< Masalimo 87 >

1 Salimo la Ana a Kora. Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera; 2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni kupambana malo onse okhalamo a Yakobo. 3 Za ulemerero wako zimakambidwa, Iwe mzinda wa Mulungu: (Sela) 4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni pakati pa iwo amene amandidziwa. Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi, ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’” 5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti, “Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye, ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.” 6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina: “Uyu anabadwira mʼZiyoni.” (Sela) 7 Oyimba ndi ovina omwe adzati, “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”

< Masalimo 87 >