< 歷代志下 2 >

1 所羅門定意要為耶和華的名建造殿宇,又為自己的國建造宮室。
Solomoni anatsimikiza zoti amange Nyumba ya Dzina la Yehova ndi nyumba yake yaufumu.
2 所羅門就挑選七萬扛抬的,八萬在山上鑿石頭的,三千六百督工的。
Iye analemba ntchito anthu 70,000 onyamula katundu ndi anthu 80,000 okumba miyala ku mapiri ndiponso akapitawo 3,600 oyangʼanira anthuwo.
3 所羅門差人去見泰爾王希蘭,說:「你曾運香柏木與我父大衛建宮居住,求你也這樣待我。
Solomoni anatumiza uthenga uwu kwa Hiramu mfumu ya ku Turo: “Munditumizire mitengo ya mkungudza monga munachitira ndi abambo anga pamene munawatumizira mitengo ya mkungudza yomangira nyumba yaufumu yokhalamo.
4 我要為耶和華-我上帝的名建造殿宇,分別為聖獻給他,在他面前焚燒美香,常擺陳設餅,每早晚、安息日、月朔,並耶和華-我們上帝所定的節期獻燔祭。這是以色列人永遠的定例。
Tsono ine ndikufuna kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wanga ndi kuyipereka kwa Iye kuti tiziyikamo buledi wopatulika nthawi zonse ndiponso kuperekeramo nsembe zopsereza mmawa uliwonse ndi madzulo ndi pa masabata ndi pa masiku a chikondwerero cha mwezi watsopano ndiponso pa masiku osankhika a chikondwerero cha Yehova Mulungu wathu, monga mwa malamulo a Aisraeli mpaka muyaya.
5 我所要建造的殿宇甚大;因為我們的上帝至大,超乎諸神。
“Nyumba ya Mulungu imene ndidzamange idzakhala yayikulu, chifukwa Mulungu wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.
6 天和天上的天,尚且不足他居住的,誰能為他建造殿宇呢?我是誰?能為他建造殿宇嗎?不過在他面前燒香而已。
Koma ndani angathe kumumangira Iye Nyumba, pakuti mlengalenga, ngakhale kumwamba kwenikweni sikungamukwane? Tsono ine ndine yani kuti ndimangire Iyeyo Nyumba, kupatula malo chabe opserezerapo nsembe pamaso pake?
7 現在求你差一個巧匠來,就是善用金、銀、銅、鐵,和紫色、朱紅色、藍色線,並精於雕刻之工的巧匠,與我父大衛在猶大和耶路撒冷所預備的巧匠一同做工;
“Tsono tumizireni munthu waluso pa ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, nsalu yapepo ndi yofiira ndi yobiriwira ndiponso waluso losema, kuti adzagwire ntchito mu Yuda ndi Yerusalemu pamodzi ndi anthu aluso amene abambo anga Davide anandipatsa.
8 又求你從黎巴嫩運些香柏木、松木、檀香木到我這裏來,因我知道你的僕人善於砍伐黎巴嫩的樹木。我的僕人也必與你的僕人同工。
“Munditumizirenso mitengo ya mkungudza, payini ndiponso matabwa a mʼbawa wa ku Lebanoni, pakuti ndikudziwa kuti anthu anu ali ndi luso locheka matabwa kumeneko. Antchito anga adzagwira ntchito pamodzi ndi antchito anu
9 這樣,可以給我預備許多的木料,因我要建造的殿宇高大出奇。
kuti andipatse matabwa ambiri, chifukwa Nyumba imene ndikumanga iyenera kukhala yayikulu ndi yokongola.
10 你的僕人砍伐樹木,我必給他們打好了的小麥二萬歌珥,大麥二萬歌珥,酒二萬罷特,油二萬罷特。」
Ine ndidzalipira antchito anu amene adzacheke matabwa matani 1,000 a tirigu wopunthapuntha, matani 2,000 a barele, malita 440,000 a vinyo, ndiponso malita 440,000 a mafuta a olivi.”
11 泰爾王希蘭寫信回答所羅門說:「耶和華因為愛他的子民,所以立你作他們的王」;
Hiramu, mfumu ya ku Turo, anamuyankha Solomoni pomulembera kalata kuti, “Chifukwa Yehova amakonda anthu ake, wayika iwe kukhala mfumu yawo.”
12 又說:「創造天地的耶和華-以色列的上帝是應當稱頌的!他賜給大衛王一個有智慧的兒子,使他有謀略聰明,可以為耶和華建造殿宇,又為自己的國建造宮室。
Ndipo Hiramu anawonjezera kunena kuti, “Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi! Iye wamupatsa Davide mwana wanzeru, wodzaza ndi luntha ndi wozindikira, amene adzamanga Nyumba ya Mulungu ndi kudzimangira yekha nyumba yaufumu.
13 「現在我打發一個精巧有聰明的人去,他是我父親希蘭所用的,
“Ine ndikukutumizira Hiramu Abi, munthu wa luso lalikulu,
14 是但支派一個婦人的兒子。他父親是泰爾人,他善用金、銀、銅、鐵、石、木,和紫色、藍色、朱紅色線與細麻製造各物,並精於雕刻,又能想出各樣的巧工。請你派定這人,與你的巧匠和你父-我主大衛的巧匠一同做工。
amene amayi ake anali wochokera ku Dani ndipo abambo ake anali a ku Turo. Iye anaphunzitsidwa kugwira ntchito zagolide ndi siliva, mkuwa ndi chitsulo, miyala yokongola ndi matabwa, ndiponso nsalu zofewa zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Alinso ndi luso la zosemasema ndipo atha kupanga chilichonse chimene wapatsidwa. Iye adzagwira ntchito ndi amisiri anu ndi a mbuye wanga, Davide abambo anu.
15 我主所說的小麥、大麥、酒、油,願我主運來給眾僕人。
“Tsono mbuye wanga tumizirani antchito anu tirigu ndi barele, mafuta a olivi ndi vinyo zimene mwalonjeza,
16 我們必照你所需用的,從黎巴嫩砍伐樹木,紮成筏子,浮海運到約帕;你可以從那裏運到耶路撒冷。」
ndipo ife tidzadula mitengo yonse imene mukuyifuna kuchokera ku Lebanoni ndipo tidzayimanga pamodzi ndi kuyiyadamitsa pa madzi mpaka ku Yopa. Ndipo inu mudzatha kuyitenga mpaka ku Yerusalemu.”
17 所羅門仿照他父大衛數點住在以色列地所有寄居的外邦人,共有十五萬三千六百名;
Solomoni anawerenga alendo onse amene anali mu Israeli, potsatira chiwerengero chimene abambo ake Davide anachita ndipo panapezeka kuti analipo anthu 153,600.
18 使七萬人扛抬材料,八萬人在山上鑿石頭,三千六百人督理工作。
Iye anayika anthu 70,000 kuti akhale onyamula katundu ndi anthu 80,000 kuti akhale ophwanya miyala mʼmapiri, anthu 3,600 anawayika kukhala akapitawo oyangʼanira anthu pa ntchitoyo.

< 歷代志下 2 >