< Masalimo 69 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.” Pulumutseni Inu Mulungu, pakuti madzi afika mʼkhosi
Au maître de chant. Sur les lys. De David. Sauve-moi, ô Dieu, car les eaux montent jusqu'à mon âme.
2 Ine ndikumira mʼthope lozama mʼmene mulibe popondapo. Ndalowa mʼmadzi ozama; mafunde andimiza.
Je suis enfoncé dans une fange profonde, et il n'y a pas où poser le pied. Je suis tombé dans un gouffre d'eau, et les flots me submergent.
3 Ndafowoka ndikupempha chithandizo; kummero kwanga kwawuma gwaa, mʼmaso mwanga mwada kuyembekezera Mulungu wanga.
Je m'épuise à crier; mon gosier est en feu; mes yeux se consument dans l'attente de mon Dieu.
4 Iwo amene amadana nane popanda chifukwa ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga; ambiri ndi adani anga popanda chifukwa, iwo amene akufunafuna kundiwononga. Ndikukakamizidwa kubwezera zomwe sindinabe.
Ils sont plus nombreux que les cheveux de ma tête, ceux qui me haïssent sans cause; ils sont puissants ceux qui veulent me perdre, qui sont sans raison mes ennemis. Ce que je n'ai pas dérobé, il faut que je le rende.
5 Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu, kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.
O Dieu, tu connais ma folie, et mes fautes ne te sont pas cachées.
6 Iwo amene amadalira Inu asanyozedwe chifukwa cha ine, Inu Ambuye Wamphamvuzonse. Iwo amene amafunafuna Inu asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine, Inu Mulungu wa Israeli.
Que ceux qui espèrent en toi n'aient pas à rougir à cause de moi, Seigneur, Yahweh des armées! Que ceux qui te cherchent ne soient pas confondus à mon sujet, Dieu d'Israël!
7 Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu, ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.
Car c'est pour toi que je porte l'opprobre, que la honte couvre mon visage.
8 Ndine mlendo kwa abale anga, munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;
Je suis devenu un étranger pour mes frères, un inconnu pour les fils de ma mère.
9 pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.
Car le zèle de ta maison me dévore, et les outrages de ceux qui t'insultent retombent sur moi.
10 Pamene ndikulira ndi kusala kudya, ndiyenera kupirira kunyozedwa;
Je verse des larmes et je jeûne: on m'en fait un sujet d'opprobre.
11 pomwe ndavala chiguduli, anthu amandiseweretsa.
Je prends un sac pour vêtement, et je suis l'objet de leurs sarcasmes.
12 Iwo amene amakhala pa chipata amandinena, ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.
Ceux qui sont assis à la porte parlent de moi, et les buveurs de liqueurs fortes font sur moi des chansons.
13 Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye, pa nthawi yanu yondikomera mtima; mwa chikondi chanu chachikulu Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.
Et moi, je t'adresse ma prière, Yahweh; dans le temps favorable, ô Dieu, selon ta grande bonté, exauce-moi, selon la vérité de ton salut.
14 Mundilanditse kuchoka mʼmatope, musalole kuti ndimire, pulumutseni ine kwa iwo amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.
Retire-moi de la boue, et que je n'y reste plus enfoncé; que je sois délivré de mes ennemis et des eaux profondes!
15 Musalole kuti chigumula chindimeze, kuya kusandimeze ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.
Que les flots ne me submergent plus, que l'abîme ne m'engloutisse pas, que la fosse ne se ferme pas sur moi!
16 Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu; mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.
Exauce-moi, Yahweh, car ta bonté est compatissante; dans ta grande miséricorde tourne-toi vers moi,
17 Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu, ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.
Et ne cache pas ta face à ton serviteur; je suis dans l'angoisse, hâte-toi de m'exaucer.
18 Bwerani pafupi ndi kundilanditsa; ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.
Approche-toi de mon âme, délivre-la; sauve-moi à cause de mes ennemis.
19 Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera, kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.
Tu connais mon opprobre, ma honte, mon ignominie; tous mes persécuteurs sont devant toi.
20 Mnyozo waswa mtima wanga ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse; ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.
L'opprobre a brisé mon cœur et je suis malade; j'attends de la pitié, mais en vain; des consolateurs, et je n'en trouve aucun.
21 Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.
Pour nourriture ils me donnent l'herbe amère; dans ma soif, ils m'abreuvent de vinaigre.
22 Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha; chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.
Que leur table soit pour eux un piège, un filet au sein de leur sécurité!
23 Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.
Que leurs yeux s'obscurcissent pour ne plus voir; fais chanceler leurs reins pour toujours.
24 Khuthulirani ukali wanu pa iwo; mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.
Déverse sur eux ta colère, et que le feu de ton courroux les atteigne!
25 Malo awo akhale wopanda anthu pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.
Que leur demeure soit dévastée, qu'il n'y ait plus d'habitants dans leurs tentes!
26 Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.
Car ils persécutent celui que tu frappes, ils racontent les souffrances de celui que tu blesses.
27 Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo, musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.
Ajoute l'iniquité à leur iniquité, et qu'ils n'aient point part à ta justice.
28 Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.
Qu'ils soient effacés du livre de vie et qu'ils ne soient point inscrits avec les justes.
29 Ndikumva zowawa ndi kuzunzika; lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.
Moi, je suis malheureux et souffrant; que ton secours, ô Dieu, me relève!
30 Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo, ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.
Je célébrerai le nom de Dieu par des cantiques, je l'exalterai par des actions de grâces;
31 Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe, kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.
Et Yahweh les aura pour plus agréables qu'un taureau, qu'un jeune taureau avec cornes et sabots.
32 Wosauka adzaona ndipo adzasangalala, Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!
Les malheureux, en le voyant, se réjouiront, et vous qui cherchez Dieu, votre cœur revivra.
33 Yehova amamvera anthu osowa ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.
Car Yahweh écoute les pauvres, et il ne méprise point ses captifs.
34 Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye, nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,
Que les cieux et la terre le célèbrent, les mers et tout ce qui s'y meut!
35 pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni ndi kumanganso mizinda ya Yuda, anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;
Car Dieu sauvera Sion et bâtira les villes de Juda, on s'y établira et l'on en prendra possession;
36 ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo, ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.
La race de ses serviteurs l'aura en héritage, et ceux qui aiment son nom y auront leur demeure.

< Masalimo 69 >