< Nehemiah 12 >

1 Now these are the priests and the Levites that went up with Zerubbabel the son of Shealtiel, and Jeshua: Seraiah, Jeremiah, Ezra,
Ansembe ndi Alevi amene anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa anali awa: Seraya, Yeremiya, Ezara,
2 Amariah, Malluch, Hattush,
Amariya, Maluki, Hatusi,
3 Shecaniah, Rehum, Meremoth,
Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
4 Iddo, Ginnethoi, Abijah,
Ido, Ginetoyi, Abiya
5 Mijamin, Maadiah, Bilgah,
Miyamini, Maadiya, Biliga,
6 Shemaiah, and Joiarib, Jedaiah.
Semaya, Yowaribu, Yedaya,
7 Sallu, Amok, Hilkiah, Jedaiah. These were the chiefs of the priests and of their brethren in the days of Jeshua.
Salu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya. Awa ndiye anali atsogoleri a ansembe ndi abale awo pa nthawi ya Yesuwa.
8 Moreover the Levites: Jeshua, Binnui, Kadmiel, Sherebiah, Judah, [and] Mattaniah, who was over the thanksgiving, he and his brethren.
Alevi anali Yesuwa, Binuyi, Kadimieli, Serebiya, Yuda, ndiponso Mataniya, amene pamodzi ndi abale ake ankatsogolera nyimbo za mayamiko.
9 Also Bakbukiah and Unno, their brethren, were over against them according to their offices.
Abale awo, Bakibukiya ndi Uri, ankayimba nyimbo molandizana.
10 And Jeshua begat Joiakim, and Joiakim begat Eliashib, and Eliashib begat Joiada,
Yesuwa anabereka Yowakimu, Yowakimu anabereka Eliyasibu, Eliyasibu anabereka Yoyada.
11 and Joiada begat Jonathan, and Jonathan begat Jaddua.
Yoyada anabereka Yonatani, ndipo Yonatani anabereka Yaduwa.
12 And in the days of Joiakim were priests, heads of fathers’ [houses]: of Seraiah, Meraiah; of Jeremiah, Hananiah;
Pa nthawi ya Yowakimu, awa ndiwo anali atsogoleri a mabanja a ansembe: Mtsogoleri wa fuko la Seraya anali Meraya; wa fuko la Yeremiya anali Hananiya;
13 of Ezra, Meshullam; of Amariah, Jehohanan;
wa fuko la Ezara anali Mesulamu; wa fuko la Amariya anali Yehohanani;
14 of Malluchi, Jonathan; of Shebaniah, Joseph;
wa fuko la Maluki anali Yonatani; wa fuko la Sebaniya anali Yosefe;
15 of Harim, Adna; of Meraioth, Helkai;
wa fuko la Harimu anali Adina; wa fuko la Merayoti anali Helikayi;
16 of Iddo, Zechariah; of Ginnethon, Meshullam;
wa fuko la Ido anali Zekariya; wa fuko la Ginetoni anali Mesulamu;
17 of Abijah, Zichri; of Miniamin, of Moadiah, Piltai;
wa fuko la Abiya anali Zikiri; wa fuko la Miniyamini ndi banja la Maadiya anali Pilitayi;
18 of Bilgah, Shammua; of Shemaiah, Jehonathan;
wa fuko la Biliga anali Samuwa; wa fuko la Semaya anali Yonatani;
19 and of Joiarib, Mattenai; of Jedaiah, Uzzi;
wa fuko la Yowaribu anali Matenayi; wa fuko la Yedaya anali Uzi;
20 of Sallai, Kallai; of Amok, Eber;
wa fuko la Salai anali Kalai; wa fuko la Amoki anali Eberi;
21 of Hilkiah, Hashabiah; of Jedaiah, Nethanel.
wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya; wa fuko la Yedaya anali Netaneli.
22 As for the Levites, in the days of Eliashib, Joiada, and Johanan, and Jaddua, there were recorded the heads of fathers’ [houses]; also the priests, in the reign of Darius the Persian.
Pa nthawi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa panalembedwa atsogolera a mabanja a Alevi ndi a ansembe mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo Mperisi.
