< Masalimo 30 >

1 Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu. Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine. 2 Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo ndipo Inu munandichiritsa. 3 Inu Yehova, munanditulutsa ku manda, munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje. (Sheol h7585) 4 Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika; tamandani dzina lake loyera. 5 Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa. 6 Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati, “Sindidzagwedezekanso.” 7 Inu Yehova, pamene munandikomera mtima, munachititsa phiri langa kuyima chilili; koma pamene munabisa nkhope yanu, ndinataya mtima. 8 Kwa Inu Yehova ndinayitana; kwa Ambuye ndinapempha chifundo; 9 “Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu? 10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo; Yehova mukhale thandizo langa.” 11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina; munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe, 12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete. Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

< Masalimo 30 >