< Masalimo 96 >

1 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano; Imbirani Yehova dziko lonse lapansi. 2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake; lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. 3 Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko, ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu. 4 Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse. 5 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano, koma Yehova analenga mayiko akumwamba. 6 Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake, mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika. 7 Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu. 8 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake; bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake. 9 Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake; njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi. 10 Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.” Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe; Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama. 11 Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere; nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo; 12 minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo. Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe; 13 idzayimba pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi; adzaweruza dziko lonse mwachilungamo ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.

< Masalimo 96 >