< Masalimo 75 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa. 2 Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo. 3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. (Sela) 4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu. 5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’” 6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu. 7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina. 8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse. 9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo. 10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.

< Masalimo 75 >