< Jeremiah 23 >

1 Woe unto the shepherds that destroy and scatter the sheep of my pasture! saith Jehovah.
“Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova.
2 Therefore thus saith Jehovah the God of Israel concerning the shepherds that feed my people: Ye have scattered my flock, and driven them away, and have not visited them: behold, I will visit upon you the evil of your doings, saith Jehovah.
Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova.
3 And I will gather the remnant of my flock out of all countries whither I have driven them, and will bring them again to their pastures; and they shall be fruitful and shall multiply.
“Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana.
4 And I will raise up shepherds over them, who shall feed them; and they shall fear no more, nor be dismayed, neither shall any be missing, saith Jehovah.
Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
5 Behold, the days come, saith Jehovah, when I will raise unto David a righteous Branch, who shall reign as king, and act wisely, and shall execute judgment and righteousness in the land.
Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
6 In his days Judah shall be saved, and Israel shall dwell in safety; and this is his name whereby he shall be called, Jehovah our Righteousness.
Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka ndipo Israeli adzakhala pamtendere. Dzina limene adzamutcha ndi ili: Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
7 Therefore behold, days are coming, saith Jehovah, that they shall no more say, [As] Jehovah liveth, who brought up the children of Israel out of the land of Egypt;
Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’
8 but, [As] Jehovah liveth, who brought up and who led back the seed of the house of Israel out of the north country, and from all countries whither I had driven them. And they shall dwell in their own land.
koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
9 Concerning the prophets: My heart within me is broken; all my bones shake; I am like a drunken man, and like a man whom wine hath overcome; because of Jehovah, and because of the words of his holiness.
Kunena za aneneri awa: Mtima wanga wasweka; mʼnkhongono mwati zii. Ndakhala ngati munthu woledzera, ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo, chifukwa cha Yehova ndi mawu ake opatulika.
10 For the land is full of adulterers; for because of execration the land mourneth. The pastures of the wilderness are dried up; for their course is evil, and their force is not right.
Dziko ladzaza ndi anthu achigololo; lili pansi pa matemberero. Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma. Aneneri akuchita zoyipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
11 For both prophet and priest are profane: even in my house have I found their wickedness, saith Jehovah.
“Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova. Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,” akutero Yehova.
12 Therefore their way shall be unto them as slippery places in the darkness; they shall be driven on, and fall therein: for I will bring evil upon them in the year of their visitation, saith Jehovah.
“Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera; adzawapirikitsira ku mdima ndipo adzagwera kumeneko. Adzaona zosaona mʼnthawi ya chilango chawo,” akutero Yehova.
13 And I have seen folly in the prophets of Samaria: they prophesied by Baal, and caused my people Israel to err.
“Pakati pa aneneri a ku Samariya ndinaona chonyansa ichi: Ankanenera mʼdzina la Baala ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
14 And in the prophets of Jerusalem have I seen a horrible thing: they commit adultery, and walk in falsehood, and strengthen the hands of evildoers, so that none doth return from his wickedness. They are all become unto me as Sodom, and the inhabitants thereof as Gomorrah.
Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu ndaonapo chinthu choopsa kwambiri: amachita chigololo, amanena bodza ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa. Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake. Kwa Ine anthu onsewa ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
15 Therefore thus saith Jehovah of hosts concerning the prophets: Behold, I will feed them with wormwood, and make them drink water of gall; for from the prophets of Jerusalem is profaneness gone forth into all the land.
Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawadyetsa zakudya zowawa ndi kuwamwetsa madzi a ndulu, chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
16 Thus saith Jehovah of hosts: Hearken not unto the words of the prophets that prophesy unto you: they lead you to vanity; they speak a vision of their own heart, not out of the mouth of Jehovah.
Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu; zomwe aloserazo nʼzachabechabe. Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi, osati zochokera kwa Yehova.
17 They say constantly unto them that despise me, Jehovah hath said, Ye shall have peace. And they say unto every one that walketh in the stubbornness of his heart, No evil shall come upon you.
Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti, ‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’ Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti, ‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’”
18 For who hath stood in the council of Jehovah, so that he hath perceived and heard his word? who hath hearkened to his word and listened?
Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova? Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake? Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
19 Behold, a tempest of Jehovah, fury is gone forth, yea, a whirling storm: it shall whirl down upon the head of the wicked.
Taonani ukali wa Yehova uli ngati chimphepo chamkuntho, inde ngati namondwe. Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
20 The anger of Jehovah shall not return, until he have executed, and until he have performed the purposes of his heart: at the end of the days ye shall understand it clearly.
Mkwiyo wa Yehova sudzaleka mpaka atachita zonse zimene anatsimikiza mu mtima mwake. Mudzazizindikira bwino zimenezi masiku akubwerawa.”
21 I did not send the prophets, yet they ran; I have not spoken to them, yet they prophesied.
Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa, komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo; Ine sindinawayankhule, komabe iwo ananenera.
22 But if they had stood in my council, and had caused my people to hear my words, then would they have turned them from their evil way and from the wickedness of their doings.
Iwo akanakhala pa msonkhano wanga ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga. Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa kuti aleke machimo awo.”
23 Am I a God at hand, saith Jehovah, and not a God afar off?
Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, ndiye sindine Mulungu?
24 Can any hide himself in secret places, that I shall not see him? saith Jehovah. Do not I fill the heavens and the earth? saith Jehovah.
Kodi wina angathe kubisala Ine osamuona?” “Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?” Akutero Yehova.
25 I have heard what the prophets say, who prophesy falsehood in my name, saying, I have dreamed, I have dreamed.
“Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’
26 How long shall [this] be in the heart of the prophets who prophesy falsehood, and who are prophets of the deceit of their own heart?
Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo.
27 who think to cause my people to forget my name by their dreams which they tell every man to his neighbour: as their fathers have forgotten my name for Baal.
Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala.
28 The prophet that hath a dream, let him tell the dream; and he that hath my word, let him speak my word faithfully. What is the chaff to the wheat? saith Jehovah.
Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga?
29 Is not my word like a fire, saith Jehovah; and like a hammer [that] breaketh the rock in pieces?
Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
30 Therefore, behold, I am against the prophets, saith Jehovah, that steal my words every one from his neighbour.
Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.”
31 Behold, I am against the prophets, saith Jehovah, that use their tongues, and say, He hath said.
Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’”
32 Behold, I am against them that prophesy false dreams, saith Jehovah, and that tell them, and cause my people to err by their lies and by their boasting; and I have not sent them, nor commanded them; and they profit not this people at all, saith Jehovah.
Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
33 And when this people, or a prophet, or a priest, ask thee, saying, What is the burden of Jehovah? thou shalt then say unto them, What burden? I will even cast you off, saith Jehovah.
Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’
34 And as for the prophet, and the priest, and the people, that shall say, The burden of Jehovah, I will even punish that man and his house.
Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake.
35 Thus shall ye say every one to his neighbour, and every one to his brother: What hath Jehovah answered? and, What hath Jehovah spoken?
Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’
36 And the burden of Jehovah shall ye mention no more; for every man's own word shall be his burden: for ye have perverted the words of the living God, of Jehovah of hosts, our God.
Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu.
37 Thus shalt thou say to the prophet: What hath Jehovah answered thee? and, What hath Jehovah spoken?
Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’
38 But since ye say, The burden of Jehovah, therefore thus saith Jehovah: Because ye say this word, The burden of Jehovah, and I have sent unto you, saying, Ye shall not say, The burden of Jehovah;
Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule,
39 therefore behold, I will utterly forget you, and I will cast you off, far from my face, and the city that I gave to you and to your fathers.
ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu.
40 And I will bring everlasting reproach upon you, and everlasting shame, that shall not be forgotten.
Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’”

< Jeremiah 23 >