< Zekariya 10 >

1 Pemphani mvula kwa Yehova pa nthawi yamphukira; ndi Yehova amene amapanga mitambo ya mvula. Iye amagwetsa mivumbi ya mvula kwa anthu, ndi kumeretsa mbewu za mʼmunda kwa aliyense.
שַׁאֲל֨וּ מֵיְהוָ֤ה מָטָר֙ בְּעֵ֣ת מַלְקֹ֔ושׁ יְהוָ֖ה עֹשֶׂ֣ה חֲזִיזִ֑ים וּמְטַר־גֶּ֙שֶׁם֙ יִתֵּ֣ן לָהֶ֔ם לְאִ֖ישׁ עֵ֥שֶׂב בַּשָּׂדֶֽה׃
2 Mafano amayankhula zachinyengo, owombeza mawula amaona masomphenya abodza; amafotokoza maloto onama, amapereka chitonthozo chopandapake. Choncho anthu amangoyendayenda ngati nkhosa zozunzika chifukwa chosowa mʼbusa.
כִּ֧י הַתְּרָפִ֣ים דִּבְּרוּ־אָ֗וֶן וְהַקֹּֽוסְמִים֙ חָ֣זוּ שֶׁ֔קֶר וַֽחֲלֹמֹות֙ הַשָּׁ֣וא יְדַבֵּ֔רוּ הֶ֖בֶל יְנַֽחֵמ֑וּן עַל־כֵּן֙ נָסְע֣וּ כְמֹו־צֹ֔אן יַעֲנ֖וּ כִּֽי־אֵ֥ין רֹעֶֽה׃ פ
3 “Ine ndawakwiyira kwambiri abusa, ndipo ndidzalanga atsogoleri; pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzasamalira nkhosa zake, nyumba ya Yuda, ndi kuwasandutsa ngati akavalo aulemerero ankhondo.
עַל־הָֽרֹעִים֙ חָרָ֣ה אַפִּ֔י וְעַל־הָעַתּוּדִ֖ים אֶפְקֹ֑וד כִּֽי־פָקַד֩ יְהוָ֨ה צְבָאֹ֤ות אֶת־עֶדְרֹו֙ אֶת־בֵּ֣ית יְהוּדָ֔ה וְשָׂ֣ם אֹותָ֔ם כְּס֥וּס הֹודֹ֖ו בַּמִּלְחָמָֽה׃
4 Mu Yuda mudzachokera mwala wapangodya, mudzachokera chikhomo cha tenti, mudzachokera uta wankhondo, mudzachokera mtsogoleri aliyense.
מִמֶּ֤נּוּ פִנָּה֙ מִמֶּ֣נּוּ יָתֵ֔ד מִמֶּ֖נּוּ קֶ֣שֶׁת מִלְחָמָ֑ה מִמֶּ֛נּוּ יֵצֵ֥א כָל־נֹוגֵ֖שׂ יַחְדָּֽו׃
5 Onse pamodzi adzakhala ngati ngwazi zankhondo zoponda mʼmatope a mʼmisewu nthawi yankhondo. Chifukwa Yehova adzakhala nawo, adzachita nkhondo ndi kugonjetsa okwera pa akavalo.
וְהָי֨וּ כְגִבֹּרִ֜ים בֹּוסִ֨ים בְּטִ֤יט חוּצֹות֙ בַּמִּלְחָמָ֔ה וְנִ֨לְחֲמ֔וּ כִּ֥י יְהוָ֖ה עִמָּ֑ם וְהֹבִ֖ישׁוּ רֹכְבֵ֥י סוּסִֽים׃
6 “Ndidzalimbitsa nyumba ya Yuda ndi kupulumutsa nyumba ya Yosefe. Ndidzawabwezeretsa chifukwa ndawamvera chisoni. Adzakhala ngati kuti sindinawakane, chifukwa ndine Yehova Mulungu wawo ndipo ndidzawayankha.
וְגִבַּרְתִּ֣י ׀ אֶת־בֵּ֣ית יְהוּדָ֗ה וְאֶת־בֵּ֤ית יֹוסֵף֙ אֹושִׁ֔יעַ וְהֹֽושְׁבֹותִים֙ כִּ֣י רִֽחַמְתִּ֔ים וְהָי֖וּ כַּאֲשֶׁ֣ר לֹֽא־זְנַחְתִּ֑ים כִּ֗י אֲנִ֛י יְהוָ֥ה אֱלֹהֵיהֶ֖ם וְאֶעֱנֵֽם׃
7 Aefereimu adzakhala ngati ankhondo amphamvu adzasangalala ngati anthu amene amwa vinyo. Ana awo adzaziona zimenezi ndipo adzasangalala; mʼmitima mwawo adzakondwa mwa Ambuye.
וְהָי֤וּ כְגִבֹּור֙ אֶפְרַ֔יִם וְשָׂמַ֥ח לִבָּ֖ם כְּמֹו־יָ֑יִן וּבְנֵיהֶם֙ יִרְא֣וּ וְשָׂמֵ֔חוּ יָגֵ֥ל לִבָּ֖ם בַּיהוָֽה׃
8 Ndidzaliza mluzu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi. Ndithu ndawawombola; adzachulukana ngati poyamba paja.
אֶשְׁרְקָ֥ה לָהֶ֛ם וַאֲקַבְּצֵ֖ם כִּ֣י פְדִיתִ֑ים וְרָב֖וּ כְּמֹ֥ו רָבֽוּ׃
9 Ndinawamwaza pakati pa mitundu ina ya anthu, koma ku mayiko akutaliwo adzandikumbukira. Iwo pamodzi ndi ana awo adzapulumuka, ndipo adzabwerera.
וְאֶזְרָעֵם֙ בָּֽעַמִּ֔ים וּבַמֶּרְחַקִּ֖ים יִזְכְּר֑וּנִי וְחָי֥וּ אֶת־בְּנֵיהֶ֖ם וָשָֽׁבוּ׃
10 Ndidzawabweretsa kuchokera ku Igupto ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku Asiriya. Ndidzawabwezera ku Giliyadi ndi ku Lebanoni, mpaka malo woti nʼkukhalamo adzatheratu.
וַהֲשִֽׁיבֹותִים֙ מֵאֶ֣רֶץ מִצְרַ֔יִם וּמֵֽאַשּׁ֖וּר אֲקַבְּצֵ֑ם וְאֶל־אֶ֨רֶץ גִּלְעָ֤ד וּלְבָנֹון֙ אֲבִיאֵ֔ם וְלֹ֥א יִמָּצֵ֖א לָהֶֽם׃
11 Adzawoloka nyanja ya masautso; nyanja yokokoma idzagonja ndipo madzi onse a mu Nailo adzaphwa. Kudzikuza kwa Asiriya kudzatha ndipo ndodo yaufumu ya Igupto idzathyoka.
וְעָבַ֨ר בַּיָּ֜ם צָרָ֗ה וְהִכָּ֤ה בַיָּם֙ גַּלִּ֔ים וְהֹבִ֕ישׁוּ כֹּ֖ל מְצוּלֹ֣ות יְאֹ֑ר וְהוּרַד֙ גְּאֹ֣ון אַשּׁ֔וּר וְשֵׁ֥בֶט מִצְרַ֖יִם יָסֽוּר׃
12 Ndidzalimbitsa iwo mwa Yehova ndipo adzayenda mʼdzina lake,” akutero Yehova.
וְגִבַּרְתִּים֙ בַּֽיהוָ֔ה וּבִשְׁמֹ֖ו יִתְהַלָּ֑כוּ נְאֻ֖ם יְהוָֽה׃ ס

< Zekariya 10 >