< Deuteronomy 31 >

1 And so, Moses went out, and he spoke all these words to all of Israel.
Tsono Mose anapita ndi kukayankhula mawu awa kwa Aisraeli onse:
2 And he said to them: “Today, I am one hundred and twenty years old. I am no longer able to go out and return, especially since the Lord has also said to me, ‘You shall not cross this Jordan.’
“Tsopano ndili ndi zaka 120, ndipo sindingathenso kukutsogolerani. Yehova wandiwuza kuti, ‘Iwe sudzawoloka Yorodani.’
3 Therefore, the Lord your God will go across before you. He himself will abolish all these nations in your sight, and you shall possess them. And this man Joshua shall go across before you, just as the Lord has spoken.
Mwini wake Yehova Mulungu wanu ndiye amene adzakutsogolerani powoloka. Iye adzawononga mitundu ina yonse, ndipo inu mudzatenga dziko lawo. Yoswa adzakutsogoleraninso powoloka, monga momwe ananenera Yehova.
4 And the Lord will do to them just as he did to Sihon and Og, the kings of the Amorites, and to their land, and he will wipe them away.
Ndipo Yehova adzawawononga iwo monga momwe anawonongera Sihoni ndi Ogi, mafumu Aamori, amene Iye anawawononga pamodzi ndi dziko lawo.
5 Therefore, when the Lord will have delivered these to you also, you shall act similarly toward them, just as I have instructed you.
Ambuye adzawapereka kwa inu, ndipo inu mukawachitire zonse zimene ndakulamulani.
6 Act manfully and be strengthened. Do not be afraid, and do not dread at the sight of them. For the Lord your God himself is your commander, and he will neither dismiss nor abandon you.”
Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite nawo mantha kapena kunjenjemera pamaso pawo, chifukwa Yehova Mulungu wanu apita nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani.”
7 And Moses called Joshua, and, before all of Israel, he said to him: ‘Be strong and valiant. For you shall lead this people into the land which the Lord swore that he would give to their fathers, and you shall divide it by lot.
Pamenepo Yehova anayitana Yoswa pamaso pa Aisraeli onse ndipo anamuwuza kuti, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima, pakuti iwe udzatsogolera anthu awa ku dziko limene Yehova analumbira kulipereka kwa makolo awo, ndipo iwe ukaligawe pakati pawo kuti likakhale cholowa chawo.
8 And the Lord, who is your commander, will himself be with you. He will neither renounce nor abandon you. Do not be afraid, and do not dread.”
Yehova mwini ndiye akukutsogolerani ndipo adzakhala nanu. Sadzakusiyani kapena kukutayani. Usachite mantha ndiponso usataye mtima.”
9 And so, Moses wrote this law, and he handed it to the priests, the sons of Levi, who carried the ark of the covenant of the Lord, and to all the elders of Israel.
Choncho Mose analemba malamulo awa nawapereka kwa ansembe, ana Alevi, amene amanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, ndiponso kwa akuluakulu onse a Aisraeli.
10 And he instructed them, saying: “After seven years, in the year of remission, at the solemnity of the Feast of Tabernacles,
Kenaka Mose anawalamula kuti, “Pamapeto pa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, chaka cha kukhululukidwa ngongole, pa nthawi ya Chikondwerero cha Misasa,
11 when all of Israel has convened in order to appear in the sight of the Lord your God, in the place which the Lord will choose, you shall read the words of this law before all of Israel, in their hearing.
pamene Aisraeli onse abwera kudzaonekera pamaso pa Yehova Mulungu wanu pamalo pamene Iye adzasankhe, mudzawerenge malamulo onsewa iwo akumva.
12 And when the people have gathered together, men as well as women and little children, and the new arrivals who are within your gates, they shall listen so that they may learn, and may fear the Lord your God, and may keep and fulfill all the words of this law,
Mudzasonkhanitse anthu onse pamodzi, amuna, akazi ndi ana pamodzi ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu, kuti adzawamve ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamala mawu onse a mʼmalamulowa.
13 and also so that their sons, who are now ignorant, may be able to listen, and may fear the Lord their God all the days that they live in the land to which you will travel, crossing the Jordan in order to obtain it.”
Ana awo amene sadziwa malamulo awa, ayenera kuwamva ndi kuphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse pamene mukukhala mʼdziko limene mukuwoloka Yorodani kukalitenga.”
14 And the Lord said to Moses: “Behold, the days of your death draw near. Call Joshua, and stand in the tabernacle of the testimony, so that I may instruct him.” Therefore, Moses and Joshua went and stood in the tabernacle of the testimony.
Yehova anawuza Mose kuti, “Nthawi ya kufa kwako yafika. Itana Yoswa ndipo mubwere ku tenti ya msonkhano, kumene Ine ndidzamulangiza.” Choncho Mose ndi Yoswa anabwera ku tenti ya msonkhano.
15 And the Lord appeared there, in a pillar of cloud, which stood at the entrance of the tabernacle.
Pamenepo Yehova anaonekera ku tenti mʼchipilala cha mtambo, ndipo mtambowo unayima pamwamba pa khomo lolowera mu tenti.
16 And the Lord said to Moses: “Behold, you shall sleep with your fathers, and this people will rise up and will fornicate after foreign gods, in the land which they will enter so that they may live in it. In that place, they will forsake me, and they will make void the covenant that I have formed with them.
