< Masalimo 43 >

1 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu; ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza; mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa. 2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga. Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine? Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira, woponderezedwa ndi mdani? 3 Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu kuti zinditsogolere; mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera, kumalo kumene inu mumakhala. 4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa. Ndidzakutamandani ndi zeze, Inu Mulungu wanga. 5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga? Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandabe Iye, Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.

< Masalimo 43 >