< Masalimo 53 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Mahalati. Ndakatulo ya Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Iwo ndi oyipa ndipo njira zawo ndi zonyansa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino. 2 Mulungu kumwamba amayangʼana pansi pano pa ana a anthu kuti aone ngati alipo wina wanzeru, wofunafuna Mulungu. 3 Aliyense wabwerera, iwo onse pamodzi akhala oyipa; palibe ndi mmodzi yemwe amene amachita chabwino, ngakhale mmodzi. 4 Kodi anthu ochita zoyipawa adzaphunziradi; anthu amene amadya anthu anga monga mmene anthu amadyera buledi, ndipo sapemphera kwa Mulungu? 5 Iwo anali pamenepo atathedwa nzeru ndi mantha aakulu pamene panalibe kanthu kochititsa mantha. Mulungu anamwazamwaza mafupa a anthu amene anakuthirani nkhondo; inuyo munawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawanyoza. 6 Ndithu, chipulumutso cha Israeli nʼchochokera ku Ziyoni! Pamene Mulungu adzabwezeretsanso ulemerero wa anthu ake, lolani Yakobo akondwere ndi Israeli asangalale!

< Masalimo 53 >