< Masalimo 64 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga; tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani. 2 Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa, ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa. 3 Iwo amanola malilime awo ngati malupanga, amaponya mawu awo olasa ngati mivi. 4 Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa; amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha. 5 Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa, amayankhula zobisa misampha yawo; ndipo amati, “Adzayiona ndani?” 6 Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati, “Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!” Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo. 7 Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi; mwadzidzidzi adzakanthidwa. 8 Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa ndi kuwasandutsa bwinja; onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza. 9 Anthu onse adzachita mantha; adzalengeza ntchito za Mulungu ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita. 10 Lolani wolungama akondwere mwa Yehova ndi kubisala mwa Iye, owongoka mtima onse atamande Iye!

< Masalimo 64 >