< 诗篇 140 >

1 大卫的诗,交与伶长。 耶和华啊,求你拯救我脱离凶恶的人, 保护我脱离强暴的人!
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Landitseni Yehova kwa anthu oyipa; tetezeni kwa anthu ankhanza,
2 他们心中图谋奸恶, 常常聚集要争战。
amene mu mtima mwawo amakonza zinthu zoyipa ndi kuyambitsa nkhondo tsiku lililonse.
3 他们使舌头尖利如蛇, 嘴里有虺蛇的毒气。 (细拉)
Iwo amanola malilime awo kukhala akuthwa ngati a njoka; pa milomo yawo pali ululu wa mamba. (Sela)
4 耶和华啊,求你拯救我脱离恶人的手, 保护我脱离强暴的人! 他们图谋推我跌倒。
Tetezeni Inu Yehova, kwa anthu oyipa; tchinjirizeni kwa anthu ankhanza amene amakonza zokola mapazi anga.
5 骄傲人为我暗设网罗和绳索; 他们在路旁铺下网,设下圈套。 (细拉)
Anthu odzikuza anditchera msampha mobisika; iwo atchera zingwe za maukonde awo ndipo anditchera misampha pa njira yanga. (Sela)
6 我曾对耶和华说:你是我的 神。 耶和华啊,求你留心听我恳求的声音!
Inu Yehova, ine ndikuti, “Ndinu Mulungu wanga.” Imvani kupempha kwanga Yehova.
7 主—耶和华、我救恩的力量啊, 在争战的日子,你遮蔽了我的头。
Inu Ambuye Wamphamvuzonse, Mpulumutsi wanga wamphamvu, mumateteza mutu wanga tsiku lankhondo.
8 耶和华啊,求你不要遂恶人的心愿; 不要成就他们的计谋,恐怕他们自高。 (细拉)
Musawapatse anthu oyipa zokhumba zawo, Inu Yehova; musalole kuti zokonza zawo zitheke, mwina iwo adzayamba kunyada. (Sela)
9 至于那些昂首围困我的人, 愿他们嘴唇的奸恶陷害自己!
Mitu ya amene andizungulira iphimbidwe ndi masautso amene milomo yawo yayambitsa.
10 愿火炭落在他们身上! 愿他们被丢在火中, 抛在深坑里,不能再起来。
Makala amoto agwere pa iwo; aponyedwe pa moto, mʼmaenje amatope, asatulukemonso.
11 说恶言的人在地上必坚立不住; 祸患必猎取强暴的人,将他打倒。
Musalole kuti anthu achipongwe akhazikike mʼdziko; choyipa chilondole anthu ankhanza.
12 我知道耶和华必为困苦人伸冤, 必为穷乏人辨屈。
Ndikudziwa kuti Yehova amapereka chiweruzo cholungama kwa anthu osauka, ndipo amateteza zolinga za anthu osowa.
13 义人必要称赞你的名; 正直人必住在你面前。
Zoonadi anthu olungama adzatamanda dzina lanu, ndipo anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.

< 诗篇 140 >