< Ezekiel 42 >

1 The man took me out through the north gate to the outer courtyard into the rooms on the far side of the Temple courtyard by the northern external wall.
Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto ndipo anafika nane ku zipinda zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto.
2 The building with the north-facing door was a hundred cubits long and fifty cubits wide.
Nyumba yakumpotoyi mulitali mwake munali mamita makumi asanu, mulifupi mwake munali mamita 25.
3 It had three floors of open halls on both sides, one facing the twenty-cubit area of the inner courtyard and one facing the pavement of the outer courtyard.
Panali midadada iwiri, umodzi umayangʼanana ndi bwalo lamʼkati la mamita khumi, winawo umayangʼanana ndi bwalo lakunja. Midadada iwiriyi inali ya nyumba zitatu zosanjikana ndipo imayangʼanana.
4 In front of the rooms was an inside walkway ten cubits wide and a hundred cubits long. Their doors opened to the north.
Kumaso kwa zipindazo kunali njira yamʼkati, mulifupi mwake munali mamita asanu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. Makomo ake analoza chakumpoto.
5 The upper rooms were smaller because of the space taken up by the open halls on the lower and middle levels of the building.
Zipinda zammwamba zinali zazifupi mʼmimbamu kupambana zipinda zamʼmunsi ndi zipinda zapakati chifukwa njira zake zinatenga malo ambiri.
6 Since they didn't have pillars like the courtyards, the upper rooms were set farther back than the lower and middle levels.
Popeza zipinda zinali zosanjikizana katatu ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo, motero zipinda zamʼmwamba zinali zochepa kuyerekeza ndi zipinda zapansi ndi zipinda zapakati.
7 An external wall ran in front of the rooms for fifty cubits long parallel to the outer courtyard.
Panali khoma lakunja lomwe limatsatana ndi zipindazo kutsogolo kwake pambali pabwalo lakunja, kutalika kwake kunali mamita 25.
8 The rooms on the outer courtyard extended for fifty cubits, but those that faced the Temple were a hundred cubits long.
Zipinda za mʼmbali mwa bwalo lakunja mulitali mwake munali mamita 25. Koma zomwe zinali mʼmbali mwa Nyumba ya Mulungu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu.
9 Below these rooms was an entrance on the east side coming from the outer courtyard.
Pansi pa zipinda zimenezi panali khomo chakummawa kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma lake linkayambira.
10 Along the wall on the south side of the outer courtyard were rooms next to the courtyard and opposite the building.
Mbali yakummwera kuyangʼanana ndi bwalo ndi nyumbayo kunali zipinda zina.
11 There was a walkway in front of them, just like the rooms on the north side. These rooms had the same length and width, the same doors, floor plan, and exits.
Kumaso kwa zipindazi kunali njira. Zipindazi mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zofanana ndi zipinda zoyangʼana zakumpoto zija. Makomo ndi zitseko zake zinalinso zofanana
12 Similarly there was an entrance under the rooms on the south side of the building, coming from the east side.
ndi makomo a zipinda zakummwera. Kunali khomo mʼmbali ya kummawa kumene ankalowerako. Kunalinso khoma logawa zipinda.
13 The man told me, “The north and south rooms that face the Temple courtyard are holy rooms where the priests who go before the Lord will eat the most holy offerings. They will place the most holy offerings there because the place is holy, and include the grain offerings, the sin offerings, and the guilt offerings.
Ndipo munthuyo anandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakummwera zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi zoyera. Mʼmenemo ansembe amene amakhala pafupi ndi Yehova amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. Mʼmenemo adzayikamo zopereka zopatulika kwambiri, zopereka za chakudya, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi opatulika.
14 Once the priests have entered these rooms, they are not to go to the outer courtyard before leaving their priestly clothes, because these are holy. They must change into other clothes before go where the ordinary people are.”
Pamene ansembe alowa ku malo opatulikawa, asatuluke kupita ku bwalo lakunja popanda kusiya momwemo zovala zimene anavala potumikira zija, pakuti zovalazi ndi zopatulika. Avale kaye zovala zina ndipo akhoza kufika kwa anthu.”
15 After the man finished measuring inside of the Temple area, he took me out through the east gate, and he measured the surrounding area as well.
Munthuyo atamaliza kuyeza zimene zinali mʼkati mwa Nyumba ya Mulungu, anatuluka nane pa chipata chakummawa ndi kuyeza bwalo lonse.
16 Using the measuring rod he measured the east side. It was five hundred cubits long.
Anayeza mbali yakummawa ndi ndodo yake yoyezera; kutalika kwake kunali mamita 250.
17 He measured the north side. It was five hundred cubits long.
Anayeza mbali ya kumpoto ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250.
18 He measured the south side. It was five hundred cubits long.
Munthuyo anayeza mbali yakummwera; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake.
19 And he came around and measured the west side. It was five hundred cubits long.
Kenaka anatembenukira ku mbali ya kumadzulo ndi kuyeza ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake.
20 So he measured all four sides. There was a wall surrounding it, five hundred cubits long and five hundred cubits wide, separating the holy from the common.
Motero anayeza mbali zonse zinayi. Panali khoma lozungulira bwalolo mulitali mwake munali mamita 250 ndipo mulifupi mwake munalinso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba.

< Ezekiel 42 >