< Masalimo 63 >

1 Salimo la Davide. Pamene anali mʼchipululu cha Yuda. Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi. 2 Inu ndinakuonani ku malo anu opatulika ndipo ndinapenya mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. 3 Chifukwa chikondi chanu ndi choposa moyo, milomo yanga idzakulemekezani. 4 Ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga, ndipo mʼdzina lanu ndidzakweza manja anga. 5 Mudzakhutitsa moyo wanga ndi zonona. Ine ndidzakutamandani ndi mawu anthetemya. 6 Pa bedi panga ndimakumbukira inu; ndimaganiza za Inu nthawi yonse ya usiku. 7 Chifukwa ndinu thandizo langa, ine ndimayimba mu mthunzi wa mapiko anu. 8 Moyo wanga umakangamira Inu; dzanja lanu lamanja limandigwiriziza. 9 Iwo amene akufunafuna moyo wanga adzawonongedwa; adzatsikira kunsi kozama kwa dziko lapansi. 10 Iwo adzaperekedwa ku lupanga ndi kukhala chakudya cha ankhandwe. 11 Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu; onse amene amalumbira mʼdzina la Mulungu adzalemekeza Mulunguyo, koma pakamwa pa anthu onama padzatsekedwa.

< Masalimo 63 >