chake ngati chingakukomereni amfumu, pachitike kafukufuku mʼnyumba yaufumu mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri ya Babuloni kuti tione ngati mfumu Koresi inalamuladi za kumanganso Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Kenaka amfumu mutiwuze zomwe zikukondweretsani kuti mugamule pa nkhani imeneyi.

< Ezra 5 >