< Masalimo 67 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire. 2 Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse. 3 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. 4 Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi. 5 Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. 6 Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu. 7 Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo.

< Masalimo 67 >