< 彌迦書 6 >

1 以色列人哪,當聽耶和華的話! 要起來向山嶺爭辯, 使岡陵聽你的話。
Tamverani zimene Yehova akunena: “Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri; zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.
2 山嶺和地永久的根基啊, 要聽耶和華爭辯的話! 因為耶和華要與他的百姓爭辯, 與以色列爭論。
Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri; tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi. Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake; Iye akutsutsa Aisraeli.
3 我的百姓啊,我向你做了甚麼呢? 我在甚麼事上使你厭煩? 你可以對我證明。
“Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani? Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.
4 我曾將你從埃及地領出來, 從作奴僕之家救贖你; 我也差遣摩西、亞倫,和米利暗在你前面行。
Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.
5 我的百姓啊,你們當追念摩押王巴勒所設的謀 和比珥的兒子巴蘭回答他的話, 並你們從什亭到吉甲所遇見的事, 好使你們知道耶和華公義的作為。
Anthu anga, kumbukirani zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha. Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala, kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”
6 我朝見耶和華, 在至高上帝面前跪拜,當獻上甚麼呢? 豈可獻一歲的牛犢為燔祭嗎?
Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba? Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza, ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?
7 耶和華豈喜悅千千的公羊, 或是萬萬的油河嗎? 我豈可為自己的罪過獻我的長子嗎? 為心中的罪惡獻我身所生的嗎?
Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000, kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta? Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga? Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?
8 世人哪,耶和華已指示你何為善。 他向你所要的是甚麼呢? 只要你行公義,好憐憫, 存謙卑的心,與你的上帝同行。
Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
9 耶和華向這城呼叫, 智慧人必敬畏他的名。 你們當聽是誰派定刑杖的懲罰。
Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda ndi nzeru kuopa dzina lanu. “Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa.
10 惡人家中不仍有非義之財 和可惡的小升斗嗎?
Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?
11 我若用不公道的天平和囊中詭詐的法碼, 豈可算為清潔呢?
Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake?
12 城裏的富戶滿行強暴; 其中的居民也說謊言, 口中的舌頭是詭詐的。
Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.
13 因此,我擊打你, 使你的傷痕甚重, 使你因你的罪惡荒涼。
Choncho, ndayamba kukuwonongani, kukusakazani chifukwa cha machimo anu.
14 你要吃,卻吃不飽; 你的虛弱必顯在你中間。 你必挪去,卻不得救護; 所救護的,我必交給刀劍。
Mudzadya, koma simudzakhuta; mudzakhalabe ndi njala. Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika, chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga.
15 你必撒種,卻不得收割; 踹橄欖,卻不得油抹身; 踹葡萄,卻不得酒喝。
Mudzadzala, koma simudzakolola. Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito. Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.
16 因為你守暗利的惡規, 行亞哈家一切所行的, 順從他們的計謀; 因此,我必使你荒涼, 使你的居民令人嗤笑, 你們也必擔當我民的羞辱。
Inu mwatsatira malangizo a Omuri ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu, ndi khalidwe lawo lonse. Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu; mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”

< 彌迦書 6 >