< Isaiah 30 >

1 Woe to the rebellious children, saith Jehovah, who take counsel, but not of me, and who make leagues, but not by my Spirit, that they may heap sin upon sin;
Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira amene amachita zowakomera iwo okha osati Ine, nachita mgwirizano wawowawo koma osati motsogozedwa ndi Ine. Choncho amanka nachimwirachimwira.
2 who walk to go down into Egypt, and have not asked of my mouth, — to take refuge under the protection of Pharaoh, and trust in the shadow of Egypt!
Amapita ku Igupto kukapempha thandizo koma osandifunsa; amathawira kwa Farao kuti awateteze, ku Igupto amafuna malo opulumulira.
3 For to you the protection of Pharaoh shall be a shame, and the trust in the shadow of Egypt a confusion.
Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu, malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi.
4 For his princes were at Zoan, and his ambassadors came to Hanes.
Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani, ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,
5 They were all ashamed of a people [that] did not profit them, nor were a help or profit, but a shame, and also a reproach.
aliyense wa ku Yuda adzachita manyazi chifukwa cha anthu opanda nawo phindu, amene sabweretsa thandizo kapena phindu, koma manyazi ndi mnyozo.”
6 — The burden of the beasts of the south: Through a land of trouble and anguish, whence come the lioness and lion, the viper and fiery flying serpent, they carry their riches upon the shoulders of asses, and their treasures upon the bunches of camels, to the people that shall not profit [them].
Uthenga wonena za nyama za ku Negevi: Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa, mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi, mphiri ndi njoka zaululu. Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo, kupita nazo kwa mtundu wa anthu umene sungawathandize.
7 For Egypt shall help in vain, and to no purpose; therefore have I named her, Arrogance, that doeth nothing.
Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe. Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitcha Rahabe chirombo cholobodoka.
8 Now go, write it before them on a tablet, and record it in a book, that it may be for the time to come, as a witness for ever,
Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita, ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha masiku a mʼtsogolo.
9 that this is a rebellious people, lying children, children that will not hear the law of Jehovah;
Amenewa ndi anthu owukira, onama ndi osafuna kumvera malangizo a Yehova.
10 who say to the seers, See not; and to the prophets, Prophesy not unto us right things; speak unto us smooth things, prophesy deceits;
Iwo amawuza alosi kuti, ‘Musationerenso masomphenya!’ Ndipo amanena kwa mneneri kuti, ‘Musatinenerenso zoona,’ mutiwuze zotikomera, munenere za mʼmutu mwanu.
11 get you out of the way, turn aside out of the path, cause the Holy One of Israel to cease from before us!
Patukani pa njira ya Yehova, lekani kutsata njira ya Yehova; ndipo tisamvenso mawu a Woyerayo uja wa Israeli!”
12 Therefore thus saith the Holy One of Israel: Because ye reject this word, and confide in oppression and wilfulness, and depend thereon,
Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti, “Popeza inu mwakana uthenga uwu, mumakhulupirira zopondereza anzanu ndipo mumadalira kuchita zoyipa,
13 therefore this iniquity shall be to you as a breach ready to fall, swelling out in a towering wall, whose breaking shall come suddenly in an instant.
choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu pa khoma lalitali ndi lopendama limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.
14 And he shall break it as the breaking of a potter's vessel, that is broken in pieces unsparingly; and in the pieces of it there shall not be found a sherd to take fire from the hearth, or to scoop water out of the cistern.
Lidzaphwanyika ngati mbiya imene yanyenyekeratu, mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhale lopalira moto mʼngʼanjo kapena lotungira madzi mʼchitsime.”
15 For thus saith the Lord Jehovah, the Holy One of Israel: In returning and rest shall ye be saved, in quietness and confidence shall be your strength; but ye would not.
Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi: “Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka, ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu, koma inu munakana zimenezi.
16 And ye said, No, but we will flee upon horses, — therefore shall ye flee; and, We will ride upon the swift, — therefore shall they that pursue you be swift.
