< Zefaniya 3 >

1 Tsoka kwa mzinda wa anthu opondereza, owukira ndi odetsedwa!
הוי מראה ונגאלה--העיר היונה
2 Sumvera aliyense, sulandira chidzudzulo. Sumadalira Yehova, suyandikira pafupi ndi Mulungu wake.
לא שמעה בקול לא לקחה מוסר ביהוה לא בטחה אל אלהיה לא קרבה
3 Akuluakulu ake ali ngati mikango yobuma, olamulira ake ndi olusa ngati mimbulu ya nthawi ya madzulo, zimene pofika mmawa sizisiya chilichonse.
שריה בקרבה אריות שאגים שפטיה זאבי ערב לא גרמו לבקר
4 Aneneri ake ndi odzikuza; anthu achinyengo. Ansembe ake amadetsa malo opatulika ndipo amaphwanya lamulo.
נביאיה פחזים אנשי בגדות כהניה חללו קדש חמסו תורה
5 Yehova amene ali pakati pawo ndi wolungama; Iye salakwa. Tsiku ndi tsiku amaweruza molungama, ndipo tsiku lililonse salephera, komabe ochita zoyipa sachita manyazi nʼkomwe.
יהוה צדיק בקרבה לא יעשה עולה בבקר בבקר משפטו יתן לאור לא נעדר ולא יודע עול בשת
6 “Ndachotseratu mitundu ya anthu; ndagwetsa malinga awo. Ndipo sindinasiye ndi mmodzi yemwe mʼmisewu mwawo, popanda aliyense wodutsa. Mizinda yawo yawonongedwa; palibe aliyense adzatsalemo.
הכרתי גוים נשמו פנותם--החרבתי חוצותם מבלי עובר נצדו עריהם מבלי איש מאין יושב
7 Ndinati, ‘Ndithudi, anthu a mu mzindawu adzandiopa ndi kumvera kudzudzula kwanga!’ Ndipo sindidzawononga nyumba zawo, kapena kuwalanganso. Koma iwo anali okonzeka kuchita mwachinyengo zinthu zonse zimene amachita.
אמרתי אך תיראי אותי תקחי מוסר ולא יכרת מעונה כל אשר פקדתי עליה אכן השכימו השחיתו כל עלילותם
8 Choncho mundidikire,” akutero Yehova, “chifukwa cha tsiku limene ndidzaperekera umboni. Ndatsimikiza kusonkhanitsa pamodzi mitundu ya anthu, kusonkhanitsa maufumu ndi kutsanulira ukali wanga pa iwo; mkwiyo wanga wonse woopsa. Dziko lonse lidzatenthedwa ndi moto wa mkwiyo wa nsanje yanga.
לכן חכו לי נאם יהוה ליום קומי לעד כי משפטי לאסף גוים לקבצי ממלכות לשפך עליהם זעמי כל חרון אפי--כי באש קנאתי תאכל כל הארץ
9 “Pamenepo ndidzayeretsa milomo ya anthu a mitundu yonse kuti anthu onsewo ayitane dzina la Yehova ndi kumutumikira Iye pamodzi.
כי אז אהפך אל עמים שפה ברורה לקרא כלם בשם יהוה לעבדו שכם אחד
10 Kuchokera kutsidya kwa mitsinje ya ku Kusi anthu anga ondipembedza, omwazikana, adzandibweretsera zopereka.
מעבר לנהרי כוש--עתרי בת פוצי יובלון מנחתי
11 Tsiku limenelo simudzachita manyazi chifukwa cha zoyipa zonse munandichitira, popeza ndidzachotsa onse mu mzinda uwu amene amakondwera chifukwa cha kunyada kwawo. Simudzakhalanso odzikuza mʼphiri langa lopatulika.
ביום ההוא לא תבושי מכל עלילתיך אשר פשעת בי כי אז אסיר מקרבך עליזי גאותך ולא תוספי לגבהה עוד בהר קדשי
12 Koma ndidzasiya pakati panu anthu ofatsa ndi odzichepetsa, amene amadalira dzina la Yehova.
והשארתי בקרבך עם עני ודל וחסו בשם יהוה
13 Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika; sadzayankhulanso zonama, ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo. Adzadya ndi kugona ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”
שארית ישראל לא יעשו עולה ולא ידברו כזב ולא ימצא בפיהם לשון תרמית כי המה ירעו ורבצו ואין מחריד
14 Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni; fuwula mokweza, iwe Israeli! Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu!
רני בת ציון--הריעו ישראל שמחי ועלזי בכל לב בת ירושלם
15 Yehova wachotsa chilango chako, wabweza mdani wako. Yehova, Mfumu ya Israeli, ali pakati pako; sudzaopanso chilichonse.
הסיר יהוה משפטיך פנה איבך מלך ישראל יהוה בקרבך לא תיראי רע עוד
16 Pa tsiku limenelo adzanena kwa Yerusalemu kuti, “Usaope, iwe Ziyoni; usafowoke.
ביום ההוא יאמר לירושלם אל תיראי ציון אל ירפו ידיך
17 Yehova Mulungu wako ali pakati pako, ali ndi mphamvu yopulumutsa. Adzakondwera kwambiri mwa iwe, adzakukhalitsa chete ndi chikondi chake, adzayimba mokondwera chifukwa cha iwe.”
יהוה אלהיך בקרבך גבור יושיע ישיש עליך בשמחה יחריש באהבתו--יגיל עליך ברנה
18 “Ndidzakuchotserani zowawa za pa zikondwerero zoyikika; nʼzolemetsa ndi zochititsa manyazi.
נוגי ממועד אספתי ממך היו--משאת עליה חרפה
19 Taonani, nthawi imeneyo ndidzathana ndi onse amene anakuponderezani; ndidzapulumutsa olumala ndi kusonkhanitsa amene anamwazika. Ndidzawayamikira ndi kuwachitira ulemu mʼdziko lililonse mmene anachititsidwa manyazi.
הנני עשה את כל מעניך בעת ההיא והושעתי את הצלעה והנדחה אקבץ ושמתים לתהלה ולשם בכל הארץ בשתם
20 Pa nthawi imeneyo ndidzakusonkhanitsani; pa nthawi imeneyo ndidzakubweretsani ku mudzi kwanu. Ndidzakuyamikirani ndi kukuchitirani ulemu pakati pa mitundu ya anthu a dziko lapansi pamene ndidzabwezeretsa mtendere wanu inu mukuona,” akutero Yehova.
בעת ההיא אביא אתכם ובעת קבצי אתכם כי אתן אתכם לשם ולתהלה בכל עמי הארץ בשובי את שבותיכם לעיניכם אמר יהוה

< Zefaniya 3 >