< Masalimo 4 >

1 Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe wa zida za zingwe. Salimo la Davide. Ndiyankheni pamene ndiyitana Inu, Inu Mulungu wa chilungamo changa. Pumulitseni ku zowawa zanga; chitireni chifundo ndi kumva pemphero langa. 2 Anthu inu, mpaka liti mudzakhala mukusandutsa ulemerero wanga kukhala manyazi? Mpaka liti mudzakonda zachabe ndi kufuna milungu yabodza? (Sela) 3 Dziwani kuti Yehova wadziyikira padera anthu okhulupirika; Yehova adzamva pamene ndidzamuyitana. 4 Kwiyani koma musachimwe; pamene muli pa mabedi anu, santhulani mitima yanu ndi kukhala chete. (Sela) 5 Perekani nsembe zolungama ndipo dalirani Yehova. 6 Ambiri akufunsa kuti, “Ndani angationetse chabwino chilichonse?” Kuwunika kwa nkhope yanu kutiwalire, Inu Yehova. 7 Inu mwadzaza mtima wanga ndi chimwemwe chachikulu kuposa kuchuluka kwa tirigu wawo ndi vinyo watsopano. 8 Ine ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha, Inu Yehova, mumandisamalira bwino.

< Masalimo 4 >