< 列王紀上 15 >

1 尼八的兒子耶羅波安王十八年,亞比央登基作猶大王,
Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Nebati, Abiya anakhala mfumu ya Yuda,
2 在耶路撒冷作王三年。他母親名叫瑪迦,是押沙龍的女兒。
ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zitatu. Amayi ake anali Maaka, mwana wa Abisalomu.
3 亞比央行他父親在他以前所行的一切惡,他的心不像他祖大衛的心,誠誠實實地順服耶和華-他的上帝。
Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide.
4 然而耶和華-他的上帝因大衛的緣故,仍使他在耶路撒冷有燈光,叫他兒子接續他作王,堅立耶路撒冷。
Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu;
5 因為大衛除了赫人烏利亞那件事,都是行耶和華眼中看為正的事,一生沒有違背耶和華一切所吩咐的。
pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti.
6 羅波安在世的日子常與耶羅波安爭戰。
Panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu masiku onse a moyo wa Abiya.
7 亞比央其餘的事,凡他所行的,都寫在猶大列王記上。亞比央常與耶羅波安爭戰。
Tsono ntchito zina za Abiya, ndi zina zonse anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu.
8 亞比央與他列祖同睡,葬在大衛的城裏。他兒子亞撒接續他作王。
Ndipo Abiya anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Asa, mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
9 以色列王耶羅波安二十年,亞撒登基作猶大王,
Mʼchaka cha makumi awiri cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda,
10 在耶路撒冷作王四十一年。他祖母名叫瑪迦,是押沙龍的女兒。
ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu.
11 亞撒效法他祖大衛行耶和華眼中看為正的事,
Asa anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake.
12 從國中除去孌童,又除掉他列祖所造的一切偶像;
Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga.
13 並且貶了他祖母瑪迦太后的位,因她造了可憎的偶像亞舍拉。亞撒砍下她的偶像,燒在汲淪溪邊,
Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni.
14 只是邱壇還沒有廢去。亞撒一生卻向耶和華存誠實的心。
Ngakhale sanachotse malo opembedzerapo mafano, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova masiku onse a moyo wake.
15 亞撒將他父親所分別為聖與自己所分別為聖的金銀和器皿都奉到耶和華的殿裏。
Asa anabweretsa ku Nyumba ya Yehova zinthu zimene abambo ake anazipereka, ndiponso zinthu zimene iye mwini anazipereka: zagolide, siliva ndi ziwiya zotengera.
16 亞撒和以色列王巴沙在世的日子常常爭戰。
Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli nthawi yonse ya ulamuliro wawo.
17 以色列王巴沙上來要攻擊猶大,修築拉瑪,不許人從猶大王亞撒那裏出入。
Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda.
18 於是亞撒將耶和華殿和王宮府庫裏所剩下的金銀都交在他臣僕手中,打發他們往住大馬士革的亞蘭王-希旬的孫子、他伯利們的兒子便‧哈達那裏去,
Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti,
19 說:「你父曾與我父立約,我與你也要立約。現在我將金銀送你為禮物,求你廢掉你與以色列王巴沙所立的約,使他離開我。」
“Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.”
20 便‧哈達聽從亞撒王的話,派軍長去攻擊以色列的城邑;他們就攻破以雲、但、亞伯‧伯‧瑪迦、基尼烈全境、拿弗他利全境。
Choncho Beni-Hadadi anamvera zimene ananena mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira magulu ake ankhondo ku mizinda ya Israeli. Ndipo iye anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Beti-Maaka ndi dera lonse la Kinereti kuphatikiza dziko lonse la Nafutali.
21 巴沙聽見,就停工不修築拉瑪了,仍住在得撒。
Baasa atamva zimenezi, anasiya kumangira linga Rama ndipo anakakhala ku Tiriza.
22 於是亞撒王宣告猶大眾人,不准一個推辭,吩咐他們將巴沙修築拉瑪所用的石頭、木頭都運去,用以修築便雅憫的迦巴和米斯巴。
Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa.
23 亞撒其餘的事,凡他所行的,並他的勇力與他所建築的城邑,都寫在猶大列王記上。亞撒年老的時候,腳上有病。
Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi.
24 亞撒與他列祖同睡,葬在他祖大衛城他列祖的墳地裏。他兒子約沙法接續他作王。
Ndipo Asa anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
25 猶大王亞撒第二年,耶羅波安的兒子拿答登基作以色列王共二年,
Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri.
26 拿答行耶和華眼中看為惡的事,行他父親所行的,犯他父親使以色列人陷在罪裏的那罪。
Nadabu anachita zoyipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira za abambo ake ndi mu uchimo womwe anachimwitsa nawo Israeli.
27 以薩迦人亞希雅的兒子巴沙背叛拿答,在非利士的基比頓殺了他。那時拿答和以色列眾人正圍困基比頓。
Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira.
28 在猶大王亞撒第三年巴沙殺了他,篡了他的位。
Baasa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa, mfumu ya ku Yuda ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
29 巴沙一作王就殺了耶羅波安的全家,凡有氣息的沒有留下一個,都滅盡了,正應驗耶和華藉他僕人示羅人亞希雅所說的話。
Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo
30 這是因為耶羅波安所犯的罪使以色列人陷在罪裏,惹動耶和華-以色列上帝的怒氣。
chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli.
31 拿答其餘的事,凡他所行的,都寫在以色列諸王記上。
Tsono ntchito za Nadabu ndi zina zonse zimene anazichita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
32 亞撒和以色列王巴沙在世的日子常常爭戰。
Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli pa nthawi yonse ya ulamuliro wawo.
33 猶大王亞撒第三年,亞希雅的兒子巴沙在得撒登基作以色列眾人的王共二十四年。
Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24.
34 他行耶和華眼中看為惡的事,行耶羅波安所行的道,犯他使以色列人陷在罪裏的那罪。
Anachita zoyipa pamaso pa Yehova, nayenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchita tchimo lake limene linachimwitsa anthu a ku Israeli.

< 列王紀上 15 >