< Masalimo 150 >

1 Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika; mutamandeni ku thambo lake lamphamvu. 2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu; mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. 3 Mutamandeni poyimba malipenga, mutamandeni ndi pangwe ndi zeze. 4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina, mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro. 5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga, mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri. 6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.

< Masalimo 150 >