< James 5 >

1 Come now, you men of wealth, give yourselves to weeping and crying because of the bitter troubles which are coming to you.
Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni.
2 Your wealth is unclean and insects have made holes in your clothing.
Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu.
3 Your gold and your silver are wasted and their waste will be a witness against you, burning into your flesh. You have put by your store in the last days.
Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza.
4 See, the money which you falsely kept back from the workers cutting the grass in your field, is crying out against you; and the cries of those who took in your grain have come to the ears of the Lord of armies.
Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse.
5 You have been living delicately on earth and have taken your pleasure; you have made your hearts fat for a day of destruction.
Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa.
6 You have given your decision against the upright man and have put him to death. He puts up no fight against you.
Mwaweruza kuti ndi wolakwa ndipo mwapha munthu wosalakwa, amene sakutsutsana nanu.
7 Go on waiting calmly, my brothers, till the coming of the Lord, like the farmer waiting for the good fruit of the earth till the early and late rains have come.
Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza.
8 Be as calm in your waiting; let your hearts be strong: because the coming of the Lord is near.
Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera.
9 Say no hard things against one another, brothers, so that you will not be judged; see, the judge is waiting at the doors.
Abale, musamanenezane zoyipa kuopa kuti mungadzaweruzidwe. Woweruza ali pa khomo!
10 Take as an example of pain nobly undergone and of strength in trouble, the prophets who gave to men the words of the Lord.
Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira.
11 We say that those men who have gone through pain are happy: you have the story of Job and the troubles through which he went and have seen that the Lord was full of pity and mercy in the end.
Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.
12 But most of all, my brothers, do not take oaths, not by the heaven, or by the earth, or by any other thing: but let your Yes be Yes, and your No be No: so that you may not be judged.
Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.
13 Is anyone among you in trouble? let him say prayers. Is anyone glad? let him make a song of praise.
Kodi alipo wina mwa inu amene ali pa mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Ayimbe nyimbo zolemekeza.
14 Is anyone among you ill? let him send for the rulers of the church; and let them say prayers over him, putting oil on him in the name of the Lord.
Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye.
15 And by the prayer of faith the man who is ill will be made well, and he will be lifted up by the Lord, and for any sin which he has done he will have forgiveness.
Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa.
16 So then, make a statement of your sins to one another, and say prayers for one another so that you may be made well. The prayer of a good man is full of power in its working.
Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.
17 Elijah was a man of flesh and blood as we are, and he made a strong prayer that there might be no rain; and there was no rain on the earth for three years and six months.
Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka.
18 And he made another prayer, and the heaven sent down rain and the earth gave her fruit.
Kenaka anapempheranso, ndipo kumwamba kunagwetsa mvula, ndipo dziko lapansi linatulutsa zomera zake.
19 My brothers, if one of you has gone out of the way of the true faith and another has made him see his error,
Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza,
20 Be certain that he through whom a sinner has been turned from the error of his way, keeps a soul from death and is the cause of forgiveness for sins without number.
kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.

< James 5 >