23 The sons of Levi, heads of fathers’ [houses], were written in the book of the chronicles, even until the days of Johanan the son of Eliashib.
Zidzukulu za Levi, makamaka atsogoleri a mabanja awo analembedwa mʼbuku la mbiri mpaka pa nthawi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu.
24 And the chiefs of the Levites: Hashabiah, Sherebiah, and Jeshua the son of Kadmiel, with their brethren over against them, to praise and give thanks, according to the commandment of David the man of God, watch next to watch.
Ndipo atsogoleri a Alevi awa, Hasabiya, Serebiya, Yesuwa mwana wa Kadimieli ndi abale awo, ankayimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza molandizana. Gulu limodzi linkavomerezana ndi linzake monga mmene Davide munthu wa Mulungu analamulira.
25 Mattaniah, and Bakbukiah, Obadiah, Meshullam, Talmon, Akkub, were porters keeping the watch at the store-houses of the gates.
Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu.
26 These were in the days of Joiakim the son of Jeshua, the son of Jozadak, and in the days of Nehemiah the governor, and of Ezra the priest the scribe.
Iwo ndiwo ankatumikira pa nthawi ya Yowakimu mwana wa Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthawi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso mlembi.
27 And at the dedication of the wall of Jerusalem they sought the Levites out of all their places, to bring them to Jerusalem, to keep the dedication with gladness, both with thanksgivings, and with singing, with cymbals, psalteries, and with harps.
Pa mwambo wopereka khoma la Yerusalemu anayitana Alevi kulikonse kumene ankakhala kuti abwere ku Yerusalemu ku mwambo wopereka khoma kwa Mulungu, mwachimwemwe ndi mothokoza poyimba nyimbo pamodzi ndi ziwiya za malipenga, azeze ndi apangwe.
28 And the sons of the singers gathered themselves together, both out of the plain round about Jerusalem, and from the villages of the Netophathites;
Tsono anthu a mabanja a Alevi oyimba nyimbo aja anasonkhana pamodzi kuchokera ku madera onse ozungulira Yerusalemu ndiponso ku midzi ya Anetofati,
29 also from Beth-gilgal, and out of the fields of Geba and Azmaveth: for the singers had builded them villages round about Jerusalem.
Beti-Giligala ndi ku madera a ku Geba ndi Azimaveti, pakuti oyimbawo anali atamanga midzi yawo mozungulira Yerusalemu.
30 And the priests and the Levites purified themselves; and they purified the people, and the gates, and the wall.
Tsono ansembe ndi Alevi anachita mwambo wodziyeretsa. Pambuyo pake anachita mwambo woyeretsa anthu onse ndi khoma la Yerusalemu.
31 Then I brought up the princes of Judah upon the wall, and appointed two great companies that gave thanks and went in procession; [whereof one went] on the right hand upon the wall toward the dung gate:
Ine ndinabwera nawo atsogoleri a dziko la Yuda ndi kukwera nawo pa khoma. Ndipo ndinasankha magulu awiri akuluakulu oyimba nyimbo za matamando. Gulu limodzi linadzera mbali ya ku dzanja lamanja pa khoma mpaka ku Chipata cha Kudzala.
32 and after them went Hoshaiah, and half of the princes of Judah,
Pambuyo pawo panali Hosayia, theka la atsogoleri a Yuda aja
33 and Azariah, Ezra, and Meshullam,
pamodzi ndi Azariya, Ezara, Mesulamu,
34 Judah, and Benjamin, and Shemaiah, and Jeremiah,
Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya.
35 and certain of the priests’ sons with trumpets: Zechariah the son of Jonathan, the son of Shemaiah, the son of Mattaniah, the son of Micaiah, the son of Zaccur, the son of Asaph;
Ena mwa ana a ansembe amene ankayimba malipenga awo anali awa: Zekariya mwana wa Yonatani mwana wa Semaya mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,
36 and his brethren, Shemaiah, and Azarel, Milalai, Gilalai, Maai, Nethanel, and Judah, Hanani, with the musical instruments of David the man of God; and Ezra the scribe was before them.
pamodzi ndi abale awo awa: Semaya, Azareli, Milalai, Gilalayi, Maayi, Netaneli, Yuda ndi Hanani. Onse ankagwiritsa ntchito zida zoyimbira za Davide, munthu wa Mulungu. Tsono Ezara mlembi uja ankawatsogolera.
