< Masalimo 15 >

1 Salimo la Davide. Yehova, ndani angathe kukhala mʼmalo anu opatulika? Kodi ndani angathe kukhala mʼphiri lanu loyera? 2 Munthu wa makhalidwe abwino, amene amachita zolungama, woyankhula choonadi chochokera mu mtima mwake, 3 ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake, 4 amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka, 5 amene amakongoletsa ndalama zake popanda chiwongoladzanja ndipo salandira chiphuphu pofuna kutsutsa anthu osalakwa. Iye amene amachita zinthu zimenezi sadzagwedezeka konse.

< Masalimo 15 >