< Masalimo 84 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora. Malo anu okhalamo ndi okomadi, Inu Yehova Wamphamvuzonse! 2 Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufuna mabwalo a Yehova; Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira Mulungu wamoyo. 3 Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga. 4 Odala amene amakhala mʼNyumba yanu; nthawi zonse amakutamandani. (Sela) 5 Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu, mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni. 6 Pamene akudutsa chigwa cha Baka, amachisandutsa malo a akasupe; mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake. 7 Iwo amanka nakulirakulira mphamvu mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni. 8 Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse; mvereni Inu Mulungu wa Yakobo. (Sela) 9 Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu; yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu. 10 Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa. 11 Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro. 12 Inu Yehova Wamphamvuzonse, wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu.

< Masalimo 84 >