< Nyimbo ya Solomoni 8 >

1 Ukanakhala kuti ndiwe mlongo wanga, amene anayamwa mawere a amayi anga! Ndikanakumana nawe pa njira, ndikanakupsompsona, ndipo palibe wina aliyense akanandinyoza. 2 Ndikanakutenga ndi kukulowetsa mʼnyumba ya amayi anga, amayi amene anandiphunzitsa, ndikanakupatsa vinyo wotsekemera kuti umwe, zotsekemera za makangadza. 3 Mutu wanga watsamira dzanja lake lamanzere ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira. 4 Inu akazi a ku Yerusalemu, ndithu ndikukupemphani: musachigwedeze chikondi kapena kuchiutsa mpaka pamene chifunire ichocho. 5 Kodi ndani uyo akutuluka ku chipululuyo, atatsamira wokondedwa wakeyo? Mkazi Ndinakudzutsa pa tsinde pa mtengo wa apulosi, pamenepo ndi pamene amayi anachirira, pamenepo ndi pamene wokubereka anamva ululu pokubala iweyo. 6 Undiyike pamtima pako ngati chidindo, ngati chidindo cha pa dzanja lako; pakuti chikondi nʼchamphamvu ngati imfa, nsanje ndiyaliwuma ngati manda. Chikondi chimachita kuti lawilawi ngati malawi a moto wamphamvu. (Sheol h7585) 7 Madzi ochuluka sangachizimitse chikondi, mitsinje singachikokolole chikondicho. Ngati wina apereka chuma chonse cha mʼnyumba mwake chifukwa cha chikondi, adzangonyozeka nazo kotheratu. 8 Ife tili naye mlongo wathu wamngʼono, koma alibe mawere, kodi tidzamuchitira chiyani mlongo wathuyu pa tsiku limene adzamufunsire? 9 Ngati iye ndi khoma, tidzamumangira nsanja ya siliva. Ngati iye ndi chitseko, tidzamutchinga ndi matabwa a mkungudza. 10 Ine ndili ngati khoma, ndipo mawere anga ndi nsanja zake. Tsono mʼmaso mwa bwenzi langa ndine wobweretsa mtendere. 11 Solomoni anali ndi munda wampesa ku Baala-Hamoni; iyeyo anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi, aliyense mwa iwo ankayenera kupereka ndalama zasiliva 1,000 mʼmalo mwa zipatso zake. 12 Koma munda wanga wampesa ndi wangawanga ndiponso wa ine ndekha. Iwe Solomoni, khala nazo ndalama zasiliva 1,000 ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za amene akusamalira mundawo. 13 Iwe amene umakhala mʼminda uli pamodzi ndi anzako, ndilole kuti ndimve liwu lako! 14 Fulumira wokondedwa wanga, ndipo ukhale ngati gwape kapena mwana wa mbawala wothamanga mʼmapiri mʼmene mumamera mbewu zokometsera chakudya.

< Nyimbo ya Solomoni 8 >