Ndipo Yehova anawuza Mose kuti, “Iwe ukupita kukapuma kumene kuli makolo ako, ndipo ukangomwalira, anthu awa adzayamba kupembedza milungu yachilendo ya mʼdziko limene akukalowamo. Adzanditaya ndi kuphwanya pangano lomwe ndinachita nawo.
17 And my fury will be enraged against them in that day. And I will abandon them, and I will hide my face from them, and they shall be devoured. Every evil and affliction will find them, so much so that they will say in that day: ‘Truly, it is because God is not with me that these evils have found me.’
Tsiku limenelo Ine ndidzawakwiyira ndi kuwataya. Ndidzawabisira nkhope yanga, ndipo adzawonongedwa. Masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, ndipo tsiku limenelo adzafunsa kuti, ‘Kodi masautso awa sanagwere ife chifukwa Yehova Mulungu wathu sali nafe?’
18 But I will hide myself, and I will conceal my face in that day, because of all the evils that they have done, because they have followed strange gods.
Ndipo Ine ndidzabisa ndithu nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoyipa zimene anachita potembenukira kwa milungu ina.
19 And so, write this canticle now, and teach it to the sons of Israel, so that they may retain it in memory, and may chant it by mouth, and so that this verse may be a testimony to me among the sons of Israel.
“Tsopano ulembe mawu a nyimbo iyi ndipo uwaphunzitse Aisraeli, uwawuze kuti aziyimba, kuti ikhale mboni yanga yowatsutsa.
20 For I will lead them into the land, about which I swore to their fathers, a land flowing with milk and honey. And when they have eaten, and have been satiated and fattened, they will turn aside to foreign gods, and they will serve them. And they will disparage me, and they will nullify my covenant.
Pamene ndawalowetsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, dziko limene ndinalonjeza mwalumbiro kwa makolo awo, ndipo pamene adzadya ndi kukhuta ndi kumasangalala, iwo adzatembenukira kwa milungu ina ndi kumayipembedza, kundikana Ine ndi kuphwanya pangano langa.
21 And after many evils and afflictions have overwhelmed them, this canticle will answer them as a testimony; it shall never pass into oblivion, away from the mouths of their offspring. For I know their thoughts and what they are about to do today, even before I lead them into the land which I have promised to them.”
Ndipo pamene masautso ambiri ndi zovuta zambiri zidzawagwera, nyimbo iyi idzakhala mboni yanga yowatsutsa, chifukwa zidzukulu zawo sizidzayiwala nyimboyi. Ine ndikudziwa zimene iwo akulingalira kuchita, ngakhale kuti sindinawalowetse mʼdziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro.”
22 Therefore, Moses wrote the canticle, and he taught it to the sons of Israel.
Choncho Mose analemba nyimbo iyi tsiku limenelo ndi kuwaphunzitsa Aisraeli.
23 And the Lord instructed Joshua, the son of Nun, and he said: “Be strong and valiant. For you shall lead the sons of Israel into the land which I have promised, and I will be with you.”
Yehova analamula Yoswa mwana wa Nuni kuti, “Khala wamphamvu ndipo limba mtima, chifukwa udzalowetsa Aisraeli mʼdziko limene ndinawalonjeza mwa lumbiro, ndipo Ine mwini ndidzakhala nawe.”
24 Therefore, after Moses had written the words of this law in a volume, and had finished it,
Mose atatha kulemba malamulowa mʼbuku, osasiyako kanthu,
25 he instructed the Levites, who carried the ark of the covenant of the Lord, saying:
analamula Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova kuti,
26 “Take this book, and place it inside the ark of the covenant of the Lord your God, so that it may be there as a testimony against you.
“Tengani Buku ili la Malamulo ndi kuliyika pambali pa Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu. Likhale kumeneko ngati mboni yokutsutsani.
27 For I know your contentiousness and your very stiff neck. Even while I am still living and entering with you, you have always acted with contention against the Lord. How much more so when I will be dead?
Pakuti Ine ndikudziwa kuwukira kwanu ndi kuwuma mtima kwanu. Ngati inu mwakhala mukuwukira Yehova ine ndili moyo ndiponso ndili nanu pamodzi, nanga mudzawukira motani ine ndikamwalira!
28 Gather to me all those greater by birth throughout your tribes, as well as your teachers, and I will speak these words in their hearing, and I will call heaven and earth as witnesses against them.
Mundisonkhanitsire atsogoleri onse a mafuko anu pamodzi ndi akuluakulu onse, kuti ndiyankhule mawu awa iwo akumva ndipo kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni yowatsutsa.
29 For I know that, after my death, you will act with iniquity, and you will quickly depart from the way that I have instructed to you. And so, evils will meet you in the end time, when you will have done evil in the sight of the Lord so as to provoke him through the works of your hands.”
Chifukwa ndikudziwa kuti ine ndikamwalira mudzayipa kwambiri ndi kutembenuka kuleka njira imene ndinakulamulani. Masiku amene akubwera, masautso adzakugwerani chifukwa mudzachita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuputa mkwiyo wake chifukwa cha zimene manja anu anapanga.”
30 Thus did Moses speak, in the hearing of the entire assembly of Israel, the words of this canticle, and he completed it to its very end.
Ndipo Mose ananena mawu a nyimbo iyi kuyiimba koyambira mpaka potsiriza gulu lonse la Aisraeli likumva:

< Deuteronomy 31 >