37 And by the fountain gate, and straight before them, they went up by the stairs of the city of David, at the ascent of the wall, above the house of David, even unto the water gate eastward.
Kuchokera ku Chipata cha Kasupe anayenda nakakwera makwerero opita ku mzinda wa Davide pa njira yotsatira khoma, chakumtundu kwa nyumba ya Davide mpaka ku Chipata cha Madzi, mbali ya kummawa.
38 And the other company of them that gave thanks went to meet them, and I after them, with the half of the people, upon the wall, above the tower of the furnaces, even unto the broad wall,
Gulu loyimba lachiwiri linadzera mbali ya kumanzere kwa khomalo. Tsono ine ndi theka lina la atsogoleri aja tinkalitsata pambuyo tikuyenda pamwamba pa khomalo. Tinapitirira Nsanja ya Ngʼanjo mpaka ku Khoma Lotambasuka.
39 and above the gate of Ephraim, and by the old gate, and by the fish gate, and the tower of Hananel, and the tower of Hammeah, even unto the sheep gate: and they stood still in the gate of the guard.
Tinadutsanso Chipata cha Efereimu, Chipata cha Yesana, Chipata cha Nsomba, Nsanja ya Hananeli, Nsanja ya Zana mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo mdipiti uwu unakayima pa Chipata cha Mlonda.
40 So stood the two companies of them that gave thanks in the house of God, and I, and the half of the rulers with me;
Choncho magulu onse awiri oyimba nyimbo zothokoza aja anakayima pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la atsogoleri aja,
41 and the priests, Eliakim, Maaseiah, Miniamin, Micaiah, Elioenai, Zechariah, and Hananiah, with trumpets;
panalinso ansembe awa akuyimba malipenga: Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya.
42 and Maaseiah, and Shemaiah, and Eleazar, and Uzzi, and Jehohanan, and Malchijah, and Elam, and Ezer. And the singers sang loud, with Jezrahiah their overseer.
Panalinso ansembe awa: Maaseya, Semaya, Eliezara, Uzi, Yehohanani, Milikiya, Elamu ndi Ezeri. Gulu loyimba linkatsogozedwa ndi Yezirahayiya.
43 And they offered great sacrifices that day, and rejoiced; for God had made them rejoice with great joy; and the women also and the children rejoiced: so that the joy of Jerusalem was heard even afar off.
Pa tsiku limenelo anthu anapereka nsembe zambiri ndipo anakondwera chifukwa Mulungu anawapatsa chimwemwe chachikulu. Nawonso akazi ndi ana anakondwera ndipo kukondwa kwa anthu a mu mzinda wa Yerusalemu kunamveka kutali.
44 And on that day were men appointed over the chambers for the treasures, for the heave-offerings, for the first-fruits, and for the tithes, to gather into them, according to the fields of the cities, the portions appointed by the law for the priests and Levites: for Judah rejoiced for the priests and for the Levites that waited.
Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi.
45 And they kept the charge of their God, and the charge of the purification, and [so did] the singers and the porters, according to the commandment of David, and of Solomon his son.
Iwowa ankagwira ntchito ya Mulungu wawo, makamaka mwambo woyeretsa zinthu. Nawonso oyimba nyimbo ndi olonda ku Nyumba ya Mulungu anagwira ntchito zawo monga Davide ndi mwana wake Solomoni analamula.
46 For in the days of David and Asaph of old there was a chief of the singers, and songs of praise and thanksgiving unto God.
Pakuti kalekale, pa nthawi ya Davide ndi Asafu, panali atsogoleri a anthu oyimba nyimbo za matamando ndi nyimbo zoyamika Mulungu.
47 And all Israel in the days of Zerubbabel, and in the days of Nehemiah, gave the portions of the singers and the porters, as every day required: and they set apart [that which was] for the Levites; and the Levites set apart [that which was] for the sons of Aaron.
Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni.

< Nehemiah 12 >