< Masalimo 98 >

1 Salimo. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso. 2 Yehova waonetsa chipulumutso chake ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina. 3 Iye wakumbukira chikondi chake ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli; malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu. 4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera. 5 Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze, ndi zeze ndi mawu a kuyimba, 6 ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu. 7 Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo. 8 Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo, mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe; 9 izo ziyimbe pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, ndi mitundu ya anthu mosakondera.

< Masalimo 98 >