Inu mukuti, ‘Ayi ife tidzathawa, tidzakwera pa akavalo aliwiro.’ Zoonadi kuti mudzakwera pa akavalo aliwiro, koma okuthamangitsani adzakhalanso aliwiro.
17 One thousand [shall flee] at the rebuke of one; at the rebuke of five shall ye flee: till ye be left as a beacon upon the top of a mountain, and as a banner on a hill.
Anthu 1,000 mwa inu adzathawa poona mdani mmodzi; poona adani asanu okha nonsenu mudzathawa. Otsala anu adzakhala ngati mbendera pa phiri, ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.”
18 And therefore will Jehovah wait, that he may be gracious unto you, and therefore will he lift himself up, that he may have mercy upon you; for Jehovah is a God of judgment: blessed are all they that wait for him.
Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima, iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo. Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
19 For the people shall dwell in Zion, at Jerusalem. Thou shalt weep no more; he will be very gracious unto thee at the voice of thy cry; as he heareth it, he will answer thee.
Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani.
20 And the Lord will give you the bread of adversity, and the water of oppression; yet thy teachers shall not be hidden any more, but thine eyes shall see thy teachers.
Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo.
21 And when ye turn to the right hand or when ye turn to the left, thine ears shall hear a word behind thee, saying, This is the way, walk ye in it.
Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.”
22 And ye shall defile the silver covering of your graven images, and the gold overlaying of your molten images; thou shalt cast them away as a menstruous cloth: Out! shalt thou say unto it.
Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”
23 And he will give the rain of thy seed with which thou shalt sow the ground; and bread, the produce of the ground, and it shall be fat and rich. In that day shall thy cattle feed in large pastures;
Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka.
24 and the oxen and the asses that till the ground shall eat salted provender, which hath been winnowed with the shovel and with the fan.
Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo.
25 And there shall be upon every high mountain and upon every hill that is lifted up, brooks [and] water-courses, in the day of the great slaughter, when the towers fall.
Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono.
26 And the light of the moon shall be as the light of the sun, and the light of the sun shall be sevenfold, as the light of seven days, in the day that Jehovah bindeth up the breach of his people, and healeth the wound of their stroke.
Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.
27 Behold, the name of Jehovah cometh from far, burning [with] his anger — a grievous conflagration; his lips are full of indignation, and his tongue as a consuming fire;
Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali, ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka. Iye wayankhula mwaukali kwambiri, ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
28 and his breath as an overflowing torrent, which reacheth even to the neck, to sift the nations with the sieve of destruction, and [to put] a bridle into the jaws of the peoples, that causeth them to go astray.
Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira, wa madzi ofika mʼkhosi. Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza; Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo, kuti ziwasocheretse.
29 Ye shall have a song, as in the night when a feast is sanctified; and joy of heart, as of one who goeth with a pipe to come unto the mountain of Jehovah, to the Rock of Israel.
Ndipo inu mudzayimba mokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu oyimba zitoliro popita ku phiri la Yehova, thanthwe la Israeli.
30 And Jehovah will cause the majesty of his voice to be heard, and will shew the lighting down of his arm with indignation of anger, and a flame of consuming fire, with waterflood and storm and hailstones.
Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehova ndipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwo ndi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa, mphenzi, namondwe ndi matalala.
31 For through the voice of Jehovah shall the Assyrian be broken down: he will smite [him] with the rod.
Asiriya adzaopa liwu la Yehova, ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo.
32 And wherever shall pass the appointed staff, which Jehovah shall lay upon him, it shall be with tambours and harps; and with tumultuous battles will he fight with it.
Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo, anthu ake adzakhala akuvina nyimbo zoyimbira matambolini ndi azeze, Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo.
33 For Topheth is prepared of old; for the king also it is prepared: he hath made it deep and large; its pile is fire and much wood; the breath of Jehovah, like a stream of brimstone, doth kindle it.
Malo otenthera zinthu akonzedwa kale; anakonzera mfumu ya ku Asiriya. Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu, ndipo muli nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova, wangati mtsinje wa sulufule, udzayatsa motowo pa nkhunizo.

< Isaiah 30 >