< 以賽亞書 34 >

1 列國啊,要近前來聽! 眾民哪,要側耳而聽! 地和其上所充滿的, 世界和其中一切所出的都應當聽!
Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve: tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse: Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
2 因為耶和華向萬國發忿恨, 向他們的全軍發烈怒, 將他們滅盡,交出他們受殺戮。
Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse; wapsera mtima magulu awo onse ankhondo. Iye adzawawononga kotheratu, nawapereka kuti aphedwe.
3 被殺的必然拋棄, 屍首臭氣上騰; 諸山被他們的血融化。
Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja, mitembo yawo idzawola ndi kununkha; mapiri adzafiira ndi magazi awo.
4 天上的萬象都要消沒; 天被捲起,好像書卷。 其上的萬象要殘敗, 像葡萄樹的葉子殘敗, 又像無花果樹的葉子殘敗一樣。
Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala; nyenyezi zonse zidzayoyoka ngati masamba ofota a mphesa, ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
5 因為我的刀在天上已經喝足; 這刀必臨到以東和我所咒詛的民, 要施行審判。
Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba; taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu, anthu amene ndawawononga kotheratu.”
6 耶和華的刀滿了血, 用脂油和羊羔、公山羊的血, 並公綿羊腰子的脂油滋潤的; 因為耶和華在波斯拉有獻祭的事, 在以東地大行殺戮。
Lupanga la Yehova lakhuta magazi, lakutidwa ndi mafuta; magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi, mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna. Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
7 野牛、牛犢,和公牛要一同下來。 他們的地喝醉了血; 他們的塵土因脂油肥潤。
Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati, ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe. Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha, ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.
8 因耶和華有報仇之日, 為錫安的爭辯有報應之年。
Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira ndi kulanga adani a Ziyoni.
9 以東的河水要變為石油, 塵埃要變為硫磺; 地土成為燒着的石油,
Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula, ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule; dziko lake lidzasanduka phula lamoto!
10 晝夜總不熄滅, 煙氣永遠上騰, 必世世代代成為荒廢, 永永遠遠無人經過。
Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana; utsi wake udzafuka kosalekeza. Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado; palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.
11 鵜鶘、箭豬卻要得為業; 貓頭鷹、烏鴉要住在其間。 耶和華必將空虛的準繩, 混沌的線鉈,拉在其上。
Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu; amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo. Mulungu adzatambalitsa pa Edomu chingwe choyezera cha chisokonezo ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
12 以東人要召貴冑來治國; 那裏卻無一個, 首領也都歸於無有。
Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko; akalonga ake onse adzachotsedwa.
13 以東的宮殿要長荊棘; 保障要長蒺藜和刺草; 要作野狗的住處, 鴕鳥的居所。
Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa, khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake. Ankhandwe azidzadya mʼmenemo; malo okhalamo akadzidzi.
14 曠野的走獸要和豺狼相遇; 野山羊要與伴偶對叫。 夜間的怪物必在那裏棲身, 自找安歇之處。
Avumbwe adzakumana ndi afisi, ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana. Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa ndi kupeza malo opumulirako.
15 箭蛇要在那裏做窩, 下蛋,菢蛋,生子, 聚子在其影下; 鷂鷹各與伴偶聚集在那裏。
Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira, adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake; akamtema adzasonkhananso kumeneko, awiriawiri.
16 你們要查考宣讀耶和華的書。 這都無一缺少, 無一沒有伴偶; 因為我的口已經吩咐, 他的靈將牠們聚集。
Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga: mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa; sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake. Pakuti Yehova walamula kuti zitero, ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
17 他也為牠們拈鬮, 又親手用準繩給牠們分地; 牠們必永得為業, 世世代代住在其間。
Yehova wagawa dziko lawo; wapatsa chilichonse chigawo chake. Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.

< 以賽亞書 34 >