< Masalimo 23 >

1 Salimo la Davide. Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu. 2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira, amanditsogolera ku madzi akumwa abwino, 3 amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera mʼnjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake. 4 Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza. 5 Mumandikonzera chakudya adani anga akuona. Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chimasefukira. 6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehova kwamuyaya.

< Masalimo 23 >